Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI 14

Citani Zinthu Zonse Moona Mtima

Citani Zinthu Zonse Moona Mtima

“Tikufuna kucita zinthu zonse moona mtima.” —AHEBERI 13:18.

1, 2. N’cifukwa ciani Yehova amakondwela akaona kuti tikuyesetsa kukhala oona mtima? Pelekani citsanzo.

AMAI ndi mwana wao wamng’ono atuluka mu sitolo. Mwadzidzidzi, mwanayo waima ndipo nkhope yake ikuoneka yacisoni. Iye wanyamula kadoli kamene watenga m’sitolo. Anaiŵala kubweza kadoliko pamalo ake kapena kupempha amai ake kuti amugulile. Iye wada nkhawa ndipo auza amai ake kuti amuthandize. Amai ake amuuza kuti asade nkhawa ndipo abwelela naye m’sitolo kuti akabweze kadoliko ndi kuti akapepese. Pamene abwelela m’sitolo, amai ake asangalala kwambili mumtima mwao. Cifukwa ciani?

2 Makolo amasangalala kwambili akaona ana ao akuphunzila khalidwe loona mtima. Nayenso Atate wathu wakumwamba amasangalala cifukwa cakuti iye ndi “Mulungu wacoonadi.” (Salimo 31:5) Pamene tipita patsogolo kuuzimu, iye amasangalala akaona kuti tikuyesetsa kukhala oona mtima. Popeza kuti timafuna kukondweletsa Yehova ndi kukhalabe m’cikondi cake, maganizo athu amagwilizana ndi mau a mtumwi Paulo akuti: “Tikufuna kucita zinthu zonse moona mtima.” (Aheberi 13:18) Tiyeni tikambitsilane mbali zinai zofunika kwambili pa umoyo wathu, zimene zingapangitse kuti kukhala woona mtima kukhale kovuta. Ndiyeno, tidzakambitsilana mapindu ena amene timapeza tikakhala oona mtima.

DZIPENDENI MOONA MTIMA

3-5. (a) Kodi Mau a Mulungu amaticenjeza bwanji za kuopsa kodzinamiza? (b) Ndipo n’ciani cingatithandize kudzifufuza moona mtima?

3 Vuto lathu loyamba ndi kulephela kudzipenda moona mtima. Ife anthu opanda ungwilo, n’zosavuta kudzinamiza. Mwacitsanzo, Yesu anauza Akristu a ku Laodikaya kuti anali kudzinamiza kuti anali olemela, pamene m’ceniceni anali ‘osauka, akhungu, ndi amalisece’ mwakuuzimu. Iwo anali mu mkhalidwe womvetsa cisoni. (Chivumbulutso 3:17) Kudzinamiza kumeneko kunawaika pangozi yoopsa.

4 Mwina inunso mukumbukila kuti wophunzila Yakobo anacenjeza kuti: “Ngati munthu akudziona ngati wopembedza, koma salamulila lilime lake, ndipo akupitiliza kunyenga mtima wake, kupembedza kwa munthu ameneyu n’kopanda pake.” (Yakobo 1:26) Ngati timaganiza kuti Yehova amavomeleza kulambila kwathu ngakhale pamene tigwilitsila nchito lilime lathu molakwika, ndiye kuti timadzinamiza. Kulambila kwathu Yehova kungakhale kopanda phindu. N’ciani cingatithandize kupewa vuto limeneli?

5 M’lemba limodzimodzili, Yakobo anayelekezela coonadi ca mau a Mulungu ndi galasi. Anatilangiza kuti tiziyang’ana m’lamulo langwilo la Mulungu ndi kupanga masinthidwe oyenelela. (Ŵelengani Yakobo 1:23-25.) Baibulo lingatithandize kudzipenda moona mtima ndi kuona zimene tiyenela kucita kuti tiongolele. (Maliro 3:40; Hagai 1:5) Ndiponso tingapemphe Yehova kuti atifufuze ndi kutithandiza kuona ngati tili ndi makhalidwe ena oipa ndi kuti tisinthe. (Salimo 139:23, 24) Kusaona mtima ndi khalidwe lovuta kulizindikila, ndipo tifunika kuliona mmene Atate wathu wakumwamba amalionela. Lemba la Miyambo 3:32 limati: “Munthu wocita zaciphamaso Yehova amanyansidwa naye, koma amakonda anthu oongoka mtima.” Yehova angatithandize kuti tiziona zinthu mmene iye amazionela ndi kuti tizidziona mmene iye amationela. Kumbukilani kuti Paulo anati: “Tikufuna kucita zinthu zonse moona mtima.” Pakali pano ndife opanda ungwilo, koma timayesetsa kucita zinthu moona mtima.

