Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI 9

“Thaŵani dama”

“Thaŵani dama”

“Cititsani ziwalo za thupi lanu padziko lapansi kukhala zakufa ku dama, zinthu zodetsa, cilakolako ca kugonana, cikhumbo coipa, ndi kusilila kwa nsanje, kumene ndiko kulambila mafano.”—AKOLOSE 3:5.

1, 2. Kodi Balamu anakonza ciwembu cotani kuti avulaze anthu a Yehova?

YELEKEZELANI kuti mukuona msodzi amene wapita pamalo amene amakonda kuŵedzela nsomba. Iye akudziŵa nsomba imene afuna kuŵedza. Ndipo wasankha nyambo imene afuna kuseŵenzetsa, ndiyeno akuponya mbedza yake m’madzi. Posapita nthawi, iye akuona kuti fumbu la mbedza yake layamba kugwedela, ndipo mwamsanga akukoka mbedzayo. Iye wagwila nsomba, ndipo akumwetulila cifukwa wagwilitsila nchito nyambo yoyenela.

2 M’caka ca 1473 B.C.E, munthu wina dzina lake Balamu, anaganizilapo kwambili za nyambo imene angagwilitsile nchito. Colinga cake cinali kukopa anthu a Mulungu, amene anali m’Cigwa ca Moabu, kumalile a Dziko Lolonjezedwa. Balamu anali kudziona monga mneneli wa Yehova, koma anali munthu wadyela amene anatumidwa kuti akatembelele Aisiraeli. Koma cifukwa cakuti Yehova analoŵelelapo, Balamu sanatembelele anthu a Yehova, m’malo mwake anawadalitsa. Pofunitsitsa kulandila malipilo, Balamu anaganiza kuti mwina angacititse Mulungu kutembelela anthu ake ngati anthuwo atacita chimo lalikulu. Ali ndi zimenezo m’maganizo, Balamu anapeza nyambo yoyenelela. Iye anagwilitsila nchito atsikana acimoabu.—Numeri 22:1-7; 31:15, 16; Chivumbulutso 2:14.

3. Kodi ciwembu ca Balamu cinapambana motani?

3 Kodi nyambo ya Balamu inaseŵenza? Tingati inde, cifukwa amuna aciisiraeli masauzande ambili anacita kudamula nyambo ndi mbedza yomwe pamene “anayamba kucita ciwelewele ndi akazi a ku Moabu.” Anayambanso kulambila milungu ya Amoabu, kuphatikizapo mulungu wonyansa Baala wa ku Peori, amene anali mulungu wobeleketsa kapena wa kugonana. Zotsatilapo zake zinali zakuti Aisiraeli okwana 24,000 anaphedwa atatsala pang’ono kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa. Koma ili linalidi tsoka lalikulu.—Numeri 25:1-9.

4. N’cifukwa ciani Aisiraeli masauzande ambili anagwidwa mu msampha wa ciwelewele?

4 Kodi ciani cinapangitsa zimenezi? Anthu ambili anakhala ndi mtima woipa mwa kupandukila Yehova, Mulungu amene anawatulutsa m’dziko la Iguputo, amene anawapatsa cakudya m’cipululu, ndi kuwatsogolela bwinobwino ku Dziko Lolonjezedwa. (Aheberi 3:12) Poganizila zimene zinacitika, mtumwi Paulo analemba kuti: “Tisamacite dama, mmene ena mwa io anacitila dama, n’kufa 23,000 tsiku limodzi.” *1 Akorinto 10:8.

5, 6. N’cifukwa ciani nkhani yokhudza chimo la Aisiraeli m’Cigwa ca Moabu ndi cenjezo kwa ife masiku ano?

5 Monga anthu a Mulungu amene tili pafupi kuloŵa m’dziko lolonjezedwa labwino koposa, timaphunzila zambili pa nkhani imeneyi ya m’buku la Numeri. (1 Akorinto 10:11) Mwacitsanzo, anthu m’dzikoli amakonda zaciwelewele monga mmene zinalili m’nthawi ya Amoabu, koma masiku ano anthu acita kunyanya. Caka ciliconse Akristu masauzande ambili amagwidwa mu msampha waciwelewele, nyambo imodzimodzi imene inagwetsa Aisiraeli. (2 Akorinto 2:11) Potsatila citsanzo ca Zimiri amene monyada anabweletsa mkazi wacimidiyani ku msasa wa Aisiraeli ndi kuloŵa naye m’hema wake, masiku ano anthu ena amene amayanjana ndi anthu a Mulungu aononga makhalidwe a Akristu ena mumpingo.—Numeri 25:6, 14; Yuda 4.

