NKHANI 5
Mmene Tingakhalile Olekana ndi Dziko
“Simuli mbali ya dziko.” —YOHANE 15:19.
1. Kodi Yesu anagogomeza za ciani pa usiku wake wotsiliza padziko lapansi?
USIKU wake womaliza kukhala padziko lino lapansi, Yesu anaonetsa kuti anali ndi nkhawa yaikulu ponena za zimene zidzacitikila ophunzila ake mtsogolo. Yesu anacita kuipemphelela nkhaniyi kwa Atate ake. Iye anati: “Sindikupempha kuti muwacotse m’dziko, koma kuti muwayang’anile kuopela woipayo. Iwo sali mbali ya dziko, monganso ine sindili mbali ya dziko.” (Yohane 17:15, 16) M’pemphelo limeneli locokela pansi pa mtima, Yesu anaonetsa kuti anali kukonda kwambili otsatila ake. Ndipo anaonetsanso kufunika kwa mau amenewa pamene anauza ena a ophunzila ake kuti: “Simuli mbali ya dzikoli.” (Yohane 15:19) Zimenezi zinaonetsadi kuti Yesu sanali kufuna otsatila ake kukhala mbali ya dziko.
2. Kodi “dziko” limene Yesu anachula n’ciani?
2 “Dziko” limene Yesu anachula limatanthauza anthu onse otalikilana ndi Mulungu, amene akulamulidwa ndi Satana, amenenso ndi akapolo a mzimu wodzikonda ndi wonyada wa Satana. (Yohane 14:30; Aefeso 2:2; 1 Yohane 5:19) Ndithudi, kukhala pa “ubwenzi ndi dziko n’kudziika pa udani ndi Mulungu.” (Yakobo 4:4) Nanga zingatheke bwanji kuti anthu onse ofuna kukhalabe m’cikondi ca Mulungu akhale m’dziko koma osakhala mbali ya dzikoli? Tidzakambilana njila zisanu izi: kukhala okhulupilika ku Ufumu wa Mulungu umene uli m’manja mwa Kristu ndi kusatenga mbali pa ndale za dziko, kupewa mzimu wa dziko, kuvala ndi kudzikonza mwaulemu, kukhala ndi diso lolunjika pa cinthu cimodzi, ndiponso kuvala zida zathu zonse zankhondo zocokela kwa Mulungu.
KUKHALA OKHULUPILIKA NDI KUSATENGA MBALI PA ZANDALE
3. (a) Kodi Yesu anaziona bwanji ndale za m’nthawi yake? (b) N’cifukwa ciani tinganene kuti otsatila a Yesu odzozedwa amatumikila monga akazembe? (Onani mau a munsi.)
3 Pamene anali padziko lapansi, Yesu sanali kutenga mbali m’ndale. Koma anaika maganizo ake pa nchito yolalikila za Ufumu wa Mulungu, umene ndi boma lakumwamba limene iye anali kudzalamulila monga Mfumu. (Danieli 7:13, 14; Luka 4:43; 17:20, 21) Conco, pamene anapita kukaonekela pamaso pa Bwanamkubwa waciroma, Pontiyo Pilato, Yesu anati: “Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino.” (Yohane 18:36) Otsatila ake okhulupilika amatengela citsanzo cake mwa kukhala okhulupilika kwa Kristu ndi Ufumu wake, ndi kulalikila za Ufumu umenewo padziko lapansi. (Mateyu 24:14) Mtumwi Paulo analemba kuti: “Cotelo ndife akazembe m’malo mwa Kristu, . . . Monga okhala m’malo mwa Kristu tikupempha kuti: ‘Gwilizananinso ndi Mulungu.’” *—2 Akorinto 5:20.
4. Kodi Akristu onse oona aonetsa bwanji kuti ndi okhulupilika ku Ufumu wa Mulungu? (Onani bokosi lakuti “ Akristu Oyambilila Sanali Kutenga Mbali M’ndale.”)
4 Popeza akazembe amaimila dziko lina, io saloŵelela m’ndale za m’maiko amene akutumikilamo. Komabe, akazembe amacilikiza boma limene amaimila. N’cimodzimodzi ndi otsatila a Kristu odzozedwa, amene ndi “nzika zakumwamba.” (Afilipi 3:20) Ndipo cifukwa colalikila Ufumu mokangalika, io athandiza mamiliyoni a “nkhosa zina” kuti ‘ayanjanitsidwe ndi Mulungu.’ (Yohane 10:16; Mateyu 25:31-40) Akristu a nkhosa zina amatumikila monga nthumwi za Kristu, pocilikiza abale a Kristu odzozedwa. Magulu onse aŵili amagwilizana pocilikiza Ufumu wa Mesiya, ndipo onse satenga mbali m’ndale.—Ŵelengani Yesaya 2:2-4.
5. Kodi mpingo wacikristu umasiyana bwanji ndi Aisiraeli akale? Ndipo kusiyana kumeneko kumaonekela bwanji?
Mateyu 28:19; 1 Petulo 2:9) Conco, ngati tingacilikize zipani zandale, tingataye ufulu wathu wa kulankhula za uthenga wa Ufumu, ndi kusokoneza mgwilizano wathu wacikristu. (1 Akorinto 1:10) Ndiponso panthawi ya nkhondo tingamamenyane ndi okhulupilila anzathu, amene timalamulidwa kuti tiziwakonda. (Yohane 13:34, 35; 1 Yohane 3:10-12) N’cifukwa cake m’pomveka kuti Yesu analetsa otsatila ake kunyamula lupanga. Anawauzanso kuti azikonda adani ao.—Mateyu 5:44; 26:52; onani kabokosi kakuti “ Kodi Ndimapewa Ndale?”
5 Kukhala okhulupilika kwa Kristu sindico cifukwa cokha cimene Akristu oona satengela mbali m’ndale. Mosiyana ndi Aisiraeli akale amene Mulungu anawapatsa dziko laolao, ife tili ndi ubale wa padziko lonse. (6. Kodi kudzipeleka kwanu kwa Mulungu kumafuna kuti muzicita ciani kwa Kaisala?
6 Monga Akristu oona, tinapeleka miyoyo yathu kwa Mulungu, osati kwa munthu aliyense, bungwe kapena dziko lililonse. Lemba la 1 Akorinto 6:19, 20 limati: “Mwiniwake wa inuyo si inu, pakuti munagulidwa pa mtengo wokwela.” Conco, pamene otsatila a Yesu amapeleka za “Kaisara” mwa kum’patsa ulemu, kulipila misonkho, ndi kumugonjela mosapitilila malile, io amapelekanso zinthu “za Mulungu kwa Mulungu.” (Maliko 12:17; Aroma 13:1-7) Izi zimaphatikizapo kum’lambila, kum’konda ndi moyo wao wonse, ndi kumumvela mokhulupilika. Pakakhala pofunika, Akristuwo amakhala okonzeka ngakhale kutaya moyo wao cifukwa ca Mulungu.—Luka 4:8; 10:27; ŵelengani Machitidwe 5:29; Aroma 14:8.
KANIZANI “MZIMU WA DZIKO”
7, 8. Kodi “mzimu wa dziko” n’ciani? Ndipo ‘ukugwila nchito’ bwanji mwa anthu osamvela?
7 Njila ina imene Akristu amakhalila olekana ndi dziko ndiyo mwa kukaniza mzimu wake woipa. Paulo analemba kuti: “Sitinalandile mzimu wa dziko, koma mzimu wocokela kwa Mulungu.” (1 Akorinto 2:12) Iye anauzanso Akristu a ku Aefeso kuti: “Munali kuyenda m’zimenezo mogwilizana ndi nthawi za m’dzikoli, momvelanso wolamulila wa mpweya umene umalamulila zocita za anthu. Mpweya umenewu, kapena kuti kaganizidwe kameneka, tsopano kakugwila nchito mwa ana a kusamvela.”—Aefeso 2:2, 3.
