Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MBALI 4

Kudziimba Mlandu​—“Ndiyeletseni ku Chimo Langa”

Kudziimba Mlandu​—“Ndiyeletseni ku Chimo Langa”

“Nditasiya nchito imene ndinali kugwila kale, ndinapeza nchito ina. Nchito yatsopanoyi inathandiza kuti umoyo wa banja lathu ukhale wapamwamba. Koma cifukwa ca nchitoyo, ndinayamba kucita zinthu zosayenela monga kukondwelela maholide, kutenga mbali m’ndale, ndi kupita ku cipembedzo cina. Ndinakhala Mboni ya Yehova yozilala kwa zaka 40. M’kupita kwa nthawi, ndinayamba kuganiza kuti Yehova sangandikhululukile. Sindinayembekezele kuti ndidzasiya kudziimba mlandu, cifukwa ndinayamba kucita zoipa nditaphunzila kale coonadi.”—Martha.

KUDZIIMBA mlandu kuli ngati katundu wolemela kwambili. Mfumu Davide analemba kuti: “Zolakwa zanga zakwela kupitilila mutu wanga. Zandilemela kwambili ngati katundu wolemela.” (Salimo 38:4) Akristu ena amezedwa ndi cisoni copitilila malile, ndipo amaganiza kuti Yehova sangawakhululukile. (2 Akorinto 2:7) Kodi ndi bwino kuganiza zimenezi? Kodi n’zoona kuti Yehova sangakukhululukileni cifukwa cakuti munacita macimo aakulu? Iyai si zoona.

“Tiyeni Tikambilane”

Yehova sanyalanyaza anthu olapa, koma amafuna kuwathandiza. M’fanizo la mwana woloŵelela, Yesu anayelekezela Yehova ndi tate wacikondi amene mwana wake anacoka panyumba ndi kuyamba khalidwe loipa. Patapita nthawi, mwanayo anaganiza zobwelela kunyumba. “[Mwanayo] ali capatali ndithu, bambo akewo anamuona ndipo anagwidwa cifundo. Pamenepo anamuthamangila ndi kumukumbatila ndipo anamupsompsona mwacikondi.” (Luka 15:11-20) Kodi mukufuna kukhalanso bwenzi la Yehova koma mukuona kuti ‘muli naye capatali ndithu’? Yehova ndi wacifundo mofanana ndi tate wa m’fanizo la Yesu, ndipo ndi wokonzeka kukulandilani.

Koma bwanji ngati mukuganiza kuti macimo anu ndi aakulu kapena kuti ndi ambili ndipo Yehova sangakukhululukileni? Apa ndiye pofunika kukumbukila pempho la Yehova pa Yesaya 1:18. Lembali limati: “Yehova akuti, ‘Bwelani tsopano anthu inu. Tiyeni tikambilane ndipo ine ndikuthandizani kuti mukhalenso pa ubwenzi wabwino ndi ine. Ngakhale macimo anu atakhala ofiila kwambili, adzayela kwambili. Ngakhale atakhala ofiila ngati magazi, adzayela ngati thonje.’” Ndithudi, Yehova amakhululuka ngakhale macimo athu atakhala ngati magazi othimbilila pa nsalu yoyela.

Yehova safuna kuti muzingovutika ndi cikumbumtima. Iye amafuna kuti mukhale pa mtendele. Ndipo mtendele umenewu mungakhale nao ngati iye wakukhululukilani ndipo ngati muli ndi cikumbumtima coyela. Nanga mungacite ciani kuti zimenezi zitheke? Onani zinthu ziŵili zimene Mfumu Davide anacita. Coyamba, iye anati: “Ndidzaulula kwa Yehova macimo anga.” (Salimo 32:5) Musaiŵale kuti Yehova wakupemphani kale kuti mulankhule naye m’pemphelo, ndi kuti ‘mukambilane.’ Mvelani pempho limenelo. Muululileni Yehova macimo anu onse, ndipo muuzeni za kukhosi kwanu. Malinga ndi zimene zinamucitikila Davide, iye anapemphela ndi cidalilo conse kuti: “Ndiyeletseni ku chimo langa. . . . Inu Mulungu, simudzanyoza mtima wosweka ndi wophwanyika.”—Salimo 51:2, 17.

Caciŵili, Davide analandila thandizo kwa mneneli Natani, munthu amene Mulungu anasankha monga womuimila. (2 Samueli 12:13) Masiku ano, Yehova waika akulu mumpingo. Akuluwa anaphunzitsidwa mmene angathandizile anthu olapa kukhalanso pa ubwenzi ndi iye. Mukapita kwa io, adzakuŵelengelani Malemba ndipo adzakupemphelelani. Zimenezi zidzakuthandizani kukhazika mtima pansi, kucepetsa kapena kuthetselatu maganizo odziimba mlandu, ndi kucila mwakuuzimu.—Yakobo 5:14-16.

Yehova afuna kuti mukhale ndi cikumbumtima coyela

“Wodala ndi Munthu Amene Wakhululukidwa Zolakwa Zake”

Mwina mungaganize kuti n’zovuta kuulula macimo anu kwa Yehova ndi kwa akulu. Davide nayenso anaganiza conco. Iye ‘anakhala cete’ kwa nthawi ndithu osaulula macimo ake. (Salimo 32:3) Koma pambuyo pake, iye anayamikila ubwino woulula macimo ake ndi kuongola njila yake.

Kaamba ka zimenezi, Davide anaphindula kwambili cifukwa anakhalanso wacimwemwe. Iye analemba kuti: “Wodala ndi munthu amene wakhululukidwa zolakwa zake, amene macimo ake aphimbidwa.” (Salimo 32:1) Anapemphelanso kuti: “Inu Yehova, tsegulani milomo yangayi, kuti pakamwa panga patamande inu.” (Salimo 51:15) Poona kuti mlandu wake watha, ndipo pofuna kuyamikila Mulungu cifukwa com’khululukila, Davide anayamba kuuza ena za Yehova.

Yehova afuna kuti mukhale ndi cikumbumtima coyela. Afunanso kuti muziuza ena za iye ndi zolinga zake momasuka ndi mwacimwemwe. (Salimo 65:1-4) Musaiŵale kuti Mulungu afuna “kuti macimo anu afafanizidwe, ndiponso kuti nyengo zotsitsimutsa zibwele” pa inu “kucokela kwa Yehova.”—Machitidwe 3:19.

Izi n’zimene zinacitikila Martha. Iye anati: “Mwana wanga wamwamuna sanaleke kunditumizila magazini a Nsanja ya Mlonda ndi Galamukani! Pang’onopang’ono, ndinayambanso kuphunzila za Yehova. Ngati pali cimene cinandivuta kwambili kucita, ndi kupempha Mulungu kuti akhululuke macimo anga onse. Ngakhale kuti zinali zovuta, ndinapemphela kwa Mulungu kuti andikhululukile. Mpaka pano sindikhulupilila kuti ndinatenga zaka 40 kuti ndibwelele kwa Yehova. Nkhani yangayi ndi umboni wakuti kaya munthu akhale wozilala kwa zaka zingati, angayambenso kutumikila Mulungu ndipo Mulungu angapitilize kum’konda.”