Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kumapeto

Kumapeto

Kodi nthawi zina mumakumbukila mmene munali kusangalalila ndi anthu a Yehova kapena mmene munasangalalila kwambili ndi msonkhano wina wa mpingo? Kodi mumakumbukilanso msonkhano wacigawo wosaiŵalika umene munapezekapo, zinthu zabwino zimene zinakucitikilani mu ulaliki, kapena makambilano olimbikitsa amene munali nao ndi Mkristu mnzanu? Ngati mumatelo, ndiye kuti simunaiŵale Yehova, ndipo nayenso sanakuiŵaleni. Iye sanaiŵale zimene munali kucita pom’tumikila, ndipo ndi wofunitsitsa kukuthandizani kubwelela kwa iye.

Yehova akuti: “Inetu ndidzafunafuna nkhosa zanga ndi kuzisamalila. Ndidzasamalila nkhosa zanga ngati mmene amacitila munthu amene amadyetsa gulu la nkhosa zake pamene ali pakati pa nkhosa zimene zinabalalika . . . ndidzapulumutsa nkhosazo kucokela m’malo onse kumene zinabalalikila.”—Ezekieli 34:11, 12.