KUPANGA OPHUNZILA
PHUNZILO 12
Kulimba Mtima
Mfundo Yaikulu: “Mafuta ndi zofukiza zonunkhila n’zimene zimasangalatsa mtima, cimodzimodzinso kukoma kwa mnzako cifukwa ca malangizo ake ocokela pansi pa mtima.”—Miy. 27:9.
Mmene Yesu Anaonetsela Khalidwe Limeneli
1. Tambani VIDIYO, kapena ŵelengani Maliko 10:17-22. Kenaka ganizilani pa mafunso otsatilawa:
Tiphunzilaponji kwa Yesu?
2. Ophunzila athu tizilankhula nawo mwacikondi komanso mosapita m’mbali kuti apite bwino patsogolo kuuzimu.
Tengelani Citsanzo ca Yesu
3. Thandizani wophunzila wanu kudziikila zolinga na kuzikwanilitsa.
-
Seŵenzetsani mbali yakuti “Colinga” m’buku la Kondwelani na Moyo Kwamuyaya!
-
Thandizani wophunzila wanu kudziŵa zimene ayenela kucita kuti akwanilitse zolinga zing’ono-zing’ono komanso zikulu-zikulu.
4. Zindikilani zopinga zimene zingam’bweze kumbuyo, ndipo m’thandizeni kuti azigonjetse.
-
-
‘Ngati wophunzila wanga sakupita patsogolo kuti akabatizike, cikum’pinga n’ciyani?’
-
‘Nanga ningam’thandize bwanji?’
-
-
Pemphelelani kulimba mtima kuti mukathe kukambilana naye, mwacikondi komabe mosapita m’mbali, zimene afunikila kucita.
5. Asiyeni maphunzilo amtatakuya osapita patsogolo.
-
Kuti mudziŵe ngati wophunzila wanu akupita patsogolo kapena ayi, dzifunseni kuti:
-
‘Kodi amagwilitsa nchito zimene akuphunzila?’
-
‘Kodi amapezeka ku misonkhano ya mpingo, ndipo amauzako ena zimene amaphunzila?’
-
‘Popeza waphunzila kwa nthawi ndithu, kodi lomba akufuna kukhala Mboni?’
-
-
Ngati wophunzila Baibo sakufuna kupita patsogolo, citani izi:
-
M’pempheni kuti aganizilepo pa cimene cikumulepheletsa.
-
Mosamala komanso mwaubwino, m’fotokozeleni cifukwa cake simudzapitiliza kuphunzila naye.
-
Muuzeni zofunikila kugwililapo nchito ngati akufuna kuti m’tsogolo mukayambilenso kuphunzila naye.
-
ONANINSO MALEMBA AWA
Sal. 141:5; Miy. 25:12; 27:6; 1 Akor. 9:26; Akol. 4:5, 6