8 “Mpweya” wa dziko, kapena kuti mzimu wake, ndi mphamvu yosaoneka imene imasonkhezela anthu kuti asamvele Mulungu, ndipo imalimbikitsa ‘cilakolako ca thupi ndi cilakolako ca maso.’ (1 Yohane 2:16; 1Timoteyo 6:9, 10) Mzimu wa dziko uli ndi “ulamulilo” cifukwa umakopa matupi athu ocimwa, suoneka, uli ndi mphamvu, ndipo umaloŵelela ngati mpweya umene umapezeka paliponse. Mzimu umenewu ‘umagwila nchito’ mwa munthu pang’onopang’ono mwa kum’cititsa kuyamba kukhala ndi makhalidwe oipa monga kudzikonda, kudzikuza, dyela, mzimu wosafuna kuuzidwa zocita ndi kupanduka. * Mwacidule, mzimu wa dziko mwapang’onopang’ono umacititsa makhalidwe a Mdyelekezi kukula mumtima mwa munthu.—Yohane 8:44; Machitidwe 13:10; 1 Yohane 3:8, 10.
9. Kodi mzimu wa dziko ungaloŵe bwanji mu mtima ndi m’maganizo athu?
9 Kodi n’zotheka kuti mzimu wa dziko uzike mizu m’maganizo ndi mumtima mwanu? Inde n’zotheka ngati mwaulola mwa kusakhala maso. (Ŵelengani Miyambo 4:23.) Mzimu wa dziko umayamba kusonkhezela munthu pang’onopang’ono, mwina kupitila m’mabwenzi amene angaoneke ngati anthu abwino, koma sakonda Yehova. (Miyambo 13:20; 1 Akorinto 15:33) Tingatengelenso mzimu woipa umenewo kupyolela m’mabuku oipa, mawebusaiti a zamalisece kapena zampatuko, zosangulutsa zoipa ndi maseŵela a mpikisano wa wafawafa. Inde, kupyolela mwa aliyense kapena ciliconse cimene cimalimbikitsa maganizo a Satana kapena dziko lake.
10. Kodi mzimu wa dziko tingaukanize bwanji?
1 Yohane 4:4) Conco, n’kofunika kwambili kuti tizipemphela kwa Yehova nthawi zonse.
10 Kodi mzimu woipa wa dziko tingaukanize bwanji kuti tikhalabe m’cikondi ca Mulungu? Ndi kokha mwa kugwilitsila nchito mokwanila zogaŵila za kuuzimu za Yehova ndi kupempha mzimu woyela nthawi zonse. Yehova ndi wamkulu kwambili kuposa Mdyelekezi kapena dziko loipali lolamulidwa ndi Satana. (KUVALA NDI KUDZIKONZA MWAULEMU
11. Kodi mzimu wa dziko waononga bwanji mavalidwe?
11 Mmene munthu amavalila, mmene amadzikonzela, ndi kudzisamalila zimaonetsa mzimu umene umamutsogolela. M’maiko ambili mavalidwe aipa kwambili cakuti woulutsa nkhani wina pa TV ananena kuti, anthu ambili atengela kavalidwe ka mahule, cakuti posacedwapa kudzakhala kovuta kudziŵa kuti hule ndi uti. Ngakhale atsikana amene sanafike zaka 13, atengela kavalidwe kameneka, cakuti nyuzipepala ina inati anthu amavala zoonetsa thupi kwambili. Ena ali ndi cizoloŵezi covala motailila, zimene zimaonetsa mzimu wopanduka ndi wosadzilemekeza.
12, 13. Kodi tiyenela kukumbukila mfundo ziti pankhani ya kavalidwe ndi kudzikonza?
12 Monga atumiki a Yehova, timafuna kuoneka bwino, mwa kuvala zovala zaudongo ndi zooneka bwino, zogwilizana ndi malo amene tili. Nthawi zonse maonekedwe athu azikhala ‘aulemu ndi anzelu.’ Maonekedwe amenewa pamodzi ndi “nchito zabwino,” azikhala oyenelela kwa onse, kaya kwa mwamuna kapena mkazi, “amene amati amalemekeza Mulungu.” Colinga cathu kwenikweni si kudzionetsela, koma ‘kukhalabe m’cikondi ca Mulungu.’ (1 Timoteyo 2:9, 10; Yuda 21) Inde, tifuna kuti kudzikonza kwathu kukhale kwa “munthu wobisika wamumtima . . . , umene uli wamtengo wapatali pamaso pa Mulungu.”—1 Petulo 3:3, 4.