6 Kodi mukuona kuti muli m’Cigwa ca Moabu ca masiku ano? Kodi mukuzindikila kuti mphoto yanu ya dziko latsopano imene mwaiyembekezela kwa nthawi yaitali ili pafupi kwambili? Ngati ndi conco, citani zonse zimene mungathe kuti mukhalebe m’cikondi ca Mulungu mwa kumvela lamulo lakuti: “Thaŵani dama.”—1 Akorinto 6:18.

Cigwa ca Moab

KODI DAMA N’CIANI?

7, 8. Kodi “dama” n’ciani? Ndipo amene amacita dama amakumana ndi mavuto otani?

7 Malinga ndi Baibulo, liu lakuti “dama” (Cigiriki, por·neiʹa) limatanthauza kugonana kwa anthu amene si okwatilana mogwilizana ndi Malemba. Limaphatikizapo cigololo, uhule, kugonana kwa anthu osakwatilana, kugonana m’kamwa, kugonana kumatako, ndi kuseŵeletsa ziŵalo zobelekela za munthu amene si mwamuna kapena mkazi wanu. Dama limaphatikizaponso kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha, ndiponso kugonana ndi nyama. *

8 Malemba amanena mosapita m’mbali kuti anthu amene amacita dama sayenela kukhala mumpingo wacikristu ndipo sadzalandila moyo wosatha. (1 Akorinto 6:9; Chivumbulutso 22:15) Ndiponso, ngakhale nthawi ino, anthu amenewo amadzivulaza, cifukwa ena amaleka kuwakhulupilila ndipo amadzicotsela ulemu, amakangana m’banja, amavutika ndi cikumbumtima, amatenga mimba zapathengo ndi matenda, ndipo ngakhale kufa kumene. (Ŵelengani Agalatiya 6:7, 8.) N’kucitilanji zinthu zimene zingatibweletsele mavuto ambili conco? N’zomvetsa cisoni kuti anthu ambili akayamba kucita zinthu zimenezi, saganizila za mavuto amenewa. Nthawi zambili cimene cimayambitsa zimenezi ndi kupenyelela zamalisece.

ZAMALISECE ZIMATSOGOLELA KU DAMA

9. Kodi zamalisece zilibe vuto monga mmene ena amanenela? Fotokozani.

9 M’maiko ambili, zamalisece zafala kwambili, cakuti zimapezeka ngakhale kwa ogulitsa nyuzipepala, m’nyimbo, ndi pa ma TV, ndipo zatenga malo pa Intaneti. * Kodi zamalisece zilibe vuto monga mmene ena amakambila? Iyai. Anthu amene amakonda kupenyelela zamalisece amakhala ndi cizoloŵezi coseŵeletsa malisece. Ndipo amakhala ndi “zilakolako zamanyazi za kugonana,” zimene zingawacititse kukhala ndi vuto lokonda zakugonana, cilakolako ca kugonana kwacilendo, mavuto aakulu m’banja, ngakhale kulekana kumene. * (Aroma 1:24-27; Aefeso 4:19) Katswili wina anayelekezela vuto lokonda zakugonana ndi matenda a kansa. Iye anati: “Vutoli limayamba pang’onopang’ono kenako n’kufalikila. Silibwelela m’mbuyo ndipo lilibe mankhwala.”

Kugwilitsila nchito Intaneti pamalo oonekela kwa onse m’nyumba ndi cinthu canzelu

10. Kodi mfundo ya pa Yakobo 1:14, 15, tingaigwilitsile nchito motani? (Onaninso kabokosi kakuti “ Zimene Zinandithandiza Kusiya Cizoloŵezi Coipa.”)

10 Mau a pa Yakobo 1:14, 15 amati: “Munthu aliyense amayesedwa mwa kukopedwa ndi kukodwa m’cilakolako cake. Ndiye cilakolako cikatenga pakati, cimabala chimo. Nalonso chimo likakwanilitsidwa, limabweletsa imfa.” Conco, cilakolako coipa cikayamba m’maganizo anu, muyenela kucitapo kanthu mwamsanga. Mwacitsanzo, mukaona cithunzithunzi coipa mwangozi, mwamsanga yang’anani kumbali, zimitsani kompyuta kapena sinthani chanelo ca TV. Citani zonse zimene mungathe kuti zilakolako zoipa zisakhazikike mumtima mwanu ndi kukugonjetsani.—Ŵelengani Mateyu 5:29, 30.

