Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI 12

Lankhulani Mau “Olimbikitsa”

Lankhulani Mau “Olimbikitsa”

“Mau alionse owola asatuluke pakamwa panu, koma alionse olimbikitsa.”—AEFESO 4:29.

1-3. (a) Ndi mphatso iti imene Yehova anatipatsa? Nanga munthu angaigwilitsile nchito bwanji molakwika? (b) Kodi tifunika kugwilitsila nchito bwanji mphatso ya kulankhula kuti tikhalebe m’cikondi ca Mulungu?

NGATI munapatsa mphatso munthu amene mumakonda, kodi mungamve bwanji ngati mwadala saigwilitsila nchito bwino? Tiyelekeze kuti munamugulila galimoto, ndipo mwadziŵa kuti amaiyendetsa mosasamala moti amagunda nayo anthu. Kodi mungamve bwanji?

2 Kulankhula ndi mphatso yamtengo wapatali yocokela kwa Yehova, Mpatsi wa “mphatso iliyonse yabwino ndi yangwilo.” (Yakobo 1:17) Mphatso imeneyi imatithandiza kufotokozela anthu ena maganizo athu ndi mmene tikumvelela, ndipo imatisiyanitsa ndi nyama. Komabe, mofanana ndi galimoto, munthu angaigwilitsile nchito molakwa mphatso yolankhula. Yehova amakhumudwa kwambili ngati tivutitsa ena kapena kuwakwiitsa cifukwa colankhula mosasamala.

3 Kuti tikhalebe m’cikondi ca Mulungu, tiyenela kugwilitsila nchito mphatso ya kulankhula m’njila imene Mpatsi wa mphatsoyi amafunila. Yehova amafotokoza momveka bwino kalankhulidwe kamene amakondwela nako. Mau ake amati: “Mau alionse owola asatuluke pakamwa panu, koma alionse olimbikitsa monga mmene kungafunikile, kuti asangalatse owamva.” (Aefeso 4:29) Tiyeni tikambilane cifukwa cake tiyenela kusamala ndi kalankhulidwe kathu. Tikambilananso za kalankhulidwe kamene tiyenela kupewa ndiponso mmene tingalankhulile mau “olimbikitsa.”

CIFUKWA CAKE TIYENELA KUSAMALA NDI KALANKHULIDWE KATHU

4, 5. Kodi miyambi ina ya m’Baibulo imafotokoza kuti mau ali ndi mphamvu yotani?

4 Cifukwa cacikulu cimene tiyenela kusamala ndi kalankhulidwe kathu n’cakuti mau ali ndi mphamvu. Lemba la Miyambo 15:4 limati: “Lilime lodekha lili ngati mtengo wa moyo, koma lilime lacinyengo limapweteketsa mtima.” * Monga mmene madzi amatsitsimulila mtengo wofota, naonso mau odekha amatsitsimula anthu owamva. Mosiyana ndi zimenezi, mau oipa a lilime lokhota angaononge mzimu wa anthu ena. Ndithudi, mau amene timakamba ali ndi mphamvu yovulaza kapena kucilitsa.—Miyambo 18:21.

5 Mwambi wina umafotokoza bwino za mphamvu ya mau kuti: “Pali munthu amene amalankhula mosaganizila ndi mau olasa ngati lupanga.” (Miyambo 12:18) Ngati tilankhula mosasamala, tingakhumudwitse ena ndi kubweletsa cidani. Kodi munthu anakulasamponi ndi mau akuthwa ngati lupanga? Mwambi umenewu umanenanso za ubwino wa lilime kuti: “Lilime la anthu anzelu limacilitsa.” Mau abwino okambidwa ndi munthu woopa Mulungu amene amaganizila ena angacilitse mtima wosweka ndi kukonzanso ubwenzi. Kodi mungakumbukile nthawi ina pamene munalimbikitsidwa ndi mau abwino? (Ŵelengani Miyambo 16:24.) Kukumbukila kuti zimene timakamba zimakhudza ena, kudzatithandiza kusamala kalankhulidwe kathu kuti tisawavulaze.

