Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 21

Kodi Uthenga Wabwino Umalalikidwa Motani?

Kodi Uthenga Wabwino Umalalikidwa Motani?

Mwa Ufumu wake, Yehova adzacotsapo mavuto athu onse posacedwa. Uthenga umenewu ni wofunika kwambili kuti munthu aliyense aumve. Ndiye cifukwa cake Yesu analamula otsatila ake kuti akalalikile uthenga umenewu kwa munthu wina aliyense! (Mateyu 28:19, 20) Kodi Mboni za Yehova zalabadila motani lamulo la Yesu limeneli?

1. Kodi Mateyu 24:14 ikukwanilitsidwa bwanji masiku ano?

Yesu ananenelatu kuti: “Uthenga wabwino uwu wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi.” (Mateyu 24:14) Mboni za Yehova zimasangalala kugwila nawo nchito yofunika kwambili imeneyi. Uthenga wabwino umenewu timaulalikila padziko lonse m’zinenelo zopitilila 1,000. Kuti nchito yaikulu imeneyi icitike bwino, pamafunika khama komanso dongosolo. Ndipo siingacitike popanda thandizo la Yehova.

2. Kodi timalalikila kwa anthu m’njila ziti?

Timalalikila kulikonse kumene tapeza anthu. Motengela Akhristu oyambilila, ifenso timalalikila “nyumba ndi nyumba.” (Machitidwe 5:42) Mwa njila yadongosolo imeneyi, timatha kulalikila mamiliyoni a anthu caka ciliconse. Popeza nthawi zina anthu sapezeka panyumba, timalalikilanso m’malo ena opezekako anthu. Nthawi zonse timafuna-funa mipata youzako anthu za Yehova na colinga cake.

3. Kodi ndani ali na udindo wolalikila uthenga wabwino?

Akhristu onse enieni ni udindo wawo kulalikila uthenga wabwino kwa ena. Ndipo udindo wathu umenewu sitiutengela kucala. Timalalikila malinga na mmene zinthu zilili pa umoyo wathu, podziŵa kuti miyoyo ya anthu ili paciswe. (Ŵelengani 1 Timoteyo 4:16.) Nchito imeneyi timaigwila popanda malipilo, cifukwa Baibo imanena kuti: “Munalandila kwaulele, patsani kwaulele.” (Mateyu 10:7, 8) Si aliyense amene amalandila uthenga wathu. Koma sitileka cifukwa kulalikila ni mbali ya kulambila kwathu, ndipo kumakondweletsa Yehova.

KUMBANI MOZAMILAPO

Dziŵani zambili zokhudza nchito ya Mboni za Yehova yolalikila padziko lonse, na mmene Yehova amatithandizila.

4. Timagwila nchito molimbika kuti tifikile anthu onse

A Mboni za Yehova amacita zonse zotheka kuti alalikile uthenga wabwino kulikonse. Tambani VIDIYO, kenako kambilanani funso lotsatila.

  • N’ciyani cikukucititsani cidwi poona mmene Mboni za Yehova zimagwilila nchito yawo yolalikila?

Ŵelengani Mateyu 22:39, komanso Aroma 10:13-15, na kukambilana mafunso aya:

  • Kodi nchito yathu yolalikila imaonetsa bwanji kuti timakonda anthu anzathu?

  • Kodi Yehova amawaona bwanji amene amalalikila uthenga wabwino?—Onani vesi 15.

5. Ndife anchito anzake a Mulungu

Zocitika zambili zimaonetsa kuti Yehova ndiye akutsogolela nchito yathu. Mwacitsanzo, m’bale wina ku New Zealand, dzina lake Paul, tsiku lina masana anapeza mzimayi wina panyumba pake polalikila khomo na khomo. M’maŵa tsiku limenelo, mzimayiyo anali atapemphela kwa Mulungu akumachula dzina lakuti Yehova, na kum’pempha kuti munthu wina akam’thandize kudziŵa Yehova. M’bale Paul anati: “Patangopita maola atatu, n’nagogoda pakhomo pake.”

Ŵelengani 1 Akorinto 3:9, na kukambilana funso ili:

  • Kodi zocitika monga ici ca ku New Zealand, zionetsa bwanji kuti Yehova ndiye amatsogolela nchito yathu yolalikila?

Ŵelengani Machitidwe 1:8, na kukambilana funso ili:

  • N’cifukwa ciyani tifunikila thandizo la Yehova kuti tikwanilitse utumiki wathu?

Kodi mudziŵa?

Mlungu uliwonse pa misonkhano yathu ya mkati mwa mlungu, timalandila maphunzilo a kalalikidwe. Ngati munapezekapo pa misonkhano imeneyi, kodi muganiza bwanji za maphunzilo amenewo?

6. Timamvela lamulo la Mulungu lakuti tizilalikila

Pa nthawi ya Akhristu oyambilila, adani a Yesu anayesa kuletsa otsatila ake kulalikila. Koma Akhristu oyambililawo anateteza ufulu wawo wolalikila mwa kutsimikizila kuti nchito yawo yolalikila niyololeka mwalamulo. (Afilipi 1:7) Masiku anonso Mboni za Yehova zimacita cimodzi-modzi. a

Ŵelengani Machitidwe 5:27-42, na kukambilana funso ili:

  • N’cifukwa ciyani sitingaleke kulalikila?—Onani mavesi 2938, komanso 39.

MUNTHU WINA ANGAFUNSE KUTI: “N’cifukwa ciyani Mboni za Yehova zimalalikila khomo na khomo?

  • Kodi inu mungayankhe bwanji?

CIDULE CAKE

Yesu analamula otsatila ake kuti akalalikile uthenga wabwino ku mitundu yonse. Ndipo Yehova amathandiza anthu ake kugwila nchito imeneyi.

Mafunso Obweleza

  • Kodi uthenga wabwino umalalikidwa motani padziko lonse?

  • Mwa kugwila nchito yathu yolalikila, timaonetsa bwanji kuti timakonda anthu?

  • Kodi muganiza kuti nchito yolalikila ingakhale yopatsa cimwemwe? Cifukwa ciyani?

Colinga

FUFUZANI

Onani mmene Mboni za Yehova zimalalikilila m’matauni akulu-akulu.

Ntchito Yapadera Yolalikira M’malo Opezeka Anthu Ambiri ku Paris (5:11)

Kodi Mboni za Yehova zimawathandiza bwanji anthu othaŵa kwawo?

Kuthetsa Ludzu Lauzimu la Othaŵa Kwawo (5:59)

Mvetselani kwa eni ake cifukwa cake utumiki wa nthawi zonse umawapatsa cimwemwe.

Ndimasangalala Kuti Ndinasankha Kutumikira Yehova (6:29)

Ŵelengani za zipambano zapadela za m’makhoti zimene zapititsa patsogolo uthenga wabwino.

“Alaliki a Ufumu Amapeleka Milandu Yao ku Khoti” (Ufumu wa Mulungu Ukulamulila!, Nkhani 13)

a Mulungu ndiye anatipatsa lamulo lakuti tizilalikila. Conco, Mboni za Yehova sizifunikila cilolezo ca boma la anthu kuti tilalikile uthenga wabwino.