3
Ningakambilane Bwanji na Makolo Anga?
KUKHALA IWE UNGACITE BWANJI?
Ganizila cocitika ici: M’pa citatu madzulo. Geoffrey wa zaka 17, watsiliza bwino-bwino nchito zake za panyumba, manje akhala pansi kuti apumule. Iye wayasha TV n’kukhala bwino-bwino pa mpando umene amakonda.
Angokhala cabe, Atate ake atulukila ndipo aonekelatu kuti ni okwiya.
Amvekele: “Iwe Geoffrey! Zoona ungotaya nthawi apa kutamba TV, m’malo mothandiza mng’ono wako kulemba homuweki? Udzamvela liti iwe!”
“Ayamba,” ang’ung’udza conco Geoffrey, koma iwo amumvela.
Atate ake apita kwa iye. “Wati cia?”
“Palibe,” ayankha moipitsa nkhope Geoffrey.
Apa lomba atate ŵake akwiilatu. Amvekele: “Uyankha ine conco iwe!”
Sembe unali Geoffrey, ukanacita ciani kuti zisafike apa?
YAMBA WAIMA NA KUGANIZA!
Kukambilana na makolo ako kuli monga kuyendetsa motoka. Ukapeza cinthu cimene cachinga mseu, umapitila njila inangu.
CITSANZO:
“Cimanivuta kukambilana na atate,” anakamba conco Leya. “Zimacitika kuti nawafotokozela zinthu kwa kanthawi ndithu, nimangodabwa anifunsa kuti, ‘Wati? Ukamba na ine?’”
APA LEYA ANGACITE CIMODZI PA ZINTHU ZITATU IZI.
-
Kuŵazazila atate ŵake.
Leya angakalipile atate ake kuti, “Nikamba na imwe! Muzimvela ngati munthu akamba!”
-
Kuleka kukambilana nawo.
Leya angalekeletu kuuzako atate ake vuto yake.
-
Ayembekezela nthawi yabwino yokawauzanso nthaniyo.
Panthawi ina yabwino Leya angakambilane na atate ake, kapena angaŵalembele kalata kuŵauza vuto lake.
Kodi iwe, Leya ungamulangize Kusankhapo citi?
GANIZILA IZI: Atate ake a Leya maganizo awo ayenda kwina—sadziŵanso kuti iye wakhumudwa. Conco ngati Leya angasankhe kucita zili pa A, atate ake angadabwe kuti akalipa ciani. Ndipo kucita izi sikungaphule kanthu, kudzangoonetsa kuti alibe ulemu. (Aefeso 6:2) Conco, kusankha A sikungathandize aliyense.
Olo kuti njila ya B ndiyo ingakhale yosavuta, sindiyo yanzelu. Cifukwa? Kuti atate ake am’thandize pa vuto lake, afunika kukambilana nawo. Ndiponso, kuti atate ake am’thandizedi afunikila kudziŵa zimene zim’citikila mu umoyo wake. Kukhala zii nako sikungathandize aliyense.
Koma ngati angasankhe zili pa C, ndiye kuti Leya safuna kulola copinga ciliconse kum’lepheletsa kukambilana ndi atate ake. Adzayesa kupeza nthawi ina yokambilana nawo. Ndipo ngati angasankhe kulemba kalata, panthawi imeneyo adzayamba kumvelako bwino.
Ubwino wina wolemba kalata ni wakuti akhoza kumasuka kufotokoza bwino-bwino vuto lake. Atate ake poŵelenga kalatayo, angamvetse manje zimene anali kuyesa kuwauza, ndi kumvetsetsa bwino vuto lake. Conco, njila ya C ingakhale yothandiza onse aŵili, Leya na atate ŵake. Kaya m’pamaso-m’pamaso kapena mu kalata, njila imeneyi imagwilizana ndi malangizo a m’Baibo akuti: “Titsatile zinthu zobweletsa mtendele ndiponso zolimbikitsana.”—Aroma 14:19.
N’cianinso cina cimene Leya angacite?
Yesa kuganizila njila imodzi, ndipo uilembe pa mzela pansi apa. Ulembenso zimene zingakhale zotsatilapo zake.
UZIPEWA KUPANGITSA MAKOLO AKO KUMVELAPO ZOSIYANA
Uzikumbukila kuti, zimene ungakambe zingasiyane na zimene makolo ako angamvelepo.
MWACITSANZO:
Ngati makolo ako akufunsa kuti n’cifukwa ciani uoneka wosakondwela. Iwe n’kuyankha kuti, “Nili cabe bwino.”
Makolo ako angamvele monga uwauza kuti: “Siningakuuzeni, sinikudalilani. N’zauzako anzanga vuto langa, osati imwe.”
Yelekeza kuti wakumana na vuto linalake ndipo makolo ako afuna kukuthandiza. Ukakamba kuti: “Osadandaula. Zonse zidzakhala bwino.”
-
Iwo angamvele monga uwauza kuti:
-
Kuti uyankhe bwino ungakambe kuti: