Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kalata Yocokela ku Bungwe Lolamulila

Kalata Yocokela ku Bungwe Lolamulila

Okondedwa Abale na Alongo:

Kukonda kwathu Mulungu komanso anthu n’kumene kumatisonkhezela kuti ‘tipite . . . na kukaphunzitsa anthu a mitundu yonse, kuti akhale ophunzila na kuwabatiza.’ (Mat. 28:19, 20; Maliko 12:28-31) Cikondi copanda dyela n’camphamvu zedi. Cimafika pa mitima ya anthu a ‘maganizo abwino amene angawathandize kukapeza moyo wosatha.’—Mac. 13:48.

Kumbuyoku, tinali kulimbikila kwambili kuloŵeza maulaliki pa mtima na kugaŵila zofalitsa. Koma lomba, tifuna tiyesetse kukulitsa luso la kuceza na anthu. Tikufuna kuonetsa kuti anthu timawakonda pokambilana nawo nkhani zimene zimawakhudza iwo. Cofunikila maka-maka ni kukhala okonzeka kusintha, komanso kuganizila bwino nkhani imene ingayenelele munthu aliyense payekha-payekha. Kodi bulosha ino idzatithandiza bwanji kucita zimenezi?

Bulosha ino ili na maphunzilo 12 ofotokoza makhalidwe amene tiyenela kukulitsa kuti tithe kukonda anthu na kupanga ophunzila. Phunzilo lililonse lazikika pa nkhani ya m’Baibo imene ionetsa mmene Yesu, kapena mmodzi wa Akhristu oyambilila, anaonetsela khalidwe limenelo mu ulaliki. Colinga cathu ulendo uno si kuloŵeza pa mtima maulaliki ayi, koma kupeza njila zoonetsela anthu kuti timawakonda. Ngakhale kuti lililonse la makhalidwe amenewo ni lofunika pa mbali zonse za ulaliki wathu, tidzaona maka-maka mmene makhalidwe ena alili ofunika kwambili poyambitsa makambilano, pa ulendo wobwelelako, komanso potsogoza phunzilo la Baibo.

Poŵelenga phunzilo lililonse, ganizilani mwakuya mmene mungaonetsele khalidwe limenelo poceza na anthu kumene mumakhala. Yesetsani kuzamitsa cikondi canu kwa Yehova, komanso kwa anthu. Cikondi cimeneco, kuposa ngakhale luso lenilenilo, n’cimene cidzakuthandizani kwambili kukwanilitsa colinga canu ca kupanga ophunzila.

Tikucitenga kukhala mwayi waukulu zedi kugwila nanu nchito imeneyi. (Zef. 3:9) Tingoti Yehova akudalitseni mowilikiza, pamene mukukonda anthu mosalekeza na kupanga ophunzila!

Ndife abale anu,

Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova