Kodi Niyenela Kubatizika?
MUTU 37
Kodi Niyenela Kubatizika?
Pa mfundo zotsatilazi, congani kuti zoona kapena zonama:
Ubatizo ni wofunika kwa Mkhristu aliyense.
□ Zoona
□ Zonama
Colinga cacikulu ca ubatizo ndico kukutetezani kuti musacite chimo.
□ Zoona
□ Zonama
Ubatizo umakuthandizani kuti mudzapulumuke.
□ Zoona
□ Zonama
Ngati simunabatizike, Mulungu sakuimbani mlandu pa zocita zanu.
□ Zoona
□ Zonama
Ngati anzanu akubatizika, ndiye kuti inunso mukhoza kubatizika.
□ Zoona
□ Zonama
NGATI mukutsatila mfundo za Mulungu, mukucita zinthu zokuthandizani kukhala naye paubwenzi ndiponso mukuuza ena zimene mumakhulupilila, sizingakhale zacilendo kufuna kubatizika. Komano kodi mungadziŵe bwanji ngati ndinu wokonzeka kubatizika? Kuti muyankhe funso limeneli, tiyeni tikambilane mfundo zimene zili pamwambazi.
● Ubatizo ni wofunika kwa Mkhristu aliyense.
Zoona. Yesu analamula kuti ophunzila ake azibatizika. (Mateyo 28:19, 20) Ndipotu, ngakhale Yesu mwiniwakeyo anabatizika. Kuti mukhale wotsatila wa Khristu, muyenela kubatizika ngati mwakula kufika pamsinkhu woti mungathe kusankha zoti mubatizike komanso ngati muli wofunitsitsa kutelo.
● Colinga cacikulu ca ubatizo nico kukutetezani kuti musacite chimo.
Zonama. Ubatizo ni cizindikilo capoyela coonetsa kuti munadzipatulila kwa Yehova. Kudzipeleka kwanu kwa Yehova si pangano limene lingakulepheletseni kucita zinthu zimene mungakonde kucita muli kwanokha. M’malo mwake, munthu amadzipeleka kwa Yehova cifukwa coti akufunitsitsa kutsatila malamulo ake.
● Ubatizo umakuthandizani kuti mudzapulumuke.
Zoona. Baibo imati ubatizo ni cimodzi mwa zinthu zofunika kwambili zimene munthu ayenela kucita kuti adzapulumuke. (1 Petulo 3:21) Komabe, izi sizikutanthauza kuti munthu akabatizika ndiye kuti basi, adzapulumuka. Cifukwa cimene muyenela kubatizikila n’coti mumakonda Yehova ndipo mukufuna kumutumikila na mtima wanu wonse kwamuyaya.—Maliko 12:29, 30..
● Ngati simunabatizike, Mulungu sakuimbani mlandu pa zocita zanu..
Zonama. Kaya munthu ni wobatizika kapena ayi, Baibo imati ngati “akudziŵa kucita cabwino koma sacita, akucimwa.” (Yakobe 4:17) Conco ngati mukudziŵa zinthu zabwino zimene muyenela kucita ndipo ndinu wamkulu ndithu moti mungathe kuganizila mofatsa zamoyo wanu, mwina ni bwino kuti panopa mukambilane nkhaniyi na makolo anu kapena Mkhristu wolimba mwauzimu. Zimenezi zingakuthandizeni kuti mudziŵe zimene mungacite kuti mufike pobatizika.
● Ngati anzanu akubatizika, ndiye kuti inunso mukhoza kubatizika.
Zonama. Munthu amayenela kusankha yekha kuti akufuna kubatizika. (Salmo 110:3) Muyenela kubatizika ngati mwadziŵa zinthu zonse zimene muyenela kucita monga wa Mboni za Yehova, ndiponso mukaona kuti mukhoza kukwanitsa kucita zimenezo.—Mlaliki 5:4, 5.
Ubatizo Umasintha Moyo Wanu
Ubatizo umasintha moyo ndipo munthu akabatizika amadalitsika kwambili. Komabe, munthu akabatizika amakhala na udindo waukulu wocita zinthu mogwilizana na lonjezo la kudzipeleka kwake kwa Yehova.
Ndiyeno, kodi ndinu wokonzeka kubatizika? Ngati n’conco, muyenela kukhala wosangalala kwambili. Mukabatizika, mudzakhala na mwayi wamtengo wapatali wotumikila Yehova, ndiponso wokhala na moyo wosonyeza kuti munadzipatulila kwa Yehova na mtima wonse.—Mateyo 22:36, 37.
M’MUTU WOTSATILA
Onani zimene mungacite kuti mukhale na zolinga pamoyo wanu ndiponso kuti zinthu zizikuyendelani bwino.
LEMBA LOFUNIKILA
“Mupeleke matupi anu nsembe yamoyo, yoyela, yovomelezeka kwa Mulungu, ndiyo utumiki wopatulika mwa kugwilitsa nchito luntha la kulingalila.”—Aroma 12:1.
MFUNDO YOTHANDIZA
Mothandizidwa na makolo anu, pezani munthu wina mumpingo amene angakuthandizeni kupita patsogolo mwauzimu.—Machitidwe 16:1-3.
KODI MUDZIŴA . . .
Ubatizo ni mbali yofunika kwambili ya “cizindikilo” coonetsa kuti munthu ni woyenela kukapulumuka.—Ezekieli 9:4-6.
ZOTI NICITE
Kuti nifike pobatizika, niyesetsa kuti nimvetse bwino mfundo za m’Baibo zotsatilazi: ․․․․․
Zimene nikufuna kufunsa makolo anga pankhaniyi ni izi ․․․․․
MUGANIZA BWANJI?
