NKHANI 16
Tsutsani Mdyelekezi ndi Zocita Zake Zacinyengo
“Tsutsani Mdyelekezi ndipo adzakuthaŵani.” —YAKOBO 4:7.
1, 2. Kodi ndani amene amasangalala panthawi ya ubatizo?
NGATI mwatumikila Yehova kwa zaka zambili, mosakaikila mwamvetselapo nkhani za ubatizo zambili pa misonkhano ya dela ndi ya cigawo. Komabe, kaya mwamvetselapo nkhani za ubatizo zingati, mumasangalala kwambili nthawi zonse mukaona anthu amene ali ku mipando yakutsogolo aimilila kuti akabatizidwe. Panthawi imeneyi, onse opezekapo pa cocitika cimeneci amasangalala ndipo amaomba m’manja. Misozi ingalengeze m’maso mwanu pamene muona gulu la anthu okondedwa amene asankha kukhala kumbali ya Yehova. Ndithudi, timasangalala kwambili panthawi zimenezi.
2 Ife timapenyelela ubatizo nthawi zoŵelengeka pa caka, koma angelo ali ndi mwai wopenyelela mwambo umenewu nthawi zambili. Ganizilani “cisangalalo coculuka” cimene cimakhala kumwamba angelo akaona anthu ena pafupifupi 5,000 mlungu uliwonse, akubwela m’gulu la Yehova padziko lapansi. (Luka 15:7, 10) Mosakaikila, angelo amasangalala kwambili akaona kuonjezeka kumeneku.—Hagai 2:7.
MDYEREKEZI “AKUYENDAYENDA UKU NDI UKU NGATI MKANGO WOBANGULA”
3. N’cifukwa ciani Satana “akuyendayenda uku ndi uku ngati mkango wobangula?” Nanga amafuna kucita ciani?
3 Koma pali zolengedwa zina zauzimu zimene zimakwiya kwambili zikaona anthu akubatizidwa. Satana ndi ziŵanda zake amaipidwa kwambili pamene aona anthu ambilimbili akucoka ku mbali ya dziko loipali. Ndipo Satana Yobu 2:4, 5.) Nthawi zonse munthu akasankha kudzipeleka kwa Yehova, Satana amaonekela kuti ndi wabodza. Zimakhala ngati kuti anthu ambili mlungu uliwonse pa caka amamuseka. N’cifukwa cake iye “akuyendayenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, wofunitsitsa kuti umeze winawake.” (1 Petulo 5:8) “Mkango” umenewu ndi wofunitsitsa kutimeza mwa kuuzimu, kusokoneza kapena kuthetsa ubwenzi wathu ndi Mulungu.—Salimo 7:1, 2; 2 Timoteyo 3:12.
modzitukumula ananena kuti, palibe munthu angatumikile Yehova cifukwa cakuti amam’kondadi, ndi kuti palibe amene angakhale wokhulupilika kwa Yehova akakumana ndi ciyeso cacikulu. (ŴelenganiMunthu aliyense akadzipeleka kwa Yehova ndi kubatizidwa, Satana amaonekela kuti ndi wabodza
4, 5. (a) Kodi Yehova waikila Satana malile m’njila ziŵili ziti? (b) Kodi Mkristu angakhale wotsimikiza za ciani?
4 Ngakhale kuti tili ndi mdani woopsa ameneyu, sitiyenela kucita mantha. Cifukwa ciani? Cifukwa cakuti Yehova waikila Chivumbulutso 7:9, 14) Maulosi a Mulungu salephela. Conco ngakhale Satana amadziŵa kuti sadzakwanitsa kupatutsa anthu onse a Mulungu.
“mkango wobangula” umenewu malile m’njila ziŵili zothandiza kwambili. Kodi njila zimenezo ndi ziti? Yoyamba, Yehova walosela kuti “khamu lalikulu” la Akristu oona, lidzapulumuka “cisautso cacikulu” cimene cikubwela. (5 Njila yaciŵili tingaidziŵe mwa kuona mfundo ya coonadi imene mtumiki wina wokhulupilika wa Mulungu wa m’nthawi zakale ananena. Mneneli Azaliya anauza Mfumu Asa kuti: “Yehova akhala nanu inuyo mukapitiliza kukhala naye.” (2 Mbiri 15:2; ŵelengani 1 Akorinto 10:13.) Zitsanzo zambili za m’Baibulo zimaonetsa kuti Satana analephela kupatutsa mtumiki wa Mulungu aliyense amene anakhalabe pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu. (Aheberi 11:4-40) Masiku ano, Mkristu amene ali pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu angatsutse Mdyelekezi ndi kumugonjetsa. Ndipo Mau a Mulungu amatiuza kuti: “Tsutsani Mdyelekezi ndipo adzakuthaŵani.”—Yakobo 4:7.
