GAWO 2
Khalani Wokhulupilika kwa Wina ndi Mnzake
“Cimene Mulungu wacimanga pamodzi, munthu asacilekanitse.” —Maliko 10:9
Yehova amafuna kuti tizikhala okhulupilika. (Mika 6:8) Zimenezi n’zofunika makamaka m’cikwati canu, cifukwa ngati simukhulupililana ndiye kuti simungadalilane. Ndipo kudalilana n’kofunika kuti cikondi cikule.
Masiku ano, kukhulupilika kukusoŵa m’zikwati. Kuti muteteze cikwati canu, muyenela kuyesetsa kucita zinthu ziŵili.
1 MUZIONA BANJA LANU KUKHALA CINTHU COFUNIKA KWAMBILI
ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA: “Muzitsimikizila kuti zinthu zofunika kwambili ndi ziti.” (Afilipi 1:10) Cikwati canu n’cimodzi mwa zinthu zofunika kwambili paumoyo wanu. Mufunikadi kuciona conco.
Yehova amafuna kuti muzisamalila kwambili mwamuna kapena mkazi wanu ndi kuti ‘musangalale ndi moyo’ pamodzi. (Mlaliki 9:9) Iye amafotokoza bwino kuti simufunika kunyalanyaza mnzanu wa m’cikwati, koma muyenela kupeza njila zosangalatsilana. (1 Akorinto 10:24) Mnzanu wa m’cikwati aziona kuti ndi wofunika ndipo mumamukonda.
ZIMENE MUNGACITE:
-
Tsimikizilani kuti nthawi zambili mukuceza pamodzi, ndi kumvetsela mosamalitsa zimene mnzanu akamba
-
Muziganizilana
2 TETEZANI MTIMA WANU
ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA: “Aliyense woyang’anitsitsa mkazi mpaka kumulakalaka, wacita naye kale cigololo mumtima mwake.” (Mateyu 5:28) Ngati munthu amangokhalila kuganiza za ciwelewele, m’mau ena tingati ndi wosakhulupilika kwa mnzake wa m’cikwati.
Yehova amanena kuti mufunika ‘kuteteza mtima wanu.’ (Miyambo 4:23; Yeremiya 17:9) Kuti mucite zimenezi muyenela kuteteza maso anu. (Mateyu 5:29, 30) Tsatilani citsanzo ca Yobu, amene anacita pangano ndi maso ake kuti asayang’ane mkazi momulakalaka kapena kuti momukhumbila. (Yobu 31:1) Yesetsani nthawi zonse kupewa kuonelela zamalisece. Pewani kukopana ndi munthu aliyense amene si mkazi kapena mwamuna wanu.
ZIMENE MUNGACITE:
-
Lolani kuti ena adziŵe kuti mumakondana kwambili ndi mkazi kapena mwamuna wanu.
-
Ganizilani mmene mnzanu wa m’cikwati akumvelela, ndipo lekani kuceza ndi anthu alionse amene angacititse mkazi kapena mwamuna wanu kusakondwela