11. Pamene tikulimbana ndi zikhumbo zoipa, kodi tingaonetse bwanji kuti timadalila Yehova?

11 Mulungu amene amatidziŵa bwino kwambili kuposa mmene timadzidziŵila amatilangiza kuti: “Cititsani ziwalo za thupi lanu padziko lapansi kukhala zakufa ku dama, zinthu zodetsa, cilakolako ca kugonana, cikhumbo coipa, ndi kusilila kwa nsanje, kumene ndiko kulambila mafano.” (Akolose 3:5) N’zoona kuti kucita zimenezo kungakhale kovuta. Koma tisaiŵale kuti tili ndi Atate wathu wakumwamba, wacikondi ndi woleza mtima amene tingafikile m’pemphelo. (Salimo 68:19) Conco, maganizo odetsa akayamba kuloŵa mumtima mwanu, mwamsanga pemphelani kwa iye. M’pempheni “mphamvu yoposa yacibadwa,” ndipo yesetsani kuika maganizo anu pa zinthu zina.—2 Akorinto 4:7; 1 Akorinto 9:27; onani kabokosi kakuti “ Kodi Ndingasiye Bwanji Khalidwe Loipa?

12. Kodi “mtima” wathu n’ciani? Nanga n’cifukwa ciani tiyenela kuuteteza?

12 Munthu wanzelu Solomo analemba kuti: “Uteteze mtima wako kuposa zonse zimene ziyenela kutetezedwa, pakuti mumtimamo ndiye muli akasupe a moyo.” (Miyambo 4:23) “Mtima” wathu ndi munthu wathu wamkati, mmene tililidi pamaso pa Mulungu. Ndiponso, cimene cidzacititsa kuti tilandile moyo wosatha ndi mmene “mtima” wathu ulili pamaso pa Mulungu, osati mmene timaonekela kwa ena. Mfundo imeneyi si yovuta kumva. Komanso ndi nkhani yaikulu. Munthu wokhulupilika, Yobu, anacita pangano ndi maso ake kuti asayang’ane mkazi ndi kum’khumbila. (Yobu 31:1) Cimeneci n’citsanzo cabwino kwambili kwa ife. Wamasalimo anaonetsa kuti anali ndi maganizo amodzimodziwo pamene anapemphela kuti: “Cititsani maso anga kuti asaone zinthu zopanda pake.”—Salimo 119:37.

DINA SANASANKHE BWINO MABWENZI

13. Kodi Dina anali ndani? Ndipo n’cifukwa ciani tinganene kuti sanasankhe bwino mabwenzi?

13 M’nkhani 3 tinaphunzila kuti anzathu angatisonkhezele kucita zabwino kapena zoipa. (Miyambo 13:20; ŵelengani 1 Akorinto 15:33.) Ganizilani citsanzo ca Dina, mwana wamkazi wa Yakobo. (Genesis 34:1) Mosasamala kanthu kuti analeledwa bwino, Dina mopanda nzelu anasankha atsikana acikanani kukhala anzake. Akanani anali kukonda zaciwelewele kwambili. (Levitiko 18:6-25) Kwa amuna acikanani kuphatikizapo Sekemu, amene anali “wolemekezeka kwambili m’nyumba yonse ya bambo ake,” Dina anaoneka kukhala wosavuta kumunyengelela.—Genesis 34:18, 19.

14. Kodi kusasankha bwino mabwenzi kwa Dina kunabweletsa mavuto otani?

14 Mwina pamene Dina anaona Sekemu sanaganize zogonana naye. Koma zimene Sekemu anacita ndi zimene Akanani ambili anali kuona kuti ndi zoyenela kucita akakhala ndi cilakolako ca kugonana. Ngakhale kuti Dina anayesa kukana, zimenezo zinali m’mbuyo mwa alendo, cifukwa “iye anam’tenga” ndi “kumuipitsa.” Ndipo zioneka kuti pambuyo pake, Sekemu “anamukonda kwambili” Dina, koma zimenezo sizinasinthe zimene anacita kwa iye. (Ŵelengani Genesis 34:1-4.) Ndipo amene anavutika si Dina yekha iyai. Cifukwa cosasankha bwino mabwenzi, iye anacititsa mavuto amene anabweletsa citonzo ndi manyazi pabanja lao lonse.—Genesis 34:7, 25-31; Agalatiya 6:7, 8.