KUKHALA OONA MTIMA M’BANJA

Kukhala oona mtima kumatithandiza kupewa kucita zinthu mwakabisila

6. N’cifukwa ciani anthu okwatilana ayenela kukhala oona mtima kwa wina ndi mnzake? Ndipo akatelo amapewa makhalidwe oipa ati?

6 Banja lacikristu liyenela kudziŵika ndi khalidwe la kuona mtima. Motelo, mwamuna ndi mkazi wake ayenela kukhala omasukilana ndi kukambitsilana zinthu moona mtima. Akristu okwatila sayenela kukhala ndi makhalidwe oipa ndi odetsa monga kuceza kokopana ndi mwamuna kapena mkazi wina, kukhala ndi cisumbali camseli pa Intaneti, kapena kupenyelela zamalisece mwa njila iliyonse. Akristu ena okwatila amacita zinthu zoipa zimenezi mwakabisila. Kucita zimenezo ndi kusaona mtima. Onani mau a mfumu yokhulupilika Davide akuti: “Sindinakhale pansi pamodzi ndi anthu acinyengo. Ndipo sindinayanjane ndi anthu obisa umunthu wao.” (Salimo 26:4) Ngati ndinu wokwatila, pewani kucita zinthu zimene zingakupangitseni kubisa khalidwe lanu.

7, 8. Ndi zitsanzo za m’Baibulo ziti zimene zingathandize ana kuphunzila kufunika kokhala oona mtima?

7 Makolo angacite bwino kugwilitsila nchito zitsanzo za m’Baibulo pophunzitsa ana ao kufunika kokhala oona mtima. Pankhani za anthu osaona mtima, pali ya Akani, amene anaba zinthu ndi kuyesa kuzibisa, Gehazi amene ananama bodza kuti apatsidwe cuma, ndi Yudasi amene anaba ndi kunama bodza kuti aike Yesu m’mavuto.—Yoswa 6:17-19; 7:11-25; 2 Mafumu 5:14-16, 20-27; Mateyu 26:14, 15; Yohane 12:6.

8 Pa zitsanzo za anthu oona mtima, pali nkhani ya Yakobo amene anauza ana ake kuti akabweze ndalama zimene anapeza m’matumba ao, cifukwa anaganiza kuti zinaikidwa mmenemo mwangozi. Palinso nkhani ya Yefita ndi mwana wake wamkazi. Mwana wakeyo anagwilizana ndi zimene atate ake analumbila kwa Yehova ngakhale kuti zinali zovuta kwambili. Nkhani ina ndi ya Yesu amene molimba mtima anadzidziŵikitsa kwa anthu amene anali kufuna kumupha. Anacita zimenezi kuti akwanilitse ulosi ndi kuti ateteze mabwenzi ake. (Genesis 43:12; Oweruza 11:30-40; Yohane 18:3-11) Zitsanzo zocepa zimenezi zingathandize makolo kudziŵa mfundo zamtengo wapatali zopezeka m’Mau a Mulungu. Izi zingawathandize kuphunzitsa ana ao kukhala oona mtima ndi kuona kuti khalidwe limeneli n’lofunika kwambili.

9. N’ciani cimene makolo ayenela kupewa kuti apeleke citsanzo cabwino kwa ana ao pankhani ya kukhala oona mtima? Ndipo n’cifukwa ciani citsanzo cimeneco ndi cofunika?