● N’cifukwa ciani ubatizo si nkhani ya masewela?
● N’ciani cingapangitse wacinyamata kubatizika asanakonzekele?
● Nanganso n’ciani cingadodometse wacinyamata kuti adzipatulile kwa Yehova kuti akabatizike?
[Mau okopa]
Kukumbukila kuti ndine wobatizika kunanithandiza kusankha zinthu mwanzelu, ndiponso kupewa zinthu zimene zikananigwetsela m’mavuto aakulu.”—Anatelo Holly
[Bokosi/Cithunzi]
Zimene Anthu Amafunsa Kaŵili-Kaŵili Zokhudza Ubatizo
Kodi ubatizo umaimila ciani? Kumizidwa na kuvuulidwa m’madzi kumatanthauza kuti mwasiya moyo wongocita zimene mukufuna ndipo lomba mukuyamba moyo wocita cifunilo ca Yehova.
Kodi kudzipatulila kwa Yehova kumatanthauza ciani? Kumatanthauza kupeleka moyo wanu wonse kwa Mulungu na kulonjeza kuti muziika zofuna zake patsogolo m’moyo wanu. (Mateyo 16:24) Conco, muyenela kudzipatulila kwa Yehova m’pemphelo musanabatizike.
Kodi muyenela kumacita zotani musanabatizike? Muyenela kumacita zinthu zogwilizana na Mawu a Mulungu, na kuuzako ena zimene mumakhulupilila. Muyenelanso kumapemphela na kuphunzila Mawu ake, zimene zingakuthandizeni kukhala naye paubwenzi. Komanso, muyenela kumatumikila Yehova cifukwa coti mwasankha nokha kucita zimenezo, osati cifukwa cokakamizidwa na ŵena.
Kodi munthu ayenela kubatizika akafika zaka zingati? Zaka kapena kuti msinkhu wa munthu si ndizo zofunikila kwenikweni kuti munthu abatizike. Komabe, muyenela kukhala wamkulu ndithu moti mukhoza kumvetsa tanthauzo la kudzipatulila kwanu kwa Mulungu.
Kodi muyenela kucita ciani ngati mukufuna kubatizika koma makolo anu akukuuzani kuti muyembekeze coyamba? Mwina iwo akucita zimenezo n’colinga coti muyambe mwakula ndithu kuuzimu. Mvelani malangizo awowo, ndipo poyembekezela ubatizo, gwilitsani nchito nthawi imeneyo kulimbitsa ubwenzi wanu na Yehova.—1 Samueli 2:26.
[Bokosi]
Wekishiti
kodi mufuna kubatizika?
Gwilitsani nchito mafunso na mfundo zotsatilazi kuti muone ngati mwapita patsogolo mwauzimu kuti mubatizike. Musanalembe mayankho anu, onetsetsani kuti mwaŵelenga malembawo.
Kodi pali pano mukuonetsa m’njila ziti kuti mumadalila Yehova?—Salmo 71:5. ․․․․․
Kodi mwacitapo zotani zimene zionetsa kuti muli na luntha la kuzindikila, ndipo mumatha kusiyanitsa coyenela na colakwika?—Aheberi 5:14. ․․․․․
Kodi mumapemphela nthawi zonse?. ․․․․․
Mukamapemphela, kodi muchula zimene mukufuna? Kodi mapemphelo anuwo amaonetsa kuti mumam’kondadi Yehova?—Salmo 17:6. ․․․․․
Lembani pansi apa zolinga zilizonse zimene mukufuna kukhala nazo pankhani ya pemphelo ․․․․․.
Kodi mumacita phunzilo la Baibo lapamweka nthawi zonse?—Yoswa 1:8 ․․․․․.
Kodi mumacita zinthu zotani pa phunzilo lanu laumwini? ․․․․․
Lembani pansi apa zolinga zilizonse zimene mukufuna kukhala nazo pa nkhani ya phunzilo laumwini. ․․․․․
Kodi mumacita utumiki wanu mogwila mtima? (Mwacitsanzo: Kodi mungakwanitse kufotokozela anthu ena mfundo zoyambilila za m’Baibo? Kodi mumacita maulendo obwelelako kwa anthu acidwi? Kodi mukuyesetsa kuti mukhale na phunzilo la Baibo lapanyumba?)
□ Inde □ Ayi
Kodi mumapita mu ulaliki ngakhale makolo anu sanapite?—Machitidwe 5:42.
□ Inde □ Ayi
Lembani pansi apa zolinga zimene mukufuna kukhala nazo pa nkhani ya ulaliki.—2 Timoteyo 2:15 ․․․․․.
Kodi mungati mumafika pa Misonkhano nthawi zonse kapena ayi?—Aheberi 10:25 ․․․․․.
Kodi mumatengako mbali pa misonkhano m’njila ziti?
Kodi mumapita ku misonkhano ngakhale ngati makolo anu sanapite (ngati amakulolezani kutelo)?
□ Inde □ Ayi
Kodi mungati mumakondadi kucita cifunilo ca Mulungu?—Salimo 40:8.
□ Inde □ Ayi
Kodi ni pazocitika ziti pamene munakana kutengela zocita za anzanu?—Aroma 12:2 ․․․․․.
Kodi mukukonza zotani kuti mupitilize kum’konda kwambili Yehova?—Yuda 20, 21. ․․․․․
Kodi mungapitilize kutumikila Yehova ngakhale makolo anu, komanso anzanu, atasiya kum’tumikila?—Mateyu 10:36, 37.
□ Inde □ Ayi
[Cithunzi]
Ubatizo uli ngati ukwati cifukwa umasintha moyo wa munthu. Conco, ni bwino kuganiza mofatsa musanabatizike