Mau abwino amatsitsimula

6. N’cifukwa ciani kulamulila lilime lathu ndi kovuta?

6 Ngakhale tiyesetse bwanji, sitingathe kulamulila kothelatu lilime lathu. Cifukwa caciŵili cimene tiyenela kusamala ndi kalankhulidwe kathu n’cakuti ucimo ndi kupanda ungwilo zimacititsa kuti tizivutika kugwilitsila nchito bwino lilime lathu. Mau athu amacokela mumtima, ndipo ‘maganizo a anthu ndi oipa.’ (Genesis 8:21; Luka 6:45) Conco, kulamulila lilime lathu ndi kovuta. (Ŵelengani Yakobo 3:2-4.) Ngakhale kuti sitingathe kulamulila lilime lathu kothelatu, tikhoza kuongolela mmene timaligwilitsilila nchito. Ngati munthu afuna kuoloka mtsinje wamphamvu ayenela kusambila zolimba kuti asakokoloke ndi madzi. Mofananamo, tiyenela kuyesetsa kulimbana ndi cizoloŵezi ca ucimo cofuna kulankhula zinthu zoipa.

7, 8. Kodi Yehova angatiimbe mlandu waukulu bwanji ngati tilankhula mau oipa?

7 Cifukwa cacitatu cimene tiyenela kusamala ndi kalankhulidwe kathu n’cakuti Yehova adzatiimba mlandu cifukwa ca mau athu. Mmene timagwilitsilila nchito lilime lathu zimakhudza ubwenzi wathu ndi ena ndiponso ubwenzi wathu ndi Yehova. Lemba la Yakobo 1:26 limati: “Ngati munthu akudziona ngati wopembedza, koma salamulila lilime lake, ndipo akupitiliza kunyenga mtima wake, kupembedza kwa munthu ameneyu n’kopanda pake.” * Monga momwe tinaphunzilila m’nkhani yapita, kalankhulidwe kathu kamagwilizana kwambili ndi kulambila kwathu. Ngati sitilamulila lilime lathu ndipo timalankhula mau okhumudwitsa ndi oipa, nchito zathu zonse zacikristu zimakhala zopanda phindu kwa Mulungu. Conco, kodi si koyenela kuti tizilamulila lilime lathu?—Yakobo 3:8-10.

8 Motelo, tili ndi zifukwa zomveka zopewela kugwilitsila nchito molakwa mphatso ya kulankhula. Tisanakambilane za kalankhulidwe kolimbikitsa, tiyeni tikambilane za kalankhulidwe kamene Akristu oona ayenela kupewa.

KALANKHULIDWE KOVULAZA

9, 10. (a) Kodi masiku ano anthu amakonda kulankhula mau otani? (b) N’cifukwa ciani tiyenela kupewa kulankhula mau otukwana? (Onani mau a munsi.)

9 Mau otukwana. Masiku ano, anthu amakonda kukamba mau otukwana ndi onyoza ndi mau ena oipa. Ambili amatukwana pofuna kugogomeza nkhani kapena cifukwa cosoŵa mau akuti akambe pofotokoza zinthu. Ocita maseŵelo a nthabwala nthawi zambili amatukwana kapena kukamba zinthu zosayenela zokhudza kugonana kuti aseketse anthu. Koma kutukwana ndi nkhani yaikulu. Zaka 2,000 zapitazo, mtumwi Paulo analangiza mpingo wa ku Kolose kuti aleke kulankhula “nkhani zotukwana.” (Akolose 3:8) Paulo anauza mpingo wa Aefeso kuti “nthabwala zotukwana,” ndi cimodzi mwa zinthu zimene siziyenela ‘kuchulidwa n’komwe pakati’ pa Akristu oona.—Aefeso 5:3, 4.

10 Yehova amanyansidwa ndi kutukwana. Anthu amene amakonda Mulungu naonso amanyansidwa ndi khalidwe limeneli. Ndithudi, kukonda kwathu Yehova kumatilimbikitsa kupewa kutukwana. Pofotokoza “nchito za thupi,” Paulo anachula “zinthu zodetsa” zimene zimaphatikizapo kulankhula mau onyansa. (Agalatiya 5:19-21) Imeneyi ndi nkhani yaikulu. Munthu angacotsedwe mumpingo ngati samvela uphungu umene wapatsidwa mobwelezabweleza, ndiponso ngati mosalapa apitiliza kulankhula mau oipa kwambili, ocititsa manyazi, kapena onyansa. *

11, 12. (a) Kodi kujeda ndi kutani? Ndipo kungakhale bwanji kovulaza? (b) N’cifukwa ciani olambila Yehova ayenela kupewa misece?

