Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nanga Mungaphunzile Bwanji za Mulungu?

Nanga Mungaphunzile Bwanji za Mulungu?

Phunzilo 4

Nanga Mungaphunzile Bwanji za Mulungu?

Mungaphunzile za Mulungu mwa kuŵelenga Baibo. Kale kwambili, Mulungu anasankha anthu ena kuti alembe maganizo ake. Zimene analemba zimapanga buku lochedwa kuti Baibo. Masiku ano timaphunzila za Mulungu mwa kuŵelenga Baibo. Baibo imachedwanso kuti Mau a Mulungu cifukwa muli mau a Yehova, kapena kuti uthenga wake. Tingakhulupilile zimene Baibo imakamba cifukwa Yehova sanganame. “Mulungu sakhoza kunama.” (Ahebri 6:18) Mau a Mulungu ndiye coonadi.—Yohane 17:17.

Mulungu anatipatsa mphatso zamtengo wapatali. Koma Baibo imaposa zonse. Baibo ili monga kalata imene tate walembela ana ake okondedwa. Imatiuza kuti Mulungu analonjeza kuti adzasintha dziko lapansi kukhala paladaiso, malo abwino okhalamo. Imatiuzanso zimene Mulungu anacitila ana ake okhulupilika kumbuyo, zimene amawacitila masiku ano, ndiponso zimene adzawacitila mtsogolo. Imatithandizanso mmene tingacitile na mavuto athu na mmene tingapezele cimwemwe.—2 Timoteo 3:16, 17.

A Mboni za Yehova ni anzake a Mulungu. Iwo adzakuthandizani kuimvetsetsa Baibo. Ngati mufuna kuphunzila Baibo, auzeni adzakuthandizani. Samalipilitsa ndalama. (Mateyu 10:8) Ndiponso, mungaziyenda kumisonkhano yawo. Amacitila misonkhano imeneyi ku malo oitanidwa kuti Nyumba ya Ufumu. Mukayamba kuyendako ku misonkhano imeneyi, mudzaphunzila zambili ponena za Mulungu, panthawi ing’ono cabe.

Mungaphunzilenso za Mulungu ku zinthu zimene anapanga. Mwacitsanzo, Baibo imakamba kuti: “Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.” (Genesis 1:1) Pamene Yehova analenga “kumwamba,” anapanganso dzuŵa. Nanga zimenezi zimatiphunzitsa ciyani ponena za Mulungu? Zimatiphunzitsa kuti Yehova ali na mphamvu zambili. Ni yekha cabe angakwanitse kupanga cinthu camphamvu monga dzuŵa. Zimatiphunzitsanso kuti Yehova ali na nzelu. Takamba conco cifukwa sembe analibe nzelu, sakanakwanitsa kupanga dzuŵa limene limatulutsa kutentha na kuwala, koma silikutha kapena kuzima.

Zimene Mulungu analenga zimaonetsa kuti amatikonda. Ganizilani zipatso zosiyanasiyana zimene zili padziko lapansi. Yehova akanafuna, sembe anatipatsa mtundu umodzi cabe wa zipatso, kapena osatipatsa cipatso ciliconse. Koma, anatipatsa zipatso zambili zosiyanasiyana mu maonekedwe, ukulu, na kukoma kwake. Zimenezi zimaonetsa kuti Yehova ni Mulungu wacikondi, wopatsa, woganizila ena komanso wabwino mtima.—Salmo 104:24.