ZAKUMAPETO
Ndi Liti Pamene Mlongo Ayenela Kuvala Cophimba Kumutu, Ndipo N’cifukwa Ciani?
Pa nkhani ya kulambila, ndi liti pamene mlongo afunikila kuvala cophimba kumutu, ndipo n’cifukwa ciani afunika kucita zimenezo? Tiyeni tikambilane zimene mtumwi Paulo anauzilidwa kulemba pa nkhani imeneyi. Iye anapeleka malangizo amene angatithandize kupanga zosankha zoyenela zimene zingalemekeze Mulungu. (1 Akorinto 11:3-16) Paulo anachula zinthu zitatu zimene tiyenela kuzilingalila: (1) zocitika zimene zingafune kuti mkazi avale cophimba kumutu, (2) malo amene iye ayenela kucitila zimenezo, ndi (3) zifukwa zimene ayenela kutsatilila malangizo amenewa.
Zocitika. Paulo anachula zocitika ziŵili: Kupemphela ndi kunenela. (Vesi 4 ndi 5) Pemphelo ndi kulankhula ndi Yehova. Masiku ano kunenela kungatanthauze nchito iliyonse yophunzitsa Baibulo imene Mkristu amacita. Koma kodi Paulo anali kutanthauza kuti mkazi ayenela kuvala cinacake kumutu nthawi zonse akamapemphela kapena kuphunzitsa Baibulo? Ai. Malo amene iye akupemphelela kapena kuphunzitsila ndi amene angaonetse ngati afunikila kuvala cophimba kumutu kapena ai.
Malo. Mau a Paulo amaonetsa kuti pali malo aŵili kumene mlongo angavale cophimba kumutu. Malo amenewo ndi m’banja ndi mumpingo. Iye anati: “Mutu wa mkazi ndi mwamuna . . . Mkazi aliyense amene akupemphela kapena kunenela osavala Vesi 3 ndi 5) M’banja, Yehova anaika mwamuna kukhala mutu wa mkazi. Ngati mkazi salemekeza ulamulilo wa mwamuna wake mwa kutenga maudindo amene Yehova anapatsa mwamunayo, angacititse mwamunayo manyazi. Mwacitsanzo, ngati afunikila kutsogoza phunzilo la Baibulo ali ndi mwamuna wake, angaonetse kuti amalemekeza ulamulilo wa mwamunayo mwa kuvala cophimba kumutu. Iye ayenela kucita zimenezo kaya mwamunayo ndi wobatizika kapena ai, cifukwa mwamuna ndi mutu wa banja. * Ngati angafunikile kupemphela kapena kuphunzitsa ali pamodzi ndi mwana wake wamng’ono wamwamuna amene ndi wobatizika, ayenelanso kuvala cophimba kumutu. Ayenela kucita zimenezo osati cifukwa cakuti mwanayo ndi mutu wa banja, koma cifukwa ca ulamulilo umene amuna obatizika ali nao mumpingo wacikristu.
kanthu kumutu akucititsa manyazi mutu wake.” (Pofotokoza za mumpingo, Paulo anati: “Ngati alipo wina amene akuoneka kuti akutsutsa zimenezi pofuna cikhalidwe cina, ifeyo, monganso mipingo ya Mulungu, tilibe cikhalidwe cinanso.” (Vesi 16) Mumpingo wacikristu, amuna obatizika ndi amene amapatsidwa udindo wotsogolela. (1 Timoteyo 2:11-14; Aheberi 13:17) Amuna okha ndi amene amaikidwa kukhala akulu ndi atumiki othandiza kuti asamalile udindo wopatsidwa ndi Mulungu woyang’anila nkhosa za Mulungu. (Machitidwe 20:28) Koma nthawi zina malinga ndi mmene zinthu zilili, mkazi wacikristu angapemphedwe kusamalila udindo umene uyenela kusamalidwa ndi mwamuna wobatizika. Mwacitsanzo, angafunikile kucititsa msonkhano wokonzekela ulaliki cifukwa cakuti palibe m’bale woyenelela kapena sanabwele. Kapena mwina mlongo angafunikile kucititsa phunzilo la Baibulo ali ndi m’bale. *Popeza kuti imeneyi ndi mbali ya nchito ya mpingo, iye ayenela kuvala cophimba kumutu pofuna kuonetsa kuti akuzindikila kuti nchitoyo ndi ya abale.