13 Kumbukilaninso kuti masitaelo a zovala zathu ndi mmene timadzikonzela zingakhudze mmene ena amaonela kulambila kwathu. Liu la Cigiriki limene analitembenuza kuti “mwaulemu,” akaligwilitsila nchito ponena za makhalidwe, limatanthauza mantha aulemu, ndi kulemekeza malingalilo a ena kapena zofuna zao. Conco, colinga cathu cikhale kulemekeza zikumbumtima za ena, m’malo mongotsatila zofuna zathu pa nkhani ya kavalidwe. Koposa zonse, timafuna kulemekeza Yehova ndi anthu ake, ndiponso kuonetsa kuti ndife atumiki a Mulungu mwa kucita “zonse ku ulemelelo wa Mulungu.”1 Akorinto 4:9; 10:31; 2 Akorinto 6:3, 4; 7:1.
—14. Pankhani ya maonekedwe athu ndi ukhondo, kodi tiyenela kudzifunsa mafunso ati?
14 Mavalidwe, mmene timadzikonzela, ndi ukhondo n’zofunika kwambili makamaka tikakhala mu ulaliki, kapena pamene tili pamsonkhano. Dzifunseni kuti: ‘Kodi maonekedwe anga ndi mmene ndimadzikonzela zimapangitsa kuti anthu azingondiyang’ana? Kodi maonekedwe anga amacititsa ena manyazi? Kodi ndimaona ufulu wanga pa mbali zimenezi kukhala wofunika kwambili kuposa mwai wotumikila mumpingo?’—Salimo 68:6; Afilipi 4:5; 1 Petulo 5:6.
15. N’cifukwa ninji Mau a Mulungu satipatsa malamulo acindunji pankhani ya kavalidwe, kudzikonza ndi ukhondo?
15 M’Baibulo mulibe malamulo acindunji pankhani ya kavalidwe, kudzikonza ndi ukhondo. Yehova safuna kutilanda ufulu wosankha zimene tifuna, kapena wogwilitsila nchito nzelu zathu pankhani imeneyi. Iye amafuna kuti tikhale anthu okhwima kuuzimu, odziŵa kugwilitsila nchito mfundo za m’Baibulo. Amafunanso kuti tikhale anthu ‘amene pogwilitsa nchito mphamvu zathu za kuzindikila, tiziphunzitsa mphamvuzo kusiyanitsa coyenela ndi cosayenela.’ (Aheberi 5:14) Koposa zonse, iye amafuna kuti tizicita zinthu cifukwa comukonda ndiponso cifukwa cokonda anthu anzathu. (Ŵelengani Maliko 12:30, 31.) Ngati titsatila mfundo zimenezi, tidzayamba kuvala ndi kudzikonza m’njila zosiyanasiyana, koma moyenelela. Umboni wa zimenezi umaonekela ndi mmene anthu a Yehova acimwemwe amavalila kulikonse kumene asonkhana padziko lapansi.
KUKHALA NDI DISO LOLUNJIKA PA CINTHU CIMODZI
16. Kodi mzimu wa dziko umasiyana bwanji ndi ziphunzitso za Yesu? Nanga tiyenela kudzifunsa mafunso ati?
16 Mzimu wa dziko ndi wonyenga, ndipo umapangitsa anthu mamiliyoni ambili kudalila ndalama ndi zinthu zakuthupi kuti apeze cimwemwe. Koma Yesu anati: “Ngakhale munthu atakhala ndi zoculuka cotani, moyo wake sucokela m’zinthu zimene ali nazo.” (Luka 12:15) Yesu sanali kulimbikitsa kudzivutitsa dala, kapena kudzimana mopitilila malile. Iye anaphunzitsa kuti anthu amene amapeza moyo ndi cimwemwe ceniceni ndi aja amene “amazindikila zosoŵa zao zauzimu” ndiponso amene ali ndi “diso lolunjika pa cinthu cimodzi,” limene limangoyang’ana pa zinthu zakuuzimu. (Mateyu 5:3; 6:22, 23) Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimakhulupililadi zimene Yesu anaphunzitsa, kapena ndimatengela nzelu za “tate wake wa bodza”? (Yohane 8:44) Kodi zokamba zanga, zolinga zanga, ndi zinthu zimene ndimaika patsogolo, ndiponso umoyo wanga zimavumbula ciani?’—Luka 6:45; 21:34-36; 2 Yohane 6.