9 Makolo ali ndi udindo waukulu wophunzitsa ana kukhala oona mtima. Mtumwi Paulo anafunsa kuti: “Kodi iwe wophunzitsa enawe, sudziphunzitsa wekha? Iwe amene umalalikila kuti ‘Usabe,’ umabanso kodi?” (Aroma 2:21) Makolo ena amasokoneza ana ao mwa kuwaphunzitsa kuti azikhala oona mtima pamene io amacita zinthu mosaona mtima. Makolowo angabe zinthu zing’onozing’ono, ndiyeno angakambe modzikhululukila kuti “Abwana amadziŵa kuti anthu amatenga zinthu zimenezi” kapena anganame bodza ndi kunena kuti “Palibe vuto. Nthawi zina bodza limapulumutsa.” Koma m’ceniceni, kuba ndi kuba ndithu, mosasamala kanthu za kucepa kwa cinthu cimene cabedwa. Ndipo kunama ndi kunama ndithu, ngakhale nkhaniyo ndi yaing’ono bwanji. * (Ŵelengani Luka 16:10.) Ana amadziŵa mwamsanga ngati makolo ao acita zinthu mosaona mtima. Ndipo zimenezi zingapangitse kuti akhale osaona mtima. (Aefeso 6:4) Koma ana akaphunzila kukhala oona mtima monga makolo ao, angakule bwino ndi kulemekeza Yehova m’dziko lino losaona mtima.—Miyambo 22:6.

KUKHALA OONA MTIMA MUMPINGO

10. Ponena za kulankhula moona mtima pamene tili ndi okhulupilila anzathu, kodi tifunika kusamala za ciani?

10 Kusonkhana ndi Akritsu anzathu kumatipatsa mipata yambili yokhala oona mtima. Monga mmene tinaphunzilila m’Nkhani 12, tiyenela kusamala mmene timagwilitsilila nchito mphatso ya kulankhula, makamaka pamene tili ndi abale ndi alongo athu. Kuceza kwathu nthawi zina kungasinthe ndi kukhala mijedo yovulaza, ngakhale misece kumene. Ngati tiuza ena za nkhani imene sitiidziŵa bwinobwino, tingathandizile kufalitsa mabodza. Conco n’kofunika kwambili kulamulila milomo yathu. (Miyambo 10:19) Nthawi zina, tingadziŵe kuti nkhani inayake ndi yoona, koma zimenezo sizitanthauza kuti tifunika kuyamba kuuzako ena. Mwacitsanzo, mwina nkhaniyo sitikhudza, kapena kuuzako ena kungakhale kusaganizila munthu wokhudzidwayo. (1 Atesalonika 4:11) Anthu ena amakamba zinthu zocititsa anzao manyazi, ndi kumati akukamba zinthu moona mtima. Koma mau athu ayenela kukhala acisomo ndi okoma nthawi zonse.—Ŵelengani Akolose 4:6.

11, 12. (a) Kodi ena amene acita colakwa cacikulu amaonongelatu zinthu mwa njila yotani? (b) Ndi mabodza ena ati okhudza macimo aakulu amene Satana amalimbikitsa? Ndipo tingawapewe bwanji? (c) Tingaonetse bwanji kuti ndife oona mtima ku gulu la Yehova?

11 Tifunika kukhala oona mtima kwa amene amatitsogolela mumpingo. Ena akacita colakwa cacikulu amaonongelatu zinthu mwa kubisa zolakwa zao ndi kukamba bodza akafunsidwa za nkhaniyo ndi akulu mumpingo. Anthu amenewa amayamba kukhala ndi moyo wapaŵili. Amanamizila kuti akutumikila Yehova, koma mwakabisila amacita macimo aakulu. Potsilizila pake, zimenezo zimapangitsa anthuwo kukhala ndi umoyo wacinyengo. (Salimo 12:2) Ena sauza akulu nkhani yonse. Iwo amabisa mbali zofunika kwambili. (Machitidwe 5:1-11) Nthawi zambili kusaona mtima kumeneku, kumayamba cifukwa cokhulupilila mabodza a Satana.—Onani bokosi lakuti “Mabodza a Satana Ponena za Macimo Aakulu,” patsamba 164 mpaka 165.

12 Tifunikanso kukhala oona mtima ndi gulu la Yehova polemba mafomu osiyanasiyana. Mwacitsanzo, polemba lipoti la ulaliki wathu wakumunda, tiyenela kulemba zinthu zoona osati zabodza. Ngakhale polemba mafomu ofunsila utumiki winawake, sitiyenela kubisa mmene thanzi lathu lilili, kapena ciliconse conena za ife.—Ŵelengani Miyambo 6:16-19.