Koma pali zocitika zambili zokhudza kulambila zimene mlongo * Ngati sadziŵabe zocita, ndipo malinga ndi cikumbumtima cake aona kuti afunikila kuvala cophimba kumutu, sangalakwitse ngati angavale monga mmene cithunzithunzi cikuonetsela.
sangafunikile kuvala cophimba kumutu. Mwacitsanzo, iye sangafunikile kuvala cophimba kumutu pamene ayankhapo pa misonkhano yacikristu, pamene acita ulaliki wa khomo ndi khomo ali ndi mwamuna wake kapena m’bale wina wobatizika. Sangafunikilenso kuvala cophimba kumutu pamene aphunzitsa kapena kupemphela ndi ana ake osabatizika. Komabe, pangakhale mafunso ena okhudza nkhaniyi, ndipo ngati mlongo sadziŵa zimene angacite, angapitilize kufufuza.Zifukwa zake. Mu vesi 10 muli zifukwa ziŵili zimene mkazi wacikristu ayenela kuvalila cophimba kumutu. Vesi limeneli limati: “Mkazi ayenela kukhala ndi cizindikilo ca ulamulilo kumutu kwake cifukwa ca angelo.” Coyamba, ganizilani mau akuti “cizindikilo ca ulamulilo.” Mwa kuvala cophimba kumutu, mkazi amaonetsa kuti amazindikila ulamulilo umene Yehova anapatsa amuna obatizika mumpingo. Mwa kutelo, amaonetsa cikondi cake ndi kukhulupilika kwake kwa Yehova Mulungu. Cifukwa caciŵili ndi mau akuti “cifukwa ca angelo.” Kodi mkazi akavala cophimba kumutu zolengedwa zauzimu zamphamvu zimakhudzidwa bwanji?
Angelo amasangalala akaona kuti ulamulilo wa Mulungu ukulemekezedwa m’gulu lonse la Yehova, kumwamba ndi padziko lapansi. Iwo amasangalalanso akaona zimene anthu opanda ungwilo amacita pa nkhani imeneyi. Ndipo angelo naonso ayenela kugonjela ulamulilo wa Yehova. Zimenezi ndi zimene angelo ena analephela kucita m’mbuyomu. (Yuda 6) Angelo amasangalala akaona mlongo waluso, wacidziŵitso ndi wanzelu kuposa m’bale mumpingo akugonjela ulamulilo wa m’baleyo ndi mtima wonse. Nthawi zina, mlongo angakhale kuti ndi wodzozedwa ndipo adzalamulila ndi Yesu. Mlongo ameneyo adzakhala ndi udindo wapamwamba kuposa umene angelo ali nao, ndipo adzalamulila ndi Kristu kumwamba. Cimeneci ndi citsanzo cabwino kwambili kwa angelo! Inde, alongo onse ali ndi mwai wapadela woonetsa kuti ndi odzicepetsa ndipo amamvela mwa kukhala okhulupilika ndi ogonjela pamaso pa angelo ambili okhulupilika.
^ par. 3 Mkazi wacikristu sayenela kupemphela mokweza mau pamene mwamuna wake wobatizika ali pafupi. Koma angacite conco ngati pali zifukwa zina monga pamene mwamunayo sakwanitsa kukamba cifukwa codwala.
^ par. 1 Mlongo sangafunikile kuvala cophimba kumutu pamene akucititsa phunzilo la Baibulo ali ndi m’bale wosabatizidwa amene si mwamuna wake.
^ par. 2 Kuti mudziŵe zambili, onani Nsanja ya Mlonda ya February 15, 2015, tsamba 30, Nsanja ya Olonda ya July 15, 2002, patsamba 26 mpaka 27, ndi ya Cingelezi ya February 15, 1977, patsamba 125 mpaka 128.