‘TIKULIMBANA . . . NDI MAKAMU A MIZIMU YOIPA’
6. Kodi Satana amaukila bwanji Mkristu aliyense payekhapayekha?
6 Satana sangapambane nkhondo yophiphilitsa imeneyi, koma angagonjetse ena a ife ngati sitisamala. Iye amadziŵa kuti akaononga ubwenzi wathu ndi Yehova, angathe kutimeza mwa kuuzimu. Kodi Satana amacita ciani kuti akwanilitse zimenezo? Amatiukila mwakhanza, amaukila aliyense payekhapayekha, ndiponso amatiukila mwamacenjela. Tiyeni tikambilane njila zikuluzikulu zimenezi, zimene Satana amagwilitsila nchito potiukila.
7. N’cifukwa ciani Satana akuukila mwankhanza anthu a Yehova?
7 Kuukila mwankhanza. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Mau amenewo ndi cenjezo kwa Akristu onse oona. Popeza kuti Satana wameza kale dziko lonse la anthu oipa, iye tsopano akuukila mwankhanza atumiki a Yehova amene acoka kale kumbali yake. (Mika 4:1; Yohane 15:19; Chivumbulutso 12:12, 17) Iye ndi wokwiya kwambili cifukwa cakuti akudziŵa kuti watsala ndi kanthawi kocepa. Conco, akuukila atumiki a Mulungu mwankhanza. Koposa ndi kale lonse, iye akumenya nkhondo zolimba kuti aononge ubwenzi wathu ndi Mulungu.
8. Kodi mtumwi Paulo anatanthauza ciani pamene anati ‘tikulimbana’ ndi mizimu yoipa?
8 Kulimbana ndi munthu payekhapayekha. Mtumwi Paulo anacenjeza Akristu anzake kuti: “Tikulimbana ndi . . . makamu a mizimu yoipa m’malo akumwamba.” (Aefeso 6: 12) N’cifukwa ciani Paulo anagwilitsila nchito liu lakuti “kulimbana”? N’cifukwa cakuti limapeleka lingalilo la kumenyana kocita kugwilana ndiponso moyandikana kwambili. Conco, pamene anagwilitsila nchito liu limeneli, iye anali kugogomeza mfundo yakuti aliyense wa ife payekha ali pankhondo yolimbana ndi mizimu yoipa. Kaya tikukhala m’dziko limene anthu amakhulupilila mizimu yoipa kapena ai, tiyenela kukumbukila kuti pamene tinadzipeleka kwa Yehova tinaloŵa m’bwalo la nkhondo yophiphilitsa. Kungocokela pamene wadzipeleka, Mkristu amakhala pa nkhondo. M’pake kuti Paulo anaona kufunika kolimbikitsa Akristu a ku Aefeso katatu konse kuti ‘akhale olimba.’—Aefeso 6: 11, 13, 14.
9. (a) N’cifukwa ciani Satana ndi ziŵanda amagwilitsila nchito “zocita zacinyengo” zosiyanasiyana? (b) N’cifukwa ciani Satana amayesa kupotoza maganizo athu? Ndipo tingalimbane naye bwanji? (Onani bokosi “ Samalani Ndi Macenjela A Satana!”) (c) Kodi tsopano tikambilana njila yacinyengo iti?
