Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Zakumapeto B

Kodi Muwathetse Makambilano?

Kodi Muwathetse Makambilano?

Ngati munthu wina wakamba moona mtima maganizo otsutsa mfundo yathu, timakhalabe ofunitsitsa kukambilana naye. Timakondwela kukamba ni anthu a ‘maganizo abwino amene angawathandize kukapeza moyo wosatha.’—Mac. 13:48.

Koma bwanji ngati munthuyo ni wokwiya, akufuna mkangano, kapena safuna kukamba naye pali pano? Mwa mtendele komanso mwaulemu thetsani makambilano anu. (Miy. 17:14) Siyanani naye mwaulemu. Potelo, mungasiye khomo lili citsegukile kaamba ka makambilano abwino a m’tsogolo.—1 Pet. 2:12.