MBALI 3
Kukhumudwa—Tikakhala Ndi “Cifukwa Codandaulila”
“Mlongo wina mumpingo wathu anandinamizila kuti ndinamubela ndalama. Anthu ena mumpingo atamva zimenezo, anayamba kukhala kumbali ya mlongoyo. Patapita nthawi, mlongoyo anandiuza kuti anamva zinazake zimene zinandimasula pa mlanduwo. Ngakhale kuti mlongoyo anapepetsa, zinandivuta kumukhululukila poganizila mmene mbili yanga inaipila.”—Linda.
KODI inunso munakhumudwapo monga Linda cifukwa ca zimene Mkristu mnzanu anakucitilani? N’zomvetsa cisoni kuti anthu ena anakhumudwa kwambili cifukwa ca zocita za ena cakuti zinasokoneza umoyo wao wa kuuzimu. Kodi ndi zimene zinakucitikilani?
Kodi Munthu ‘Angatilekanitsa ndi Cikondi ca Mulungu’?
N’zoona kuti zingakhale zovuta kukhululukila Mkristu mnzathu amene watikhumudwitsa, makamaka podziŵa kuti Akristu ayenela kukondana. (Yohane 13:34, 35) Zimakhala zopweteka mtima kwambili Mkristu mnzathu akatikhumudwitsa.—Salimo 55:12.
Baibulo limakamba kuti nthawi zina Akristu ena amacita zinthu zimene zingacititse anzao kukhala ndi “cifukwa codandaulila.” (Akolose 3:13) Zimenezo zikaticitikila, zimakhala zovuta kuzipilila. Kodi pali zimene zingatithandize? Taganizilani mfundo zitatu izi za m’Malemba.
Atate wathu wa kumwamba amaona zonse zimene zamacitika. Yehova amaona zonse zimene zimacitika, ngakhale mavuto amene tingakumane nao cifukwa ca cisalungamo cimene ena angaticitile. (Aheberi 4:13) Kuonjezela apo, Yehova amavutikanso ife tikamavutika. (Yesaya 63:9) Iye salola kuti ‘cisautso, kapena zowawa’ kapena cina ciliconse, ngakhalenso mtumiki wake wina “kutilekanitsa ndi cikondi” cake. (Aroma 8:35, 38, 39) Motelo, ifenso sitiyenela kulola ciliconse kapena aliyense kutilekanitsa ndi Yehova.
Kukhululuka sikutanthauza kulekelela colakwa. Tikakhululukila anthu amene amatilakwila, sizitanthauza kuti tacepetsa, talungamitsa kapena talekelela zocita zao. Musaiŵale kuti Yehova savomeleza ucimo, koma amakhululuka ngati pali cifukwa cofunikila kutelo. (Salimo 103:12, 13; Habakuku 1:13) Yehova akamatilimbikitsa kukhululukila ena, amakhala akutiuza kuti titengele citsanzo cake. Iye ‘sasunga mkwiyo mpaka kalekale.’—Salimo 103:9; Mateyu 6:14.
Timapindula tikacotsa cakukhosi. Mwa njila yotani? Taganizilani kuti mwanyamula mwala wosalemela kwambili, ndipo mwaugwila m’manja mutatambasula mkono wanu. Sizingavute kunyamula mwalawo kwa mphindi zocepa poyamba. Koma bwanji ngati munganyamule mwalawo kwa nthawi yaitali? Kodi mungakwanitse kuugwila conco kwa mphindi zingati? Kwa ola limodzi kapena kuposelapo? Mosakaikila, mkono wanu ungatope kwambili. N’zoona kuti kulemela kwa mwalawo sikungasinthe. Koma kunyamula mwalawo kwa nthawi yaitali ndi kumene kungapangitse kuti mwalawo uyambe kulemela. Izi n’zimene zimacitika tikasunga cakukhosi. Tikasunga cakukhosi kwa nthawi yaitali, ngakhale Miyambo 11:17.
nkhaniyo itakhala yocepa bwanji, timadzipweteka tokha. M’pake kuti Yehova amatilimbikitsa kucotsa cakukhosi. Indedi, tikacotsa cakukhosi timapindula.—“Zinali Ngati Kuti Yehova Mwiniyo Akulankhula Nane”
N’ciani cinathandiza Linda kuti asasunge cakukhosi pa zimene Mkristu mnzake anam’citila? Cimodzi mwa zinthu zimene iye anacita ndi kusinkhasinkha pa Malemba amene amafotokoza za ubwino wokhululukila ena. (Salimo 130:3, 4) Linda anakhudzidwa mtima kwambili podziŵa kuti ngati tikhululukila ena, Yehova amatikhululukilanso. (Aefeso 4:32–5:2) Pofotokoza mmene mfundozo zinamukhudzila, Linda anati: “Zinali ngati kuti Yehova mwiniyo akulankhula nane.”
M’kupita kwa nthawi, Linda anacotsa cakukhosi. Iye anakhululukila mlongo uja, ndipo panopa mlongoyo ndi bwenzi lake lapamtima. Linda akupitilizabe kutumikila Yehova. Dziŵani kuti Yehova afuna kukuthandizani kuti mucite cimodzimodzi.