15, 16. Kodi tingapeze bwanji nzelu yeniyeni? (Onaninso bokosi lakuti “ Malemba Amene Tiyenela Kusinkhasinkha.”)

15 Dina ayenela kuti anamva nkhwangwa ili m’mutu. Anthu amene amakonda Yehova ndi kumumvela, sayenela kucita kuyembekezela kukumana ndi mavuto kuti aphunzile zinthu. Cifukwa comvela Mulungu, io amasankha ‘kuyenda ndi anthu anzelu.’ (Miyambo 13:20a) Conco, io amadziŵa “njila yonse ya zinthu zabwino,” ndipo amapewa mavuto oputa dala ndi zoŵaŵa zambili.—Miyambo 2:6-9; Salimo 1:1-3.

16 Anthu amene amapeza nzelu yaumulungu ndi aja amene amailakalaka ndi kucitapo kanthu, mwa kulimbikila kupemphela, kuphunzila Mau a Mulungu, ndi zofalitsa za kapolo wokhulupilika ndi wanzelu. (Mateyu 24:45; Yakobo 1:5) Cinanso cofunika ndi kudzicepetsa, kumene kumaonekela pamene titsatila uphungu wa m’Malemba mwaufulu. (2 Mafumu 22:18, 19) Mwacitsanzo, Mkristu angavomeleze mfundo yakuti mtima wake ndi wonyenga kwambili ndipo ungacite coipa ciliconse. (Yeremiya 17:9) Koma ngati zacitika kuti walakwitsa pena pake, kodi angadzicepetse ndi kulandila uphungu wacindunji ndi wacikondi?

17. Fotokozani zimene zingacitike m’banja ndi zimene tate angakambilane ndi mwana wake.

17 Ganizilani cocitika ici: Atate aletsa mwana wao wamkazi kupita kwinakwake ndi mnyamata wacikristu popanda wowapelekeza. Mtsikanayo ayankha kuti: “Atate, ndiye kuti simundikhulupilila? Sitingacite coipa ciliconse.” Mtsikanayo angakhale kuti amakondadi Yehova ndipo ali ndi zolinga zabwino. Koma kodi ‘akuyendadi mwanzelu’ za Mulungu? Kodi ‘akuthaŵadi dama’? Kapena kodi ‘akudalila mtima wake’ mopanda nzelu? (Miyambo 28:26) Mwina mungaganizile mfundo zina zoonjezela zimene zingathandize tateyo ndi mwana wake pokambilana nkhani imeneyi.—Onani Miyambo 22:3; Mateyu 6:13; 26:41.

YOSEFE ANATHAŴA DAMA

18, 19. Kodi ndi ciyeso cotani cimene Yosefe anakumana naco? Ndipo iye anacita ciani?

18 Mnyamata wabwino amene anali kukonda Mulungu ndipo anathaŵa dama ndi Yosefe, mlongo wa Dina. (Genesis 30:20-24) Akali mwana, Yosefe anadzionela yekha zotsatilapo zoipa za kupanda nzelu kwa mlongo wake. Mosakaikila, kukumbukila zinthu zimenezi, komanso kufunitsitsa kwa Yosefe kukhalabe m’cikondi ca Mulungu, kunamuchinjiliza pa zaka za mtsogolo ku Iguputo, pamene mkazi wa abwana ake anali kum’nyengelela “tsiku ndi tsiku” kuti agone naye. Pokhala kapolo, Yosefe sakanangosiya nchito ndi kubwelela kwao. Anangofunikila kulimbana ndi zocitikazo mwanzelu ndiponso molimba mtima. Yosefe anakana mobwelezabweleza pamene mkazi wa Potifara anali kumukopa, ndipo potsilizila pake anam’thaŵa.—Ŵelengani Genesis 39:7-12.