9 Kuukila mwamacenjela. Paulo analimbikitsa Akristu kuti asasunthike polimbana ndi “zocita zacinyengo” za Mdyelekezi. (Aefeso 6: 11) Onani kuti Paulo anagwilitsila nchito mau oonetsa kuti akukamba zinthu zambili. Mizimu yoipa imagwilitsila nchito njila zambili za macenjela, ndipo pali cifukwa cimene imacitila zimenezi. Akristu ena amene akhala okhulupilika pa ciyeso cina, agonja ndi ciyeso ca mtundu wina m’kupita kwa nthawi. Conco, Mdyelekezi ndi ziŵanda zake amayang’anitsitsa zocita za aliyense wa ife kuti adziŵe cofooka cathu cacikulu. Ndiyeno amatengela mwai pa cifooko ca kuuzimu ciliconse cimene tingakhale naco. Koma cosangalatsa n’cakuti, timawadziŵa macenjela ambili a Mdyelekezi cifukwa avumbulidwa m’Baibulo. (2 Akorinto 2:11) Kuciyambi kwa buku lino, tinakambilana macenjela monga msampha wokonda cuma, mayanjano oipa, ndi ciwelewele. Tiyeni tsopano tikambilane njila ina yacinyengo imene Satana amagwilitsila nchito. Njila imeneyo ndi kukhulupilila mizimu.
KUKHULUPILILA MIZIMU N’KUSAKHULUPILIKA
10. (a) Kodi kukhulupilila mizimu n’ciani? (b) Kodi Yehova amakuona bwanji? Nanga inu mumakuona bwanji?
10 Ngati munthu akhulupilila mizimu kapena zauciŵanda, amagwilizana mwacindunji ndi mizimu yoipa. Kuombeza, kucita zamatsenga, kulodza ena, ndi kufunsila kwa akufa ndi njila zina za kukhulupilila mizimu. Monga mmene tidziŵila, Yehova amaona kuti kukhulupilila mizimu ndi ‘konyansa.’ (Deuteronomo 18:10-12; Chivumbulutso 21:8) Popeza kuti ifenso tiyenela ‘kudana naco coipa,’ kungakhale kupanda nzelu kugwilizana ndi mizimu yoipa. (Aroma 12:9) Kucita zimenezo kungaonetse kuti ndife osakhulupilika kwa Atate wathu wakumwamba, Yehova.
11. N’cifukwa ciani tinganene kuti Satana angapambane kwambili ngati angaticititse kukhulupilila mizimu? Pelekani citsanzo.
11 Popeza kuti kucita zamizimu ngakhale pang’ono cabe n’kusakhulupilika ndithu kwa Yehova, Satana amafunitsitsa kuti ticite zimenezo. Nthawi iliyonse imene Satana wakopa Mkristu kuti acite zauciŵanda, amakhala kuti wapambana kwambili. N’cifukwa ciani tikutelo? Onani citsanzo ici: Ngati msilikali wapanduka ndi kucoka ku gulu lake ndi kukagwilizana ndi gulu la adani, mkulu wa adaniwo angakondwele kwambili. Iye angaonetse msilikali wopandukayo monyadila ku gulu limene analimo poyamba. Angamuonetse monga cizindikilo cakuti wapambana pofuna kunyoza mkulu wa asilikali enawo. Mofananamo, ngati Mkristu wayamba kukhulupilila mizimu, iye mwadala amasiya Yehova ndi kusankha kulamulidwa ndi Satana mwacindunji. Ganizilani mmene
Satana angasangalalile kuonetsa munthu wopandukayo monga cizindikilo cakuti wapambana nkhondo. Ndani wa ife amene angafune kusangalatsa Mdyelekezi? Palibe amene angafune. Ife sindife opanduka.AMAGWILITSILA NCHITO MAFUNSO OPANGITSA MUNTHU KUKAIKILA
12. Pankhani ya kukhulupilila mizimu, kodi Satana amagwilitsila nchito njila iti kuti apotoze maganizo athu?
12 Ngati tipitilizabe kudana ndi kukhulupilila mizimu, Satana sangathe kutigonjetsa pogwilitsila nchito njila imeneyi. Conco, iye amadziŵa kuti ayenela kupotoza maganizo athu. Kodi amacita bwanji zimenezo? Iye amayesa kupeza njila zimene angapotozele maganizo a Akristu ena kuti ayambe kuganiza kuti “cabwino n’coipa ndipo coipa n’cabwino.” (Yesaya 5:20) Kuti acite zimenezi, Satana amagwilitsila nchito njila ina imene iye amadalila. Njila imeneyi ndi kugwilitsila nchito mafunso opangitsa munthu kukaikila zinthu zina.