11 Mijedo yovulaza, misece. Kujeda kumatanthauza kulankhula za anthu ena ndi umoyo wao. Koma kodi kulankhula za anthu ena ndi kulakwa? Iyai, makamaka ngati zimene tikamba ndi zinthu zabwino, ndi zothandiza, monga za amene anabatizidwa posacedwapa kapena amene afunikila cilimbikitso. Akristu a m’nthawi ya atumwi anali ndi cidwi cofuna kudziŵa za umoyo wa ena ndi kuuzana nkhani zokhudza okhulupilila anzao. (Aefeso 6:21, 22; Akolose 4:8, 9) Komabe, mijedo ingakhale yoipa ngati munthu akamba zabodza ndi kuulula zisinsi za ena. Ndipo coipa kwambili n’cakuti mijedo imayambitsa misece, imene nthawi zonse imakhala yovulaza. Misece ndi “kunenela munthu zonama . . . zimene zimaononga mbili yake.” Mwacitsanzo, Afalisi anali kudyela Yesu misece yovulaza kuti amuwonongele mbili. (Mateyu 9:32-34; 12:22-24) Misece nthawi zambili imayambitsa mikangano.—Miyambo 26:20.

12 Yehova amakhumudwa ndi anthu amene amagwilitsila nchito mphatso yao ya kulankhula kuononga mbili ya anzao kapena kuyambitsa magaŵano. Amadana ndi anthu amene ‘amayambitsa mikangano pakati pa abale.’ (Miyambo 6:16-19) Liu la Cigiliki lakuti di·aʹbo·los, limatembenuzidwa kuti “woneneza” ndipo limeneli ndi dzina linanso la Satana. Iye ndi “Mdyelekezi” woneneza Mulungu. (Chivumbulutso 12:9, 10) Ndithudi, tiyenela kupewa kalankhulidwe kamene kangaticititse kukhala ngati Mdyelekezi. Mumpingo simuyenela kukhala anthu olankhula misece imene imasonkhezela nchito za thupi monga “mikangano” ndi “magawano.” (Agalatiya 5:19-21) Conco, musanauze munthu wina nkhani, dzifunseni kuti: ‘Kodi nkhaniyi ndi yoona? Nanga ndi cikondi kuuzako ena? Kodi n’kofunikadi kuti ndiuzeko ena nkhaniyi?—Ŵelengani 1 Atesalonika 4:11.

13, 14. (a) Kodi mau acipongwe amakhudza motani anthu owamva? (b) Kodi kulalata n’kutani? Nanga n’cifukwa ciani munthu wolalata amaika moyo wake pangozi?

13 Mau acipongwe. Monga mmene taonela kale, mau ali ndi mphamvu yovulaza. N’zoona kuti cifukwa ca kupanda ungwilo, tonse nthawi zina timakamba mau amene pambuyo pake timamva nao cisoni. Koma Baibulo limaticenjeza za kalankhulidwe kamene Akristufe tiyenela kupewa ku nyumba kapena mumpingo. Paulo anakumbutsa Akristu kuti: “Kuŵaŵidwa mtima konse kwa njilu, kupsa mtima, mkwiyo, kulalata ndiponso mau acipongwe zicotsedwe mwa inu.” (Aefeso 4:31) Ma Baibulo ena amamasulila mau akuti “mau acipongwe” kukhala “mau oipa,” “mau opweteka” ndi “mau otukwana.” Mau acipongwe monga kuchulana maina oipa, ndi kudzudzula mwaukali, amacotsela ena ulemu ndi kuwapangitsa kudzimva ngati ndi acabecabe. Ana ndi amene amavutika kwambili ndi mau acipongwe cifukwa sacedwa kukhulupilila zinthu.—Akolose 3:21.

14 Baibulo limagwilitsila nchito mau amphamvu poletsa kulalata. Kulalata ndi khalidwe lonyoza ena ndi mau otukwana, oseleula, kapena acipongwe. Munthu amene amakonda kulalata amadziika pangozi, cifukwa akhoza kucotsedwa mumpingo ngati samvela pambuyo popatsidwa uphungu mobwelezabweleza. Ngati sasintha, akhoza kutaya mwai wolandila madalitso a Ufumu. (1 Akorinto 5:11-13; 6:9, 10) Conco, n’zoonekelatu kuti ngati tipitiliza kulankhula mau oipa, abodza, kapena osaganizila ena, n’zosatheka kukhalabe m’cikondi ca Mulungu. Mau otelo amavulaza.

