KUYAMBITSA MAKAMBILANO
PHUNZILO 2
Kukamba Mwacibadwa
Mfundo Yaikulu: “Mawu onenedwa pa nthawi yoyenela ndi abwino kwambili!”—Miy. 15:23.
Mmene Filipo Anacitila Zimenezi
1. Tambani VIDIYO, kapena ŵelengani Machitidwe 8:30, 31. Kenaka, ganizilani pa mafunso otsatilawa:
Tiphunzilaponji kwa Filipo?
2. Ngati tilankhula mwacibadwa, munthuyo adzakhala womasuka, komanso adzamvetsela uthenga wathu mosavuta.
Tengelani Citsanzo ca Filipo
3. Khalani oyang’anitsitsa. Nkhope ya munthu, manja ake, ngakhale thupi lake, zingatiuze zambili za munthuyo. Kodi aoneka na cidwi cofuna kuceza nanu? Mungayambe nkhani ya m’Baibo mongom’funsa kuti, “Kodi mudziŵa kuti . . . ?” Pewani kuumiliza munthu woonekelatu kuti safuna kukambilana naye.
4. Khalani woleza mtima. Musaumilizike kungoyamba na mfundo ya m’Baibo. Yembekezani mpata woyenela kuti muiloŵetsepo mosavutikila. Mwinanso mpatawo ungadzapezeke bwino pa ulendo wina wodzaceza naye.
5. Khalani wokonzeka kusintha. N’kutheka makambilano anu angaloŵele kwina kumene simunayembekezele. Zikatelo, kambilanani naye mfundo ina imene angagwilizane nayo, na kusiya imene munaikonzekela.
ONANINSO MALEMBA AWA
Mlal. 3:1, 7; 1 Akor. 9:22; 2 Akor. 2:17; Akol. 4:6