Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Onetsani Cikondi Canu kwa Mulungu

Onetsani Cikondi Canu kwa Mulungu

Phunzilo 16

Onetsani Cikondi Canu kwa Mulungu

Kuti ubwenzi wanu na munthu wina upitilize, mufunikila kumakambitsana. Mumamumvela, nayenso amakumvelani. Ndiponso, mumauzako anthu ena zinthu zabwino ponena za iye. Ni cimodzimodzi na kukhala mnzake wa Mulungu. Onani zimene Baibo imakamba pankhani imeneyi:

Muzikamba na Yehova m’pemphelo nthawi zonse. “Limbikani cilimbikile m’kupemphela.”—Aroma 12:12.

Muziŵelenga Mau a Mulungu, Baibo. “Lemba lililonse adaliuzila Mulungu, ndipo lipindulitsa pa ciphunzitso, citsutsano, cikonzelo, cilangizo ca m’cilungamo.”—2 Timoteo 3:16.

Muziphunzitsa ena za Mulungu. “Cifukwa cake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, . . . asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulilani inu.”—Mateyu 28:19, 20.

Khalani mnzawo wa aja amene ni anzake a Mulungu. “Ukayenda ndi anzelu udzakhala wanzelu.”—Miyambo 13:20.

Muzipezeka kumisonkhano ku Nyumba ya Ufumu. ‘Tiyeni tiganizilane wina ndi mnzake, kuti tilimbikitsane pa cikondi ndi nchito zabwino.’—Ahebri 10:24, NW.

Muzithandiza panchito ya Ufumu na zopeleka zanu. ‘Yense acite monga atsimikiza mtima, si mwa cisoni kapena mokakamiza, pakuti Mulungu akonda opeleka mokondwelela.’—2 Akorinto 9:7.