19 Taganizilani: Ngati Yosefe anali kukhumbila mkaziyo kapena ngati anali ndi cizoloŵezi coganiza za kugonana, kodi akanakhalabe wokhulupilika? Kutalitali. M’malo mokhala ndi maganizo oipa, Yosefe anaona kufunika kwa ubwenzi wake ndi Yehova, ndipo izi zinaonekela m’mau amene anauza mkazi wa Potifara. Iye anali kuuza mkaziyo kuti: “Mbuye wanga anaika ciliconse m’manja mwanga kupatulapo inuyo, cifukwa ndinu mkazi wake. Ndiye ndingacitilenji coipa cacikulu conci n’kucimwila Mulungu?”—Genesis 39:8, 9.

20. Kodi Yehova analoŵelelapo motani pankhani ya Yosefe?

20 Talingalilani cisangalalo cimene Yehova anali naco pamene anaona Yosefe wacinyamatayo, amene ngakhale kuti anali kutali ndi kwao, anakhalabe  wokhulupilika tsiku ndi tsiku. (Miyambo 27:11) Pambuyo pake, Yehova analoŵelelapo mpaka Yosefe anamasulidwa m’ndende ndi kuikidwa kukhala nduna yaikulu mu  Iguputo ndi  woyang’anila zakudya. (Genesis 41:39-49) Mau a pa Salimo 97:10 ndi oona pamene amati: “Inu okonda Yehova danani naco coipa. Iye amateteza moyo wa anthu ake   okhulupilika. Amawalanditsa m’manja mwa anthu oipa.”

21. Kodi m’bale wacinyamata m’dziko lina mu Africa, anaonetsa bwanji kulimba mtima kuti asacite zoipa?

21 N’cimodzimodzi masiku ano, atumiki ambili a Mulungu amaonetsa kuti ‘amadana ndi coipa ndi kukonda cabwino.’ (Amosi 5:15) M’bale wina wacinyamata m’dziko lina mu Africa ananena kuti, tsiku lina mtsikana wina wa m’kalasi mwake anamufikila ndi kumuuza kuti akamuthandizako masamu adzagona naye. M’baleyo anati: “Ndinakana kwa mtu wagalu. Mwa kukhalabe wokhulupilika ndadzisungila ulemu, umene ndi wofunika kwambili kuposa golide ndi siliva.” N’zoona kuti uchimo ungabweletse cisangalalo ca kanthawi, koma cisangalalo cotelo cimabweletsa mavuto oculuka. (Aheberi 11:25) Cisangalalo cimeneci cimakhala cocepa pociyelekezela ndi cisangalalo cokhalitsa cimene timakhala naco cifukwa comvela Yehova.—Miyambo 10:22.

LANDILANI THANDIZO LA MULUNGU WACIFUNDO

22, 23. (a) N’cifukwa ciani tinganene kuti Mkristu amene wacita chimo lalikulu angalandile thandizo? (b) Ndi thandizo lotani limene munthu angapeze akacimwa?

22 Popeza ndife opanda ungwilo, tonse timavutika kuti tigonjetse zilakolako za thupi ndi kucita zoyenela pamaso pa Mulungu. (Aroma 7:21-25) Yehova amadziŵa zimenezi, cifukwa “amakumbukila kuti ndife fumbi.” (Salimo 103:14) Koma nthawi zina, Mkristu angacite chimo lalikulu. Kodi izi zitanthauza kuti sangalandile thandizo lililonse? Iyai! N’zoona kuti wocimwayo angakumane ndi mavuto cifukwa ca chimo lake monga mmene zinalili ndi Mfumu Davide. Koma ngakhale ndi conco, Mulungu nthawi zonse ndi ‘wokonzeka kukhululukila’ onse olapa ndi amene ‘aulula’ macimo ao.—Salimo 86:5; Yakobo 5:16; ŵelengani Miyambo 28:13.

23 Kuonjezela pamenepo, Mulungu mokoma mtima watipatsa mpingo wacikristu mmene muli “mphatso za amuna,” abusa okhwima kuuzimu amene ndi oyenelela ndipo ndi okonzeka kutithandiza. (Aefeso 4:8, 12; Yakobo 5:14, 15) Colinga cao ndi kuthandiza wocimwayo kuti akonzenso ubwenzi wake ndi Mulungu, ndiponso malinga ndi mau a Solomo, io amafuna kuti wocimwayo ‘akhale ndi mtima wanzelu’ kuti asadzabwelezenso chimo lake.—Miyambo 15:32.

