PHUNZILO 1
Kodi Baibo Ingakuthandizeni Bwanji pa Umoyo Wanu?
Tonse timafuna kudziŵa mayankho pa mafunso okhudza moyo, mavuto, imfa, komanso za kutsogolo. Timakhalanso na nkhawa zina, monga mmene tingapezele ndalama kapena mmene tingakhalile na cimwemwe m’banja. Anthu ambili apeza kuti Baibo yawathandiza kupeza mayankho pa mafunso ofunika pa umoyo, komanso yawapatsa ulangizi wothandiza kwambili. Ndithudi, Baibo ingathandize munthu aliyense.
1. Kodi ni mafunso ena ati amene Baibo imayankha?
Baibo imayankha mafunso ofunika kwambili aya: Kodi moyo unayamba bwanji? Nanga colinga ca moyo n’ciyani? N’cifukwa ciyani anthu osalakwa nawonso amavutika? Kodi munthu akamwalila amayenda kuti? Popeza tonse mtendele timaufuna, n’cifukwa ciyani padziko pakucitika nkhondo zambili conco? Kodi n’ciyani cidzacitike padziko lapansi m’tsogolo? Baibo imatilimbikitsa kufufuza mayankho a mafunso amenewa. Ndipo pali anthu mamiliyoni amene apeza mayankho okhutilitsa kwambili.
2. Kodi Baibo ingatithandize bwanji kukondwela na umoyo wathu?
Baibo imatipatsa malangizo anzelu. Mwacitsanzo, imaphunzitsa mabanja mmene angapezele cimwemwe ceni-ceni. Imatilangizanso zocita tikakhala na nkhawa, komanso mmene tingakondwele na nchito yathu. Mudzadziŵa zimene Baibo imaphunzitsa pa nkhani zimenezi, komanso zina zambili pamene tikambitsilana za m’buku lino. Inunso mudzavomeleza kuti “malemba onse [zonse zolembedwa m’Baibo] ndi . . . opindulitsa.”—2 Timoteyo 3:16.
Buku lino silitenga malo a Baibo. Koma lidzakulimbikitsani kuti muziiŵelenga Baibo kuti muimvetsetse. Conco, muziŵelenga malemba amene aikidwa m’maphunzilo ano, ndiponso onani mmene akugwilizanila na zimene mukuphunzila.
KUMBANI MOZAMILAPO
Ganizilani mmene Baibo yathandizila anthu, mmenenso mungasangalalile poiŵelenga, komanso cifukwa cake kuli kofunika kuti wina akuthandizeni kuimvetsetsa.
3. Baibo ingatiunikile njila
Baibo ili monga toci yowala bwino. Ingatithandize kupanga zisankho zanzelu, na kudziŵilatu zimene zidzacitika kutsogolo.
Ŵelengani Salimo 119:105, na kukambilana mafunso aya:
-
Kodi mlembi wa salimo ili anali kuiona bwanji Baibo?
-
Nanga inu mumaiona bwanji Baibo?
4. Baibo ikhoza kuyankha mafunso athu
Mzimayi wina anakamba kuti Baibo inayankha mafunso amene anam’vutitsa maganizo kwa zaka zambili. Tambani VIDIYO, kenako kambilanani mafunso aya.
-
Kodi mzimayi wa mu vidiyo iyi anali na mafunso otani?
-
Kodi kuphunzila Baibo kunam’thandiza bwanji?
Baibo imatilimbikitsa kufunsa mafunso. Ŵelengani Mateyu 7:7, na kukambilana funso ili:
-
Kodi muli na mafunso abwanji amene mungakonde kupeza mayankho ake m’Baibo?
5. Kuŵelenga Baibo kungakukondweletseni
Anthu ambili amakondwela kuŵelenga Baibo, ndipo kumawapindulila. Tambani VIDIYO, kenako kambilanani mafunso aya.
-
Mu vidiyo iyi, kodi acinyamatawo nkhani ya kuŵelenga anali kuiona bwanji?
-
Nanga n’cifukwa ciyani kuŵelenga Baibo lomba amakuona mosiyana?
Baibo imanena kuti ingatipatse malangizo otitonthoza, imatipatsanso ciyembezo. Ŵelengani Aroma 15:4, na kukambilana funso ili:
-
Pamene Baibo imalonjeza za citonthozo na kupeleka ciyembekezo, kodi zimakukopani mtima?
6. Ena angatithandize kuimvetsetsa Baibo
Kuwonjezela pa kuŵelenga Baibo paokha, ambili apeza kuti n’zothandizanso kuikambilana na munthu wina. Ŵelengani Machitidwe 8:26-31, na kukambilana funso ili:
-
Kodi n’ciyani cingatithandize kuimvetsetsa Baibo?—Onani mavesi 30 na 31.
ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Kuphunzila Baibo n’kutaya cabe nthawi.”
-
Nanga inu muganiza bwanji? Cifukwa ciyani?
CIDULE CAKE
Baibo imatipatsa ulangizi wothandiza pa umoyo, imayankha mafunso ofunika kwambili, ndiponso imapeleka citonthozo na ciyembekezo.
Mafunso Obweleza
-
Kodi m’Baibo tingapezemo ulangizi wotani wothandiza?
-
Nanga ni mafunso ena ati amene Baibo imayankha?
-
N’ciyani cimene mungakonde kuphunzila m’Baibo?
FUFUZANI
Ganizilani mmene ulangizi wa m’Baibo ulili wothandiza masiku ano.
“Ziphunzitso za m’Baibo N’zothandiza Nthawi Zonse” (Nsanja ya Mlonda Na. 1 2018)
Onani mmene Baibo inathandizila munthu amene anali na mtima wapacala kuyambila ali wamng’ono.
Onani malangizo othandiza pa umoyo wa banja.
Onani mmene Baibo imaunikila bwino za amene akulamulila dziko lapansi, zimene anthu ambili sadziŵa.
N’cifukwa Ciani Muyenela Kuphunzila Baibulo? —Vidiyo Yonse (3:14)