17. Chulani mapindu amene anthu okhala ndi diso lolunjika pa cinthu cimodzi amapeza.
17 Yesu anati: “Nzelu imatsimikizilika kuti ndi yolungama cifukwa ca nchito zake.” (Mateyu 11:19) Taganizilani mapindu ena amene anthu okhala ndi diso lolunjika pa cinthu cimodzi amapeza. Amapeza citsitsimulo ceniceni pogwila nchito ya Ufumu. (Mateyu 11:29, 30) Amapewa nkhawa zopambanitsa, ndipo mwa kutelo amapewa kuvutika maganizo. (Ŵelengani 1 Timoteyo 6:9, 10.) Cifukwa cokhutila ndi zimene ali nazo, io amakhala ndi nthawi yambili yokhala ndi banja lao ndi Akristu anzao. Amagona tulo twabwino. (Mlaliki 5:12) Amapeza cimwemwe coculuka cifukwa cokhala ndi mzimu wopatsa mulimonse mmene angakwanitsile. (Machitidwe 20:35) Amakhala ndi “ciyembekezo cacikulu,” mtendele wa mumtima ndi cikhutilo. (Aroma 15:13; Mateyu 6:31, 32) Inde, madalitso amenewa ndi osaneneka!
KUNYAMULA “ZIDA ZONSE ZA NKHONDO”
18. Kodi Baibulo limamufotokoza bwanji mdani wathu, njila zake, ndi mmene nkhondo yathu ilili?
18 Anthu amene amakhalabe m’cikondi ca Mulungu amatetezedwa mwakuuzimu kuti Satana asawaononge. Satana amafuna kuti Akristu asakhale ndi cimwemwe, ndi kuti asakapeze moyo wamuyaya. (1 Petulo 5:8) Paulo anati: “Cifukwa sitikulimbana ndi anthu athupi la magazi ndi nyama ai, koma ndi maboma, maulamulilo, olamulila dziko a mdimawu, ndi makamu a mizimu yoipa m’malo akumwamba.” (Aefeso 6:12) Liu lakuti ‘kulimbana’ lionetsa kuti nkhondo yathu si yomenyana motalikilana kapena yobisalilana koma ndi yomenyana moyandikilana. Ndiponso mau akuti “maboma,” “maulamulilo,” ndi akuti “olamulila dziko,” amaonetsa kuti ziŵanda zili ndi dongosolo lao ndipo zimacita kukonzekela kuti ziukile munthu.
19. Chulani ndi kufotokoza zida za kuuzimu zimene Mkristu ayenela kuvala.
19 Komabe, ngakhale kuti tili ndi zofooka, tingapambane pa nkhondo imeneyi. Motani? Mwa kunyamula “zida zonse zankhondo zocokela kwa Mulungu.” (Aefeso 6:13) Pofotokoza zida zimenezo, lemba la Aefeso 6:14-18 limati: “Khalani olimba, mutamanga kwambili coonadi m’ciuno mwanu, mutavalanso codzitetezela pacifuŵa cacilungamo, mapazi anu mutawaveka nsapato zokonzekela uthenga wabwino wamtendele. Koposa zonse, nyamulani cishango cacikulu cacikhulupililo, cimene mudzathe kuzimitsila mivi yonse yoyaka moto ya woipayo. Komanso landilani cisoti colimba ca cipulumutso, ndiponso lupanga la mzimu, lomwe ndilo mau a Mulungu. Pamene mukutelo, muzipemphela pa cocitika ciliconse mu mzimu, mwa mtundu uliwonse wa pemphelo ndi pembedzelo. Kuti mucite zimenezi, khalani maso mosalekeza ndi kupemphela mopembedzela m’malo mwa oyela onse.”