13. Kodi tingaonetse bwanji kuti ndife oona mtima pocita zamalonda ndi okhulupilila anzathu?

13 Kukhala oona mtima kwa okhulupilila anzathu kumaphatikizapo nkhani zamalonda. Nthawi zina abale ndi alongo angacite malonda ndi Akristu anzao. Iwo ayenela kusamala kuti asaphatikize nkhani zamalonda ndi kulambila pamene ali pa Nyumba ya Ufumu kapena muulaliki. Nthawi zina m’bale angalembe nchito m’bale wina kapena iye kulembedwa nchito ndi m’bale wina. Ngati talemba nchito abale ndi alongo, tiyenela kukhala osamala kuti tiziwacitila moona mtima, kuwapatsa malipilo ao panthawi yake, kuphatikizapo ndalama za penshoni mogwilizana ndi malamulo a boma. (1 Timoteyo 5:18; Yakobo 5:1-4) N’cimodzimodzinso ngati ndife amene tinalembedwa nchito ndi m’bale kapena mlongo. Tiyenela kugwila nchito maola onse ofunikila. (2 Atesalonika 3:10) Sitiyenela kuganiza kuti popeza amene anatilemba nchito ndi m’bale wathu wa kuuzimu, ayenela kutipatsa masiku a chuti ambili, ndalama zambili kapena zinthu zina kuposa anchito ena.—Aefeso 6:5-8.

14. Ngati Akristu acitila bizinesi pamodzi, kodi mwanzelu amasamala za ciani? Ndipo n’cifukwa ciani?

14 Nanga bwanji ngati abale agwilizana zakuti acitile bizinesi pamodzi kapena kukongoletsana ndalama? Baibulo limapeleka mfundo yothandiza pa mbali imeneyi. Muyenela kulembelana zonse pa zikalata. Mwacitsanzo, pamene Yeremiya anagula malo, analemba zikalata ziŵili ndipo zinasainidwa ndi mboni. Ndiyeno zikalatazo anazisunga bwino kuopela zamtsogolo. (Yeremiya 32:9-12; onaninso Genesis 23:16-20.) Pamene ticita malonda ndi okhulupilila anzathu, kulembelana zikalata zokonzedwa ndi kusainidwa bwino pamaso pa mboni, sikutanthauza kuti timakaikilana. Koma kucita zimenezo kumathandiza kuti pasadzakhale kusiyana maganizo, kukhumudwitsana ngakhale kukangana. Mkristu aliyense amene akucita bizinesi ndi anzake, ayenela kukumbukila kuti bizinesi yao siyenela kuononga mgwilizano ndi mtendele wa mpingo. *1 Akorinto 6:1-8.

KUKHALA OONA MTIMA M’DZIKOLI

15. Kodi Yehova amaliona bwanji khalidwe locita malonda mosaona mtima? Nanga Akristu ayenela kuliona bwanji khalidwe lofala limeneli?

15 Mkristu sayenela kukhala woona mtima mumpingo mokha. Paulo anati: “Tikufuna kucita zinthu zonse moona mtima.” (Aheberi 13:18) Pocita bizinesi m’dzikoli, Mlengi wathu amafuna kuti tizikhala oona mtima. M’buku la Miyambo lokha, muli mavesi angapo amene amanena za masikelo acinyengo. (Miyambo 11:1; 20:10, 23) M’nthawi zakale, anthu anali kugwilitsila nchito masikelo pocita malonda, kupima zinthu zimene agulitsa ndi kupima ndalama zimene alipilila katundu. Azamalonda osaona mtima anali kugwilitsila nchito masikelo aŵili, sikelo ina inali yonama kuti azibela makasitomala ao. * Yehova amadana ndi khalidwe limeneli. Kuti tikhalebe m’cikondi ca Mulungu, tiyenela kupewelatu kucita malonda mosaona mtima.

16, 17. Ndi kusaona mtima kotani kumene kwafala m’dziko masiku ano? Ndipo Akristu ndi otsimikiza mtima kucita ciani?