13. Kodi Satana wagwilitsila nchito motani mafunso opangitsa munthu kukaikila zinthu zina?
13 Onani mmene Satana anagwilitsila nchito njila imeneyi m’nthawi yakale. Mu Edeni, iye anafunsa Hava kuti: “Eti n’zoona kuti Mulungu anati musadye zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu?” M’nthawi ya Yobu, pamene angelo anali pa msonkhano kumwamba, Satana anafunsa kuti: “Kodi mukuganiza kuti Yobu amangoopa Mulungu pacabe?” Ndiponso pamene Yesu anayamba utumiki wake padziko lapansi, Satana anayesa Kristu pamene anati: “Ngati ndinudi mwana wa Mulungu, uzani miyala iyi kuti isanduke mitanda ya mkate.” Pa cocitika ici, onani kuti Satana anasuliza mau amene Yehova mwini ananena milungu 6 yapitayo akuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwela naye.”—Genesis 3:1; Yobu 1:9; Mateyu 3:17; 4:3.
14. (a) Kodi Satana amagwilitsila nchito bwanji njila yacinyengo kuti acititse anthu kuona ngati kukhulupilila mizimu ndi kwabwino? (b) Kodi tikambilana ciani tsopano?
14 Masiku ano, Mdyelekezi amagwilitsilanso nchito njila 2 Akorinto 11:3) Kodi anthu aconco tingawathandize bwanji kusintha maganizo ao? Kodi tingacite ciani kuti Satana asatisoceletse ndi njila yake yacinyengo imeneyi? Kuti tiyankhe, tiyeni tikambilane mbali ziŵili pa umoyo wathu zimene mwamacenjela, Satana waloŵetsamo zinthu za mizimu. Mbali zimenezi ndi zosangulutsa ndiponso kusamalila thanzi.
imeneyi kuti apangitse anthu kukaikila ngati kukhulupilila mizimu n’koipadi. N’zacisoni kuti iye wakwanitsa kucititsa Akristu ena kukhala ndi maganizo okaikila. Iwo ayamba kukaikila ngati njila zina za kukhulupilila mizimu ndi zoipadi. (AMATENGELA MWAYI PA ZOKONDA ZATHU NDI ZOSOŴA ZATHU
15. (a) Kodi anthu ambili ku maiko a azungu amakuona bwanji kukhulupilila mizimu? (b) Kodi Akristu ena akhudzidwa bwanji ndi maganizo a dziko pankhani ya kukhulupilila mizimu?
15 Makamaka ku maiko a azungu, matsenga, ufiti, ndi njila zina za kukhulupilila mizimu, amazitenga mopepuka. Nthawi zambili mafilimu, mabuku, mapulogalamu apa TV, ndi maseŵela a pakompyuta, amapangitsa anthu kuona kuti kucita za mizimu ndi kosangalatsa, kwabwinobwino ndiponso kuti kumaonetsa munthu kukhala wocenjela. Mafilimu ndi mabuku azamatsenga afala kwambili. Mwacionekele, ziŵanda zapangitsa anthu kuona kuti kucita zamatsenga kulibe vuto kwenikweni. Kodi maganizo amenewa akhudzanso Akristu? Inde, ena akhudzidwa. Mwanjila yotani? Mwacitsanzo, Mkristu wina pambuyo popenyelela filimu ya zamatsenga anati, “Ndinapenyelela filimu imeneyo, koma sindinacite zamizimu.” N’cifukwa ciani maganizo amenewa ndi oopsa?
16. N’cifukwa ciani kusankha zosangulutsa zokhala ndi zamatsenga n’koopsa?
16 N’zoona kuti kucita zamizimu n’kosiyana ndi kuzipenyelela, koma zimenezi sizitanthauza kuti kupenyelela zamatsenga kulibe vuto. N’cifukwa ciani tikutelo? Ganizilani izi: Mau a Mulungu amasonyeza kuti Satana kapena ziŵanda zake * Conco, monga mmene taonela kale, kuti ziŵanda zidziŵe zimene timaganiza ndi zofooka zathu za kuuzimu, zimayang’anitsitsa zocita zathu kuphatikizapo zosangulutsa zimene timasankha. Ngati zocita za Mkristu zimaonetsa kuti amakonda mafilimu kapena mabuku onena za olankhula ndi mizimu, matsenga, zocita za anthu ogwidwa ndi ziŵanda, kapena nkhani zilizonse zokhudza ziŵanda, iye amathandiza ziŵanda kudziŵa zimene zili m’maganizo mwake. Mwanjila imeneyi, iye amadziŵitsa ziŵandazo cofooka cake. Zikatelo, ziŵanda zingalimbikile kwambili kulimbana ndi Mkristuyo pa cofooka cakeco mpaka zitamugonjetsa. Ndipo anthu ena amene anayamba kucita cidwi ndi zamizimu cifukwa cokonda zosangulutsa zokhala ndi zamatsenga, ayamba kukhulupilila mizimu.—Ŵelengani Agalatiya 6:7.