20. Kodi ife timasiyana bwanji ndi asilikali enieni pa nkhondo yathu?
20 Popeza zida zankhondo za kuuzimu zimacokela kwa Mulungu, sizidzalephela kutiteteza malinga ngati tizivala nthawi zonse. Mosiyana ndi asilikali enieni, amene nthawi zina amafunikila kupuma pomenya nkhondo, Akristu ali pa nkhondo yopulumutsa moyo yosalekeza, mpaka pamene Mulungu adzaononga dziko la Satana, ndi kuponya ziŵanda kuphompho. (Chivumbulutso 12:17; 20:1-3) Conco, musataye mtima ngati mulimbana ndi zofooka kapena zikhumbo zoipa, pakuti tonse tiyenela ‘kudzimenyamenya’ kuti tikhalebe okhulupilika kwa Yehova. (1 Akorinto 9:27) Koma ngati sitikulimbana ndi ciliconse, m’pamene tiyenela kuda nkhawa.
21. Kodi tingapambane pankhondo yathu ya kuuzimu kokha ngati ticita ciani?
21 Komanso, nkhondo imeneyi sitingapambane mwa mphamvu Filimoni 2; Aheberi 10:24, 25) Onse okhulupilika pa mbali zimenezi adzapambana ndithu, ndipo adzathanso kuteteza cikhulupililo cao pamene ciyesedwa.
zathu. Ndiye cifukwa cake Paulo anakamba kuti tiyenela kupemphela kwa Yehova “pa cocitika ciliconse mu mzimu.” Ndiponso, tiyenela kumvetsela Yehova mwa kuphunzila Mau ake, ndi kusonkhana pamodzi ndi “asilikali” anzathu nthawi zonse, cifukwa sitili tokha pa nkhondo imeneyi. (KHALANI OKONZEKA KUTETEZA CIKHULUPILILO CANU
22, 23. (a) N’cifukwa ciani tiyenela kukhala okonzeka nthawi zonse kuteteza cikhulupililo cathu? Nanga ndi mafunso ati amene tiyenela kudzifunsa? (b) Kodi tidzakambilana ciani m’nkhani yotsatila?
22 Yesu anati: “Popeza simuli mbali ya dzikoli, . . . dziko likudana nanu.” (Yohane 15:19) Conco, Akristu afunika kukhala okonzeka nthawi zonse kuteteza cikhulupililo cao, ndipo ayenela kucita zimenezo mwaulemu ndiponso ndi mtima wofatsa. (Ŵelengani 1 Petulo 3:15.) Motelo, dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimamvetsetsa cifukwa cake Mboni za Yehova nthawi zina zimafunika kusiyana ndi anthu ambili? Ngati ndakumana ndi ciyeso cimeneci, kodi ndimakhulupililadi kuti zimene Baibulo ndi kapolo wokhulupilika amanena ndi zoyenela? (Mateyu 24:45; Yohane 17:17) Ndipo pa nkhani yocita cabwino pamaso pa Yehova, kodi ndine wokonzeka kukhala wosiyana ndi ena ndipo kodi ndimanyadila kutelo?’—Salimo 34:2; Mateyu 10:32, 33.
23 Nthawi zambili, timayesedwa m’njila zina zovuta kuzizindikila kuti tikhale mbali ya dziko. Mwacitsanzo, monga tafotokozela kale, Mdyelekezi amakopa atumiki a Yehova kuti aloŵelele m’zinthu za dziko mwa kugwilitsila nchito zosangulutsa zoipa. Kodi tingasankhe bwanji zosangulutsa zoyenela zimene zingatitsitsimule ndi kutisiya ndi cikumbumtima coyela? Tidzakambilana zimenezi m’nkhani yotsatila.
^ par. 3 Kuyambila pa Pentekosite wa mu 33 C.E., Kristu wakhala Mfumu pa mpingo wa Akristu odzozedwa padziko lapansi. (Akolose 1:13) Mu 1914, Kristu analandila mphamvu za ulamulilo pa “ufumu wa dziko.” Conco, Akristu odzozedwa tsopano amatumikilanso monga akazembe a Ufumu wa Mesiya.—Chivumbulutso 11:15.
^ par. 8 Onani buku la Kukambitsirana za m’Malemba, patsamba 323 mpaka 327, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
^ par. 65 Onani Zakumapeto, kamutu kakuti “Kucitila Saliyuti Mbendela, Kuvota ndi Kugwila Nchito Imene Si Yausilikali.”