10
Kodi Baibo Ingan’thandize Bwanji?
KUKHALA IWE UNGACITE BWANJI?
Ganizila cocitika ici: David ali paulendo ayendetsa motoka. Kenako, aona kuti ciliconse cioneka cacilendo. Poyang’ana zikwangwani za m’mbali mwa mseu, David wadziŵa kuti wasoŵa. Azindikila kuti penapake watenga mseu wolakwika.
Kukhala David, ungacite bwanji?
YAMBA WAIMA NA KUGANIZA!
Sankha zimene ungacite pa izi:
-
Kufunsa anthu kuti akuonetse njila.
-
Kuyang’ana pa mapu, olo pa pulogilamu ya GPS.
-
Kungopitiliza kuyendetsa motoka kuti mwamwayi ungatulukile m’njila imene ufuna.
Mwacionekele, C si yothandiza kweni-kweni.
Koma B ni yabwino kuposa A. Zili conco cifukwa mapu kapena GPS imakutsogolela paliponse pamene wafika.
Baibo ingakuthandize m’njila yofanana.
Buku yofunika kwambili imeneyi
-
ingakuthandize pa mavuto mu umoyo wako
-
ingakuthandize kudzidziŵa bwino kuti ukhale munthu wanzelu
-
ingakupatse nzelu zopezela umoyo wabwino lelo mpaka muyaya
KUYANKHA MAFUNSO OFUNIKA KWAMBILI MU UMOYO
Mwana akangoyamba kukamba, amafunsa mafunso.
-
Dzuŵa imayenda kuti?
-
Nyenyezi ni zingati?
Tikakula timayamba kufunsa pa zocitika za m’dziko.
-
N’cifukwa ciani anthu amafa?
Kodi udziŵa kuti mayankho pa mafunso aya alimo m’Baibo?
Anthu ambili amakamba kuti nkhani zonse za m’Baibo ni nthano cabe, inasila nchito, kapena ni yovuta kuimvetsetsa. Kodi uganiza vuto ni Baibo, kapena ni zimene anthu amakamba? Kodi si zoona kuti amauzidwa zolakwika?
Mwacitsanzo, anthu amaganiza kuti Baibo imakamba kuti Mulungu ndiye amalamulila dziko lonse. Koma zimenezo n’zosatheka! M’dziko muli cipwilikiti cokha-cokha. Muli mavuto, matenda, imfa, umphawi, na ngozi zosiyana-siyana. Kodi n’zoona kuti Mulungu wacikondi ndiye amacititsa mavuto onse aya?
Koma kodi ufuna kudziŵa yankho ya zoona? Mwina ungadabwe kumvela amene Baibo imamutomola kuti ndiye wolamulila dziko lonse lapansi.
Tikhulupilila waona kuti malangizo ali m’kabuku kano ni ocokela m’Baibo. A Mboni za Yehova amadziŵa bwino kuti malangizo anzelu amapezeka m’Baibo. Zili conco cifukwa mau ake “anauzilidwa ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, kuwongola zinthu.” (2 Timoteyo 3:16, 17) Ufunika kuisanthula na kuimvetsetsa bwino buku imeneyi—yamakedzana, komanso yamakono!
[DO NOT SET] This page will not contain any WEB tags or SEO information.