sadziŵa zimene timaganiza.17. Kodi Satana angagwilitsile nchito njila yacinyengo iti kuti asoceletse Mkristu wodwala?
17 Kuonjezela pa zosangulutsa, Satana amatengelanso mwai pa nkhani ya thanzi lathu. Amacita motani zimenezo? Mkristu amene wadwala nthawi yaitali angathedwe nzelu kuti sadzacila, ngakhale pambuyo polandila cithandizo ca kucipatala mobwelezabweleza kapena kuonana ndi madokotala osiyanasiyana. (Maliko 5:25, 26) Zimenezi zingapatse Satana ndi ziŵanda zake mwai wakuti zisoceletse wodwalayo. Ziŵanda zingasonkhezele wodwalayo kufunafuna thandizo la mankhwala lophatikizapo kukhulupilila mizimu kapena “mphamvu zamatsenga.” (Yesaya 1:13) Ziŵanda zikapangitsa Mkristu kucita zimenezi, ubwenzi wa wodwalayo ndi Mulungu umasokonezeka. Motani?
18. Ndi njila zocilitsila ziti zimene Mkristu ayenela kukana? Ndipo n’cifukwa ciani?
18 Yehova amacenjeza anthu amene amaphwanya malamulo Miyambo 28:9) Cotelo, nthawi zonse timafuna kupewa ciliconse cimene cingapangitse kuti Yehova asamve mapemphelo athu ndi kuleka kutithandiza, makamaka pamene tikudwala. (Salimo 41:3) Conco, tisanalandile cithandizo ciliconse ca mankhwala, tiyenela kufufuza mayankho a mafunso awa: “Kodi sing’anga ameneyo amadziŵika kuti amacita zamizimu? Kodi cithandizo cimeneco n’cogwilizana ndi cikhulupililo cakuti matenda kapena imfa, zimacitika cifukwa cakuti mizimu ya akufa yakwiya, kapena cifukwa cakuti wodwalayo walodzedwa? Nanga mankhwala ake amakonzedwa kapena kugwilitsilidwa nchito motsatila miyambo yokhudza zamizimu? Ngati zioneka kuti mankhwala kapena njila zina zodziŵila matenda zimalowetsamo zamizimu, Mkristu woona ayenela kuzikana. * (Mateyu 6:13) Akatelo, sayenela kukaikila kuti Yehova adzam’thandiza.—Onani kabokosi kakuti “ Kodi Kucita Izi ndi Kukhulupilila Mizimu?”
lake kuti: “Munthu amene amathaŵitsa khutu lake kuti asamve cilamulo, ngakhale pemphelo lake limakhala lonyansa.” (NGATI NKHANI ZA ZIŴANDA N’ZOFALA
19. (a) Kodi Mdyelekezi wapusitsa anthu kuti azikhulupilila ciani ponena za mphamvu zake? (b) Ndi nkhani zotani zimene Akristu oona ayenela kupewa?
19 Ngakhale kuti anthu a ku maiko a azungu amapeputsa
mphamvu ya Satana, anthu a ku maiko ena amamuopa kwambili. Mdyelekezi wapusitsa anthu amenewo kuti azikhulupilila kuti iye ali ndi mphamvu kwambili kuposa zimene ali nazo. Anthu ena amangokhalila kuopa mizimu yoipa pakudya, pogwila nchito, pogona ndi pocita ciliconse. Nkhani zokhudza zocita za ziŵanda zili paliponse. Nthawi zambili anthu amakamba nkhani zimenezi mokokomeza, ndipo ena amacita nazo cidwi. Kodi nafenso tiyenela kufalitsa nkhani zaconco? Iyai. Atumiki a Mulungu woona amapewa kucita zimenezo pa zifukwa ziŵili zazikulu.20. Kodi munthu angafalitse bwanji mosadziŵa mabodza a Satana?
