Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MBALI 1

“Nkhosa Zosocela Ndidzazifunafuna”

“Nkhosa Zosocela Ndidzazifunafuna”

Tiyelekezele kuti nkhosa yasocela. Inali kudya msipu limodzi ndi zinzake, koma pa cifukwa cosadziŵika bwino inasiya zinzake n’kusocela. Nkhosayo sikudziŵa kumene zinzake zili kapena kumene kuli mbusa. Ndiyeno dzuŵa likuyamba kuloŵa. Apa n’kuti nkhosayo ili kwayokha m’cigwa mmene muli zilombo zolusa. Mwadzidzidzi, ikumva mau a mbusa. Mbusayo akuithamangila. Atainyamula, aiika pacifuwa ndipo aifunda covala cake n’kupita nayo kunyumba.

NTHAWI zambili Yehova amafuna kuti anthu azimuona ngati mbusa waconco. M’Mau ake, iye amatitsimikizila kuti: “Inetu ndidzafunafuna nkhosa zanga ndi kuzisamalila.”—Ezekieli 34:11, 12.

“Nkhosa Zimene Ndikuzisamalila”

Kodi nkhosa za Yehova ndani? Nkhosa za Yehova ndi anthu amene ama’mkonda ndi kum’lambila. Baibulo limati: “Bwelani timuŵelamile ndi kumupembedza. Tiyeni tigwade pamaso pa Yehova amene ndiye Wotipanga. Pakuti iye ndi Mulungu wathu ndipo ife ndife anthu ake. Iye amatisamalila ngati nkhosa zimene akuweta.” (Salimo 95:6, 7) Mofanana ndi nkhosa zenizeni zimene zimatsatila mbusa, alambili a Yehova amafuna kutsatila Mbusa wao. Kodi io ndi angwilo? Iyai. Tikunena conco cifukwa cakuti mofanana ndi nkhosa, zimacitika atumiki a Mulungu ‘kubalalika,’ ‘kutaika,’ ndi ‘kusocela.’ (Ezekieli 34:12; Mateyu 15:24; 1 Petulo 2:25) Munthu akasocela, Yehova sataya mtima koma amayembekezelabe kuti munthuyo adzabwelela.

Kodi mumaona kuti Yehova ndi Mbusa wanube? Kodi Yehova amaonetsa bwanji kuti ndi Mbusa masiku ano? Tiyeni tione njila zitatu zimene amacitila zimenezi.

Iye amatidyetsa mwakuuzimu. Yehova akuti: “Nkhosazo ndidzazidyetsela m’malo a msipu wabwino . . . Kumeneko zizidzagona pansi m’malo abwino kwambili. Zizidzadya msipu wobiliŵila bwino.” (Ezekieli 34:14) Yehova sanalephelepo kutipatsa cakudya cosiyanasiyana ca kuuzimu cotsitsimula ndi ca pa nthawi yake. Timakhala ndi nkhani zosiyanasiyana m’mabuku, pamisonkhano, ndi m’mavidiyo. Kodi mungakumbukile nkhani inayake imene inali yankho la pemphelo lanu? Mwacionekele, umenewo unali umboni wakuti Yehova amakuganizilani panokha.

Iye amatiteteza ndi kutithandiza. Yehova akulonjeza kuti: “Nkhosa zosocela ndidzazifunafuna, zomwazika ndidzazibweza. Yothyoka mwendo ndidzaimanga mwendo wothyokawo. Yodwala ndidzailimbitsa.” (Ezekieli 34:16) Yehova amalimbitsa anthu ofooka kapena omwe akuvutika ndi nkhawa. Amasamala nkhosa zake ndi kuzithandiza kucila zikakhumudwa ndi okhulupilila anzao. Iye amathandiza anthu osocela kubwelela kwa iye ndipo saiŵala anthu amene ali ndi nkhawa.

Iye amaona kuti ndi udindo wake kutisamalila. Yehova akuti: “Ndidzapulumutsa nkhosazo kucokela m’malo onse kumene zinabalalikila. Nkhosa zosocela ndidzazifunafuna.” (Ezekieli 34:12, 16) Yehova amaona munthu wofooka monga nkhosa yosocela, osati ngati munthu woipa amene sangabwelele kwa iye. Mulungu amadziŵa nkhosa ikasocela, ndipo amaifunafuna. Akaipeza, amakondwela kwambili. (Mateyu 18:12-14) M’pake kuti iye amacha alambili ake oona kuti “nkhosa zanga, nkhosa zimene ndikuzisamalila.” (Ezekieli 34:31) Inunso ndinu nkhosa yake.

Yehova amaona munthu wofooka monga nkhosa yosocela, osati ngati munthu woipa amene sangabwelele kwa iye. Iye amakondwela akapeza nkhosayo

“Mubwezeletse Zinthu Zonse Kuti Zikhale Ngati Mmene Zinalili Kale”

Yehova akukufunafunani ndi kukupemphani kuti mubwelele kwa iye. Cifukwa ciani? Cifukwa afuna kuti mukhale osangalala. Iye akulonjeza kuti ‘adzagwetsela [nkhosa zake] mvula yambili yamadalitso.’ (Ezekieli 34:26) Lonjezo limeneli si maloto iyai, ndipo inu muli ndi umboni wa zimenezi.

Mwacitsanzo, tiyeni tibwelele pa nthawi imene munayamba kudziŵa Yehova. Kodi munamva bwanji mutaphunzila coonadi cocititsa cidwi conena za dzina la Mulungu ndi colinga cake pa anthu? Kodi sizinali zosangalatsa kupezeka pamisonkhano yadela ndi yacigawo ndi Akristu anzanu? Kodi munamva bwanji nthawi yoyamba imene munauza munthu wacidwi uthenga wabwino? Mosakaikila muyenela kuti munasangalala kwambili.

Conco, ngakhale pano mukhoza kukhalanso wosangalala ngati kale. Atumiki akale a Mulungu anapemphela kuti: “Inu Yehova, tibwezeni kwa inu ndipo ife tibwelela mwamsanga. Mubwezeletse zinthu zonse kuti zikhale ngati mmene zinalili kale.” (Maliro 5:21) Yehova anayankha pemphelo limenelo, ndipo anthu ake anayambanso kum’tumikila mwacisangalalo. (Nehemiya 8:17) Inunso Yehova adzakuyankhani pemphelo lanu lakuti mubwelele kwa iye.

Komabe, nthawi zina kubwelela kwa Yehova kungaoneke kovuta. Onani zopinga zina zimene zingakhalepo ndi mmene mungazigonjetsele.