MAU “OLIMBIKITSA”

15. Kodi ndi mau otani amene ‘amalimbikitsa’?

15 Tingagwilitsile nchito bwanji mphatso ya kulankhula monga mmene Mpatsi wa mphatsoyi amafunila? Kumbukilani kuti Mau a Mulungu amatilimbikitsa kulankhula mau alionse “olimbikitsa.” (Aefeso 4:29) Yehova amasangalala ngati tilankhula mau olimbikitsa ena. Pamafunika kulingalila bwino kuti tilankhule mau aconco. M’Baibulo mulibe malamulo acindunji a mmene tiyenela kulankhulila kapena mndandanda wa ‘mau oyenelela’ amene tiyenela kulankhula. (Tito 2:8) Kuti tilankhule mau “olimbikitsa,” ndi bwino kukumbukila kuti mau olimbikitsa amakhala oyenelela, oona, ndi acifundo. Tili ndi mfundo zitatu zimenezi m’maganizo athu, tiyeni tikambilane zitsanzo zitatu za kalankhulidwe kolimbikitsa.—Onani bokosi lakuti “ Kodi Ndimalankhula Molimbikitsa?

16, 17. (a) N’cifukwa ciani tiyenela kuyamikila ena? (b) Ndi mipata yotani imene timakhala nayo mumpingo yoyamikila ena? Nanga bwanji m’banja?

16 Kuyamikila ena mocokela pansi pa mtima. Yehova ndi Yesu amaona kuti kulankhula mau olimbikitsa n’kofunika kwambili. (Mateyu 3:17; 25:19-23; Yohane 1:47) Ifenso monga Akristu tiyenela kuyamikila ena mocokela pansi pa mtima. Cifukwa ciani? Lemba la Miyambo 15:23 limati: “Mau onenedwa pa nthawi yoyenela ndi abwino kwambili.” Dzifunseni kuti: ‘Ndimamva bwanji ena akandiyamikila mocokela pansi pa mtima? Kodi ndimakondwela ndi kulimbikitsidwa?’ Ndithudi, mau olimbikitsa amaticititsa kumva kuti anthu ena amaona zocita zathu, amatiganizila, ndi kuti khama lathu silinapite pacabe. Mau aconco amatilimbikitsa kuti tipitilize kucita zinthu mwakhama. Popeza kuti mukalimbikitsidwa ndi munthu wina mumasangalala, kodi inunso simuyenela kucita zonse zimene mungathe kulimbikitsa ena?—Ŵelengani Mateyu 7:12.

17 Phunzilani kuona zabwino mwa ena, ndipo ayamikileni. Kumisonkhano ya mpingo, mungamve nkhani yolimbikitsa, mungaone wacinyamata amene akupita patsogolo kuuzimu, kapena wacikulile amene amabwela ku misonkhano mokhulupilika mosasamala kanthu ndi mavuto aukalamba. Kuyamikila anthu otelo mocokela pansi pa mtima kungawakhudze mtima ndi kuwalimbikitsa mwakuuzimu. M’banja, mwamuna ndi mkazi ayenela kuyamikilana mocokela pansi pa mtima nthawi zonse. (Miyambo 31:10, 28) Makamaka ana amakula bwino akadziŵa kuti ndi ofunika. Kuyamikila ndi kulimbikitsa mwana kumapangitsa kuti akule bwino monga mmene madzi ndi dzuŵa zimathandizila mtengo kukula bwino. Makolo, muzifunafuna mipata yoyamikila ana anu cifukwa ca khalidwe lao labwino ndi khama lao. Zimenezi zimapangitsa anao kukhala olimba mtima ndiponso zimawapatsa cidalilo cakuti apitilize kuyesetsa kucita zabwino.

18, 19. N’cifukwa n’ciani tiyenela kuyesetsa kulimbikitsa ndi kutonthoza okhulupilila anzathu? Nanga tingacite bwanji zimenezo?

18 Kulimbikitsa ena ndi kuwatonthoza. Yehova amasamalila kwambili “anthu onyozeka” ndi “opsinjika.” (Yesaya 57:15) Mau ake amatilimbikitsa kuti “pitilizani kutonthozana” ndipo “lankhulani molimbikitsa kwa amtima wacisoni.” (1 Atesalonika 5:11, 14) Ndife otsimikiza kuti Mulungu amaona ndi kuyamikila khama lathu polimbikitsa ndi kutonthoza okhulupilila anzathu amene ali ndi cisoni.

Yehova amakondwela ngati tikamba mau olimbikitsa ena

19 Nanga mungakambe ciani kuti mulimbikitse Mkristu mnzanu amene walefuka ndi kupsinjika maganizo? Musaone kuti muyenela kuthetsa vutolo. Nthawi zambili kungokamba tumau tolimbikitsa n’kothandiza. Tsimikizilani munthu wosweka mtimayo kuti mumam’konda. Mungapemphele naye mokweza mau. Mungapemphe Yehova kuti amuthandize kudziŵa kuti anthu ena ndiponso Mulungu amamukonda kwambili. (Yakobo 5:14, 15) M’tsimikizileni kuti anthu a mumpingo amamuona kuti ndi wofunika ndipo amamukonda. (1 Akorinto 12:12-26) Mukhoza kuŵelenga naye lemba limodzi m’Baibulo kuti mumutsimikizile kuti Yehova amam’konda. (Salimo 34:18; Mateyu 10:29-31) Pezani nthawi yokwanila yolankhula “mau abwino” kwa wosweka mtima. Kumulimbikitsa kucokela pansi pa mtima kudzam’thandiza kuona kuti ndi wofunika ndipo mumam’konda.—Ŵelengani Miyambo 12:25.