20 Coyamba, ngati munthu akufalitsa nkhani zokhudza zocita za ziŵanda, ndiye kuti akuthandiza kufalitsa mabodza a Satana. N’cifukwa ciani tikunena conco? Mau a Mulungu amavomeleza kuti Satana angacite nchito zamphamvu, koma amaticenjezanso kuti iye amagwilitsila nchito “zizindikilo zabodza” ndi “cinyengo.” (2 Atesalonika 2:9, 10) Popeza Satana ndiye wonyenga wamkulu, iye amadziŵa kupotoza maganizo a anthu amene amakonda kukhulupilila mizimu, ndi kuwacititsa kukhulupilila zinthu zabodza. Anthu amenewo angakhulupililedi kuti anaona ndi kumva zinthu zina, ndipo angayambe kuuza ena kuti zinacitikadi. M’kupita kwa nthawi, anthu amayamba kukokomeza nkhanizo cifukwa cakuti zakambidwa mobwelezabweleza. Ngati Mkristu akufalitsa nkhani zotelo, ndiye kuti akucita cifunilo ca Mdyelekezi, amene ndi “tate wake wa bodza.” Motelo, iye amakhala kuti akufalitsa mabodza a Satana.—Yohane 8:44; 2 Timoteyo 2:16.
21. Kodi zokamba zathu ziyenela kuzikidwa pa ciani?
21 Caciŵili, ngati Mkristu anavutitsidwapo ndi mizimu yoipa m’mbuyomu, ayenela kupewa kuuza Akristu anzake nkhani zimenezo mobwelezabweleza. Cifukwa ciani? Cifukwa cakuti timalimbikitsidwa “kuyang’anitsitsa Mtumiki Wamkulu ndi Wokwanilitsa cikhulupililo cathu, Yesu.” (Aheberi 12:2) Inde, tiyenela kuika maganizo athu pa Kristu, osati pa Satana. Cocititsa cidwi n’cakuti pamene Yesu anali padziko lapansi, sanali kuuza ophunzila ake nkhani zokhudza mizimu yoipa, ngakhale kuti iye akanatha kuwauza zambili ponena za mphamvu zimene Satana ali nazo. M’malo mwake, Yesu anaika maganizo ake pa uthenga wa Ufumu. Conco, motsatila citsanzo ca Yesu ndi ca atumwi, zokamba zathu ziyenela kuzikidwa pa “zinthu zazikulu za Mulungu.”—Machitidwe 2:11; Luka 8:1; Aroma 1:11, 12.
22. Kodi tiyenela kucita ciani kuti ‘kumwamba kukhale cisangalalo coculuka’?
22 Satana amagwilitsila nchito njila zacinyengo zosiyanasiyana, kuphatikizapo kukhulupilila mizimu, kuti aononge ubwenzi wathu ndi Yehova. Komabe, ngati timadana ndi coipa ndi kugwilitsitsa cabwino, sitidzam’patsa mpata Mdyelekezi wakuti aticititse kukhulupilila mizimu mwa njila iliyonse. (Ŵelengani Aefeso 4:27.) Ganizilani za “cisangalalo coculuka” cimene cidzakhala kumwamba ngati tipitiliza kukhala ‘osasunthika polimbana ndi zocita zacinyengo za Mdyelekezi’ mpaka ataonongedwa.—Luka 15:7; Aefeso 6:11.
^ par. 16 Maina ofotokoza zocita za Satana (monga akuti Wotsutsa, Woneneza, Wonyenga, Woyesa, Wabodza) satanthauza kuti iye amadziŵa zimene zili mumtima ndi m’maganizo athu. Koma mosiyana ndi Satana, Yehova amafotokozedwa kuti “amayesa mitima,” ndipo Yesu ‘amafufuza impso ndi mitima.’—Miyambo 17:3; Chivumbulutso 2:23.
^ par. 18 Kuti mudziŵe zambili, onani nkhani yakuti “Kodi Kupima Matenda Kumeneko N’koyenela kwa Inu?” mu Nsanja ya Olonda ya December 15, 1994, patsamba 19 mpaka 22, ndi yakuti “Lingalilo la Baibulo: Kusankha Cithandizo ca Mankhwala—Kodi N’kofunikila?” mu Galamukani! ya January 8, 2001.