Kodi Baibo Mumaiona Bwanji?
Kodi mumaiona ngati . . .
-
buku la anthu?
-
buku la nthano?
-
buku locokela kwa Mulungu?
ZIMENE BAIBO IMANENA
“Malemba onse anauzilidwa ndi Mulungu.”—2 Timoteyo 3:16, Baibulo la Dziko Latsopano.
UBWINO WOKHULUPILILA ZIMENEZI
Mudzapeza mayankho okhutilitsa a mafunso ofunika kwambili onena za umoyo.—Miyambo 2:1-5.
Mudzapeza malangizo othandiza pa umoyo wa tsiku ndi tsiku.—Salimo 119:105.
Mudzakhala ndi ciyembekezo codalilika ca umoyo wabwino mtsogolo.—Aroma 15:4.
KODI TINGAKHULUPILILEDI ZIMENE BAIBO IMANENA?
Inde, pa zifukwa zitatu izi:
-
Nkhani zake n’zogwilizana. Baibo inalembedwa ndi anthu osiyana-siyana okwanila 40 kwa zaka zopitilila 1,600. Ndipo ambili a io sanakumanepo. Koma Baibo yonse ndi yogwilizana, ndipo ili ndi mfundo yaikulu imodzi.
-
Alembi ake anali oona mtima. Olemba mbili kaŵili-kaŵili salemba zoona ngati anthu ao agonjetsedwa. Koma alembi a Baibo anali oona mtima, cakuti analemba zolakwa zao ndi za mtundu wao.—2 Mbiri 36:15, 16; Salimo 51:1-4.
-
Ulosi wake ndi wodalilika. Kukali zaka 200, Baibo inakambilatu kuti mzinda wakale wa Babulo udzaonongedwa. (Yesaya 13:17-22) Inafotokozanso mmene mzinda wa Babulo udzaonongedwela ndi dzina la amene adzaugonjetsa.—Yesaya 45:1-3.
Maulosi ena ambili a m’Baibo naonso anakwanilitsidwa ndendende monga mmene Baibo inanenela. Kodi zimenezi si zimene timayembekezela ndi buku locokela kwa Mulungu?—2 Petulo 1:21.
GANIZILANI FUNSO ILI
Kodi Mau a Mulungu angakuthandizeni kuti mukhale ndi umoyo wabwino kwambili?
Baibo imayankha funso limeneli pa YESAYA 48:17, 18 ndi pa 2 TIMOTEYO 3:16, 17.