Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MBALI 2

Nkhawa​—“Timapanikizidwa Mwamtundu Uliwonse”

Nkhawa​—“Timapanikizidwa Mwamtundu Uliwonse”

“Cikwati cathu cinatha pambuyo pokhala m’cikwati ndi amuna anga zaka 25. Ana anga anasiya coonadi. Ndinayamba kudwala matenda aakulu osiyanasiyana, ndipo ndinapsinjika maganizo. Ndinasowa koloŵela ndipo ndinaona kuti sindingathenso kupilila. Ndinasiya kusonkhana, kenako ndinazilala.”—June.

MUNTHU aliyense, kuphatikizapo anthu a Mulungu, angakhale ndi nkhawa. Wamasalimo analemba kuti malingalilo osautsa anali atamuculukila mumtima mwake. (Salimo 94:19) Pofotokoza za nthawi ya mapeto, Yesu nayenso anakamba kuti cifukwa ca “nkhawa za moyo,” kutumikila Yehova kudzaoneka kukhala kovuta. (Luka 21:34) Nanga bwanji za inu? Kodi mumakhala ndi nkhawa cifukwa ca mavuto a zacuma, mavuto a m’banja, kapena thanzi lanu? Kodi Yehova angakuthandizeni bwanji kupilila?

“Mphamvu Yoposa Yacibadwa”

Ife sitingalimbane ndi nkhawa patokha. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Timapanikizidwa mwamtundu uliwonse . . . Timathedwa nzelu . . . Timagwetsedwa pansi.” Komabe, iye anakambanso kuti ‘sitipsinjidwa moti n’kulephela kusuntha,’ ‘siticita kusoŵa koloŵela,’ ndipo “sitionongedwa.” N’ciani cimatithandiza kupilila? Ndi “mphamvu yoposa yacibadwa” yocokela kwa Mulungu Wamphamvuyonse, Yehova.—Akorinto 4:7-9.

M’mbuyomu Mulungu anali kukupatsani “mphamvu yoposa yacibadwa,” si conco kodi? Kodi mukukumbukila mmene nkhani inayake yolimbikitsa inakuthandizilani kumvetsetsa kukoma mtima kwa Yehova? Kodi cikhulupililo canu m’malonjezo a Yehova cinalimba kwambili pamene munauzako ena za ciyembekezo ca Paladaiso? Tikamapezeka pa misonkhano yacikristu ndi kuuzako ena zimene timakhulupilila, timalandila mphamvu zotithandiza kupilila nkhawa za moyo. Mwakutelo, mtima umakhala pa mtendele ndipo timatumikila Yehova mwacimwemwe.

“Talaŵani Ndipo Muone Kuti Yehova Ndi Wabwino”

Nthawi zina mungaone kuti ndinu wopanikizika. Mwacitsanzo, Yehova amatiuza kuti tiyenela kufunafuna Ufumu coyamba ndi kuti tisanyalanyaze zinthu za kuuzimu. (Mateyu 6:33; Luka 13:24) Koma bwanji ngati mulephela kucita zambili cifukwa ca citsutso, matenda, kapena mavuto a m’banja? Nanga bwanji ngati nchito yanu imakuonongelani nthawi ndi mphamvu, zimene mukanagwilitsila nchito kutumikila limodzi ndi mpingo? Ngati muli ndi zocita zambili, koma mulibe nthawi ndi mphamvu yocitila zinthu zimenezo, mungakhale ndi nkhawa. Mwina mungafike mpaka poganiza kuti Yehova akufuna zimene simungakwanitse.

Yehova amatimvetsa. Iye sayembekezela kuti tizicita zinthu zimene sitingakwanitse. Iye amadziŵanso kuti zimatenga nthawi kuti munthu asiye kukhala ndi nkhawa.—Salimo 103:13, 14.

Mwacitsanzo, ganizilani mmene Yehova anasamalila mneneli Eliya. Kodi Yehova anadzudzula mneneliyu ndi kum’lamula kuti abwelele kukagwila nchito yake panthawi imene anakhumudwa ndi kuthaŵila ku cipululu cifukwa ca mantha? Iyai. Yehova anatuma mngelo maulendo aŵili. Mngeloyo anadzutsa Eliya pang’onopang’ono ndi kum’patsa cakudya. Eliya anali akali ndi nkhawa ndi mantha ngakhale pambuyo pa masiku 40. N’ciani cimene Yehova anacitanso kuti athandize Eliya? Coyamba, Yehova anatsimikiza Eliya kuti adzam’teteza. Caciŵili, Yehova anatonthoza Eliya ndi “mau acifatse apansipansi.” Cacitatu, Yehova anam’dziŵitsa kuti panalinso anthu ena masauzande ambili omwe anali kulambila Mulungu mokhulupilika. Posapita nthawi, Eliya anakhalanso mneneli wacangu. (1 Mafumu 19:1-19) Tiphunzilapo ciani pa nkhaniyi? Eliya atafooka ndi nkhawa, Yehova analeza naye mtima, ndipo anam’citila cifundo. Yehova sanasinthe. Iye amatisamalila kwambili monga mmene anacitila ndi Eliya.

Musaganize kuti mufunika kupatsa Yehova zinthu zimene simungakwanitse. Musayembekezele kuti mudzangoyamba ndi mphamvu ngati kale. Mwacitsanzo, wocita mpikisano wothamanga akasiya kulimbitsa thupi lake kwa miyezi ingapo kapena zaka zingapo, angavutike kuyambanso kuthamanga monga kale nthawi yomweyo. M’malo mwake, iye amafunika kuyamba pang’onopang’ono kulimbitsa thupi, zimene zingamuthandize kupilila pa mpikisano wake. Akristu naonso ali ngati anthu ocita mpikisano wothamanga. Iwo sathamanga popanda colinga. (1 Akorinto 9:24-27) Bwanji osayamba ndi kuziikila colinga cakuuzimu cimene mungakwanitse pakali pano? Mwacitsanzo, mungayambe ndi kupezeka pa msonkhano wa mpingo. M’pempheni Yehova kuti akuthandizeni kukwanilitsa colinga cimeneco. Mukalimba mwakuuzimu, ‘mudzalaŵa ndi kuona kuti Yehova ndi wabwino.’ (Salimo 34:8) Musaiŵale kuti ciliconse cimene mungacite poonetsa kuti mumakonda Yehova, kaya cinthuco ndi cacing’ono bwanji, Mulungu amaona.—Luka 21:1-4.

Yehova sayembekezela kuti tizicita zinthu zimene sitingakwanitse

“Cilimbikitso Cimene Ndinali Kufunikila”

Kodi Yehova anathandiza bwanji mlongo June kubwelela kwa iye? June anati: “Ndinali kupemphela kwa Yehova kuti andithandize. Ndiyeno apongozi anga aakazi anandiuza za msonkhano umene unali kudzacitikila m’tauni yathu. Conco, ndinaganiza zokapezekapo tsiku limodzi cabe. Ndinakondwela kwambili kugwilizananso ndi anthu a Yehova. Msonkhanowo unali cilimbikitso cimene ndinali kufunikila. Panopa, ndikutumikilanso Yehova mwacimwemwe, ndipo ndikuona kuti umoyo wanga uli ndi phindu. Ndikudziŵa kuti ndifunikila abale ndi alongo kuposa kale, ndipo ndifunikilabe thandizo lao. Ndikuyamikila kwambili kuti ndinabwelela nthawi ikalipo.”