PHUNZILO 16
Kodi Yesu Anacita Zotani Ali Padziko Lapansi?
Anthu ambili akaganiza za Yesu, m’maganizo mwawo amaona mwana wakhanda ali modyelamo ziweto, mmeneli wanzelu, kapena munthu wopacikidwa pa mtengo. Koma tikapenda umoyo wake ali padziko lapansi, tingaphunzile zambili. M’phunzilo lino, tiona zinthu zina zofunika kwambili zimene Yesu anacita, komanso mmene zingakuthandizileni.
1. Kodi nchito yofunika kwambili kwa Yesu inali iti?
“Kukalengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu,” ndiyo inali nchito yofunika kwambili kwa Yesu. (Ŵelengani Luka 4:43.) Analalikila uthenga wabwino wakuti Mulungu adzakhazikitsa ufumu, kapena kuti boma, limene lidzacotsapo mavuto onse a anthu. a Popanda kutopa, Yesu analalikila uthenga umenewu kwa zaka zitatu na hafu.—Mateyu 9:35.
2. Kodi n’colinga canji cimene Yesu anacitila zozizwitsa?
Baibo imachula “zodabwitsa komanso . . . zizindikilo, zimene Mulungu anacita . . . kudzela mwa [Yesu].” (Machitidwe 2:22) Mwa mphamvu ya Mulungu, Yesu anakwanitsa kukhalitsa bata cimphepo camphamvu, kudyetsa anthu masauzande, kucilitsa odwala, ngakhale kuukitsa akufa. (Mateyu 8:23-27; 14:15-21; Maliko 6:56; Luka 7:11-17) Zozizwitsa za Yesu zinaonetselatu poyela kuti Mulungu ndiye anamutuma. Zinaonetsanso kuti Yehova ali na mphamvu zocotsapo mavuto athu onse.
3. Kodi tingaphunzile ciyani pa umoyo wa Yesu?
Yesu anali womvela kwa Yehova pa ciliconse. (Ŵelengani Yohane 8:29.) Ngakhale kuti ambili anali kumutsutsa, Yesu anakhulupilikabe mpaka imfa, akucita zonse zimene Atate wake anamuuza. Iye anaonetsa kuti n’zotheka ndithu anthu kutumikila Mulungu mokhulupilika, ngakhale akumane na zovuta. Conco, Yesu anatisiyila citsanzo kuti titsatile mapazi ake.—1 Petulo 2:21.
KUMBANI MOZAMILAPO
Onani mmene Yesu analalikilila uthenga wabwino na kucita zozizwitsa.
4. Yesu anali kuuza anthu uthenga wabwino
Yesu anayenda mitunda ya makilomita ambili-mbili m’misewu yafumbi, akulalikila uthenga wabwino mmene akanathela. Ŵelengani Luka 8:1, kenako kambilanani mafunso aya:
-
Kodi Yesu anali kungolalikila kwa anthu amene anali kubwela kudzasonkhana kwa iye kuti amvetsele?
-
Kodi Yesu anacita khama motani kuti azipeza anthu?
Mulungu anakambilatu kuti Mesiya adzalalikila uthenga wabwino. Ŵelengani Yesaya 61:1, 2, na kukambilana mafunso aya:
-
Kodi Yesu anaukwanilitsa motani ulosi umenewu?
-
Kodi muganiza anthu masiku anonso akufunikila kumvela uthenga wabwino umenewu?
5. Yesu anaphunzitsa mfundo zothandiza
Pambali pa kulalikila uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu, Yesu anaphunzitsanso mfundo zothandiza pa umoyo. Onani zitsanzo zingapo pa Ulaliki wake wa pa Phili. Ŵelengani Mateyu 6:14, 34 komanso 7:12, kenako kambilanani mafunso aya:
-
Kodi m’mavesi amenewa Yesu anapeleka uphungu wanji wothandiza?
-
Kodi muganiza uphungu umenewu ukali wothandiza masiku ano?
6. Yesu anacita zozizwitsa
Mwa mphamvu zocokela kwa Yehova, Yesu anacita zozizwitsa zambili. Kuti muone citsanzo cimodzi, ŵelengani Maliko 5:25-34, kapena tambani VIDIYO. Ndiyeno kambilanani mafunso aya.
-
Mu vidiyo iyi, kodi mzimayiyo anakhulupilila ciyani mumtima mwake?
-
Nanga cakukondweletsani n’ciyani pa cozizwitsa cimeneci?
Ŵelengani Yohane 5:36, kenako kambilanani funso ili:
-
Kodi zozizwitsa za Yesu ‘zinacitila umboni,’ kapena zinatsimizikila ciyani za iye?
Kodi mudziŵa?
Zambili zimene tikudziŵa pa Yesu zimacokela m’mabuku anayi a m’Baibo ochedwa Mauthenga Abwino—Mateyu, Maliko, Luka, komanso Yohane. Wolemba Uthenga Wabwino aliyense anaphatikizamo mfundo zosiyanako zokhudza Yesu. Mfundo zimenezi zimathandizila kupeleka cithunzi cabwino ca umoyo wake.
-
MATEYU
ndiye anayamba kulemba Uthenga Wabwino. Anaunika kwambili ziphunzitso za Yesu, maka-maka zimene Yesu anaphunzitsa zokhudza Ufumu wa Mulungu.
-
MALIKO
ndiye analemba Uthenga Wabwino waufupi kwambili. Anafotokoza zinthu zocititsa cidwi ngako.
-
LUKA
amagogomeza kufunika kwa pemphelo, na mmene Yesu anali kulemekezela azimayi.
-
YOHANE
amaunika kwambili makhalidwe a Yesu posimba za makambilano ambili pakati pa Yesu na mabwenzi ake apamtima, komanso anthu ena.
ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Yesu ni Mulungu Wamphamvuzonse.”
-
Nanga inu muona bwanji?
CIDULE CAKE
Yesu analalikila za Ufumu wa Mulungu, anacita zozizwitsa, ndipo anali womvela kwa Yehova pa ciliconse.
Mafunso Obweleza
-
Kodi nchito yofunika kwambili kwa Yesu padziko lapansi inali iti?
-
Nanga zozizwitsa za Yesu zimatsimikizila ciyani za iye?
-
Ni mfundo zotani zothandiza pa umoyo zimene Yesu anaphunzitsa?
FUFUZANI
Kodi nkhani yaikulu imene Yesu anali kulalikila inali nkhani yanji?
“Yesu Anali Kuona Kuti Ufumu wa Mulungu Ni Wofunika Kwambili” (Nsanja ya Mlonda, October 1, 2014)
Onani cifukwa cake tiyenela kukhulupilila kuti zozizwitsa za Yesu zinacitikadi.
“Kodi pa Zozizwitsa za Yesu Mungaphunzilepo Ciyani?” (Nsanja ya Mlonda, July 15, 2004)
Ŵelengani za mmene citsanzo ca Yesu ca kudzipeleka pofuna kuthandiza anthu cinakhudzila mwamuna wina.
“N’nali Munthu Wodzikonda Kwambili” (Nsanja ya Mlonda, October 1, 2014)
Onani zocitika zikulu-zikulu mu utumiki wa Yesu mwa tsatanetsane wake.
10 “Zocitika Zazikulu Paumoyo wa Yesu wa Padziko” (Buku Lothandiza Pophunzila Mau a Mulungu, 4-B)
a M’maphunzilo 31-33, tidzakambilana zambili zokhudza Ufumu wa Mulungu.