‘PEZANI MTIMA WANZELU’

24, 25. (a) Kodi mnyamata wofotokozedwa pa Miyambo 7:6-23 anasonyeza bwanji kuti ndi ‘wopanda nzelu’? (b)  Tingapeze bwanji ‘mtima wanzelu’?

24 Baibulo limakamba za anthu “opanda nzelu” ndi za amene ‘amapeza mtima wanzelu.’ (Miyambo 7:7) Cifukwa cokhala osakhwima kuuzimu ndiponso cifukwa cakuti sanatumikile Mulungu kwa nthawi yaitali, munthu “wopanda nzelu mumtima mwake” amakhala wosazindikila ndipo saganiza bwino pocita zinthu. Monga mnyamata wofotokozedwa pa Miyambo 7:6-23, iye akhoza kugwela m’chimo mosavuta. Koma amene ‘amapeza mtima wanzelu’ amasamalila kwambili umunthu wake wamkati mwa kukhala ndi phunzilo laumwini la Mau a Mulungu ndi kupemphela nthawi zonse. Ngakhale ndi wopanda ungwilo, amayesetsa kuti maganizo ake, zokhumba zake, mtima wake, ndi zolinga zake zigwilizane ndi zimene Mulungu amafuna. Mwa kucita zimenezo, iye ‘amakonda moyo wake,’ kapena kuti amadzibweletsela madalitso, ndipo “amapeza zabwino.”—Miyambo 19:8.

25 Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimaonadi kuti miyezo ya Mulungu ndi yolungama? Kodi ndimakhulupilila kuti kuitsatila kungandibweletsele cimwemwe cacikulu?’ (Salimo 19:7-10; Yesaya 48:17, 18) Ngati mumakaikila ngakhale pang’ono, lekani kukaikila. Ganizilani zotsatilapo zake zonyalanyaza malamulo a Mulungu. Kuonjezela pamenepo, “talawani ndipo muone kuti Yehova ndi wabwino” mwa kutsatila coonadi ndi kudzaza maganizo anu ndi zinthu zoyenela. Zinthu zoyenela zimenezi ndi “zinthu zoona, zolungama, zoyela, zacikondi, ndi khalidwe labwino.” (Salimo 34:8; Afilipi 4:8, 9) Mosakaikila, ngati muyesetsa kucita zimenezi, mudzamukonda kwambili Mulungu, mudzayamba kukonda zimene iye amakonda, ndi kudana ndi zimene iye amadana nazo. Yosefe sanali munthu wangwilo. Koma ‘anathaŵa dama’ cifukwa analola Yehova kumuumba kwa zaka zambili, ndi kumupatsa mtima wofuna kumukondweletsa. Inunso muyenela kucita cimodzimodzi.—Yesaya 64:8.

26. Kodi m’nkhani yotsatila tidzakambitsilana nkhani iti yofunika?

26 Mlengi wathu anatilenga ndi ziwalo zobelekela osati kuti tiziziseŵeletsa monga zidoli iyai, koma kuti tizizigwilitsila nchito kubelekela ana ndi kusangalalila m’cikwati. (Miyambo 5:18) Tidzakambitsilana mmene Mulungu amaonela cikwati m’nkhani ziŵili zotsatila.

^ par. 4 Ciŵelengelo cochulidwa m’buku la Numeri, mwacionekele cimaphatikizapo anthu 1000 ‘amene anali kutsogolela anthuwo’ amene anaphedwa ndi oweluza, ndiponso anthu ena amene anaphedwa mwacindunji ndi Yehova.—Numeri 25:4, 5.

^ par. 7 Ponena za nkhani yokhudza cidetso ndi khalidwe lotailila, onani “Mafunso ocokela kwa oŵelenga” mu Nsanja ya Olonda ya July 15, 2006, yofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ par. 9 “Zamalisece” zimene zachulidwa pano ndi zinthu monga zithunzithunzi, mabuku, ndi mau a pafoni odzutsa cilakolako cakugonana. Zamalisece zimaphatikizapo cithunzithunzi ca munthu amene waima modzutsa cilakolako ca kugonana, kapena zithunzithunzi za anthu aŵili kapena oposelapo amene akugonana.

^ par. 9 Onani Zakumapeto mutu wakuti “Kugonjetsa Cizoloŵezi Coseŵeletsa Malisece” kuti mudziŵe mmene mungagonjetsele cizoloŵezi ca kuseŵeletsa malisece.