Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

KUYAMBITSA MAKAMBILANO

Luka 19:1-7

PHUNZILO 6

Kucotsa Mantha

Kucotsa Mantha

Mfundo Yaikulu: “Tinalimba mtima mothandizidwa ndi Mulungu wathu ndipo tinalankhula kwa inu uthenga wabwino.”—1 Ates. 2:2.

Mmene Yesu Anacitila Zimenezi

1. Tambani VIDIYO, kapena ŵelengani Luka 19:1-7. Kenaka ganizilani pa mafunso otsatilawa:

  1.    Cingakhale ciyani cinapangitsa anthu ena kum’pewa Zakeyu?

  2.   Koma n’cifukwa ciyani Yesu anamulalikilabe?

Tiphunzilaponji kwa Yesu?

2. Tiyenela kucotsa mantha kuti tilalikile uthenga wa Ufumu mosayang’ana nkhope.

Tengelani Citsanzo ca Yesu

3. Dalilani Yehova. Mzimu wa Mulungu unapatsa Yesu mphamvu kuti alalikile. Inunso ungakupatseni mphamvu. (Mat. 10:19, 20; Luka 4:18) M’pempheni Yehova akucotseni mantha kuti muzitha kuwalalikila ngakhale anthu aja amene mungacite nawo mantha.—Mac. 4:29.

4. Pewani kuweluzilatu anthu. Anthu ena tingadodome kuwalalikila cifukwa ca maonekedwe awo, kulemekezeka kwawo, cuma, kuchuka, kapena cipembedzo cawo. Koma kumbukilani izi:

  1.    Yehova na Yesu amaona zili mu mtima; ife sitingathe.

  2.   Yehova angathandize munthu aliyense.

5. Khalani wopanda mantha komabe wosamala. (Mat. 10:16) Pewani mikangano. Mwaulemu, thetsani makambilano anu ngati munthuyo safuna kumvetsela uthenga wabwino, kapena mukaona kuti pangacitike coipa.—Miy. 17:14.

ONANINSO MALEMBA AWA

Mac. 4:31; Aef. 6:19, 20; 2 Tim. 1:7