20, 21. N’ciani cimacititsa uphungu kukhala wabwino?

20 Uphungu wogwila mtima. Pokhala anthu opanda ungwilo, nthawi ndi nthawi tonse timafunikila uphungu. Baibulo limatilimbikitsa kuti: “Mvela uphungu ndipo utsatile malangizo kuti udzakhale wanzelu m’tsogolo.” (Miyambo 19:20) Kupeleka uphungu si nchito ya akulu okha. Makolo amapeleka uphungu kwa ana. (Aefeso 6:4) Alongo acikulile ayenela kupeleka uphungu kwa alongo acitsikana. (Tito 2:3-5) Kukonda anthu ena kumatilimbikitsa kuwapatsa uphungu m’njila imene sangakhumudwe nao. N’ciani cingatithandize kupeleka uphungu wotelo? Tiyeni tione mfundo zitatu zimene zimapangitsa uphungu kukhala wogwila mtima. Mfundo zitatu zimenezo ndi izi: Maganizo ndi zolinga za wopeleka uphunguyo, cifukwa coupelekela, ndi mmene uphunguwo aupelekela.

21 Kuti uphungu ukhale wogwila mtima zimadalila munthu woupelekayo. Dzifunseni kuti, ‘Kodi n’ciani cimene cimandithandiza kulandila uphungu mosavuta?’ Mukadziŵa kuti munthu amene wapeleka uphungu amakukondani, sakulankhula cifukwa cakuti wakwiya, ndipo alibe zolinga zolakwika, uphunguwo suvuta kuulandila. Conco, ifenso tiyenela kupeleka uphungu kwa ena mwanjila imeneyi. Ndipo uphungu wabwino umacokela m’Mau a Mulungu. (2 Timoteyo 3:16) Kaya uphungu wathu wacokela m’Baibulo mwacindunji kapena ai, Malemba ndiwo ayenela kukhala maziko a uphunguwo. Conco, akulu ayenela kusamala kuti asaumilize ena kutsatila malingalilo ao, kapena kupotoza Malemba ndi colinga cakuti uphungu wao uoneke ngati ucokela m’Baibulo. Uphungu umalandilidwa ngati wapelekedwa m’njila yoyenela. Uphungu wopelekedwa mokoma mtima suvuta kulandila ndipo sucotsela ulemu munthu amene akuulandilayo.—Akolose 4:6.

22. Kodi mwatsimikiza mtima kugwilitsila nchito bwanji mphatso yanu ya kulankhula?

22 Zoonadi, kulankhula ndi mphatso yamtengo  wapatali yocokela kwa Mulungu. Kukonda kwathu Yehova kuyenela kutilimbikitsa kugwilitsila nchito bwino mphatso imeneyi. Ndipo tizikumbukila kuti zimene timakamba zili ndi  mphamvu yomanga kapena yopasula. Conco, tiyeni  tiyesetse kugwilitsila nchito mphatso imeneyi “kulimbikitsa” ena, monga mmene Mpatsi wa mphatsoyi amafunila. Tikatelo, mau athu adzakhala olimbikitsa ndi otsitsimula kwa ena, ndipo adzatithandiza kukhalabe m’cikondi ca Mulungu.

^ par. 4 Liu la Ciheberi lotembenuzidwa kuti “cinyengo” pa Miyambo 15:4 lingatanthauzenso “kupotoka.”

^ par. 7 Liu la Cigiriki lotembenuzidwa kuti “kupanda pake” limamasulidwanso kuti “cacabecabe” kapena “copanda phindu.”—1 Akorinto 15:17.

^ par. 10 M’Malemba, mau akuti “zinthu zodetsa” amaphatikizapo macimo ambili. Ngakhale kuti si zodetsa zonse zimene zimafunikila komiti ya ciweluzo, munthu angacotsedwe mumpingo ngati mosalapa apitiliza kucita khalidwe lodetsa kwambili.2 Akorinto 12:21; Aefeso 4:19; onani “Mafunso Ocokela kwa Owelenga” mu Nsanja ya Olonda ya July 15, 2006.