16 Popeza kuti wolamulila wa dziko lino ndi Satana, mpake kuti kusaona mtima kuli pali ponse. Masiku onse timayesedwa kuti ticite zinthu mwacinyengo. Anthu ena pofunsila nchito, amakonda kunama kuti amadziŵa nchito inayake, ndipo ena amapangitsa ngakhale masatifiketi abodza. Posaina mafomu a pasipoti kapena citupa, misonkho, inshuwalansi kapena mafomu okhudza zinthu zina, ena amanama kuti alandile zimene afuna. Ana a sukulu ambili amakopela pa mayeso, ndipo ngati kusukulu awauza kuti alembe cimangilizo kapena nkhani ina yake kapenanso malipoti, amafufuza pa Intaneti, kukopela zimene ena analemba ndi kunama kuti analemba okha. Ndipo anthu ena pofuna kuti apeze zimene afuna, amapeleka ziphuphu kwa a nchito a boma osaona mtima. Sitingadabwe ndi makhalidwe amenewa m’dziko limene anthu ambili ndi “odzikonda, okonda ndalama, osakonda zabwino.”—2 Timoteyo 3:1-5.

17 Akristu oona ndi otsimikiza mtima kupewa zimenezo. Nthawi zina kukhala woona mtima kumavuta cifukwa cakuti anthu osaona mtima amaoneka kuti zinthu zimawayendela bwino ndi kuti amatukuka m’dzikoli. (Salimo 73:1-8) Kumbali ina, Akristu angakhale osauka cifukwa cokhala oona mtima “mu zinthu zonse.” Kodi pali cifukwa covutikila ndi kukhala oona mtima? Inde! N’cifukwa ciani? Nanga kukhala oona mtima kumabweletsa mapindu otani?

MAPINDU AMENE TIMAPEZA TIKAKHALA OONA MTIMA

18. N’cifukwa ciani kukhala ndi mbili yakuti ndife oona mtima ndi kothandiza kwambili?

18 Ndi zinthu zocepa paumoyo wathu zimene zingapose mbili yathu yabwino monga munthu woona mtima ndi wodalilika. (Onani bokosi lakuti “ Kodi Ndinedi Woona Mtima?” Ndipo ganizilani izi: Aliyense angakhale ndi dzina labwino limeneli. Conco kukhala ndi dzina labwino sikudalila luso lanu, cuma, maonekedwe, kumene munakulila, kapena zinthu zina zimene simungasinthe. Ambili amalephela kupanga dzina labwino, ndipo ndi ocepa amene amakwanitsa. (Mika 7:2) Ena angakusekeni cifukwa cokhala woona mtima, koma ena adzayamikila kuona mtima kwanu. Ndipo cifukwa ca zimenezo adzayamba kukudalilani ndi kukupatsani ulemu. Cifukwa ca kuona mtima kwao, Mboni za Yehova zambili zapindula pa nkhani ya zacuma. Zasungabe nchito zao pamene anthu osaona mtima acotsedwa nchito, ndipo zapeza nchito pamakampani amene afuna anchito oona mtima.

19. Kodi kuona mtima kwathu kungakhudze motani cikumbumtima cathu ndi ubwenzi wathu ndi Yehova?

19 Kaya zotele zinakucitikilani nthawi ina kapena ai, mudzaona kuti kuona mtima kuli ndi mapindu ambili. Mudzakhala ndi cikumbumtima coyela. Paulo analemba kuti: “Tikukhulupilila kuti tili ndi cikumbumtima coona.” (Aheberi 13:18) Kuonjezela pamenepo, Atate wathu wakumwamba wacikondi amadziŵa kuona mtima kwanu, ndipo iye amakonda anthu oona mtima. (Ŵelengani Salimo 15:1, 2; Miyambo 22:1.) Inde, kukhala oona mtima kumakuthandizani kukhalabe m’cikondi ca Mulungu, ndipo palibe mphoto imene tingafune kuposa imeneyo. Tiyeni tikambitsilane nkhani ina yogwilizana ndi imeneyi. Nkhani imeneyo ndi yokhudza mmene Yehova amaonela nchito.

^ par. 9 Ngati wina mumpingo ali ndi khalidwe loneneza ena mabodza ndi colinga cofuna kuwaipitsila mbili, akulu mumpingo angaone ngati nkhaniyo ikufunikila komiti ya ciweluzo.

^ par. 14 Kuti mudziŵe zimene mungacite ngati bizinesi yalepheleka, onani Zakumapeto mutu wakuti “Kuthetsa Mikangano Pankhani Zamalonda.”

^ par. 15 Iwo anali kugwilitsila nchito sikelo ina pogula ndi ina pogulitsa ndi colinga cakuti apeze phindu loculuka. Anali kugwilitsilanso nchito sikelo ya ndodo yaitali kapena yolema kwambili mbali imodzi, ndi colinga cakuti azibela anthu.