PHUNZILO 22
Kodi Ena Mungawauzeko Bwanji Uthenga Wabwino?
Pamene mukuphunzila coonadi ca m’Baibo, mu mtima mwanu munganene kuti: ‘Izi n’zofunika kuti munthu aliyense amveko!’ Ndipo n’zoona, munthu aliyense afunika kucidziŵa coonadi ca m’Baibo. Koma mungacite mantha kuti muuzeko ena zimene mumaphunzila. Tiyeni tikambilane mmene mungacotsele mantha amenewo, kuti muyambe kuuzako ena uthenga wabwino wa m’Baibo.
1. Kodi anthu amene mumadziŵana nawo mungawauzeko bwanji zimene mukuphunzila?
Ophunzila a Yesu anakamba kuti: “Sitingaleke kulankhula zinthu zimene tinaziona ndi kuzimva.” (Machitidwe 4:20) Mfundo za coonadi zimene iwo anamva kwa Yesu anazikonda ngako, cakuti anali ofunitsitsa kuuzako munthu aliyense. Kodi inunso mumamva conco? Ngati n’telo, yesani kupeza mipata kuti mwaulemu, muziuzako acibale anu na mabwenzi anu zimene mukuphunzila.—Ŵelengani Akolose 4:6.
Njila zimene mungayambilepo
-
Pamene muceza na acibale anu, yambitsani nkhani ya m’Baibo ponena kuti: “Wiki ino naphunzila Mfundo yabwino kwambili.”
-
Ngati mnzanu akudwala kapena ali na nkhawa, muŵelengelenkoni lemba.
-
Anzanu a kunchito akakufunsani kuti kodi wikendi inali bwanji, auzenkoni zimene munaphunzila pa phunzilo lanu la Baibo, kapena pa msonkhano wa mpingo.
-
Onetsani mabwenzi anu webusaiti ya jw.org.
-
Muzipemphako anthu ena kukhalapo pa phunzilo lanu la Baibo, kapena aonetseni mmene angapemphele pa jw.org kuti wina aziphunzila nawo Baibo.
2. N’cifukwa ciyani kudziikila colinga cakuti mukayambe kulalikila pamodzi na mpingo n’kofunika?
Ophunzila a Yesu sanali kungolalikila uthenga wabwino kwa amene anali kuŵadziŵa. Yesu anawatumiza “aŵiliaŵili kuti atsogole kupita mumzinda ndi malo alionse” kukalalikila. (Luka 10:1) Ulaliki wokonzedwa mwadongosolo umenewo, unapatsa mwayi anthu ambili kumva uthenga wabwino. Kulalikila capamodzi nakonso kunathandiza ophunzila a Yesu kugwila nchitoyo mosangalala. (Luka 10:17) Kodi inunso simungadziikile colinga cakuti mukayambe kulalikila pamodzi na mpingo?
KUMBANI MOZAMILAPO
Onani mmene mungacepetsele mantha, kuti mukhale na cimwemwe pouzako ena uthenga wabwino.
3. Yehova adzakuthandizani
Ena amene amafuna kulalikila amacita mantha poganizila mmene anthu ena angaŵaonele, kapena zimene angakambe.
-
Kodi mumacita mantha kuuzako ena zimene mumaphunzila? N’cifukwa ciyani mwayankha conco?
Tambani VIDIYO, kenako kambilanani funso lotsatila:
-
Kodi acinyamata amenewa anagonjetsa bwanji mantha awo?
Ŵelengani Yesaya 41:10, na kukambilana funso ili:
-
Mukacita mantha kuti mulalikile, kodi pemphelo lingakuthandizeni bwanji?
Kodi mudziŵa?
Mboni za Yehova zambili panthawi ina sizinaganizepo kuti zidzakwanitsa kulalikila kwa ena uthenga wabwino. Mwacitsanzo, cifukwa Sergey anali na vuto la kusadzidalila, cinali cinthu comuvuta kukamba na ŵanthu. Koma ataphunzila Baibo, iye anati: “Olo kuti n’nali na mantha, n’nayamba kuuzako ena zimene n’nali kuphunzila. Ndipo n’nadabwa kuona kuti kuuzako ena za m’Baibo, kunanithandiza kukhala wodzidalila. Kunanithandizanso kulimbitsa cikhulupililo canga.”
4. Khalani aulemu
Pouzako ena uthenga wabwino, musamangoganizila zimene mufuna kukamba, muziganilanso mozikambila. Ŵelengani 2 Timoteyo 2:24, komanso 1 Petulo 3:15, na kukambilana mafunso aya:
-
Kodi mungaseŵenzetse bwanji mfundo zili pa mavesi aya pouzako ena za m’Baibo?
-
Ngati acibale anu ena kapena anzanu sakuvomeleza zimene mukukamba, kodi muyenela kucita ciyani? Ndipo muyenela kupewa kucita ciyani?
-
N’cifukwa ciyani ni bwino kukambilana nawo mwaulemu, m’malo mowaumiliza kuti akhulupilile zimene mukukamba?
5. Kuuzako ena uthenga wabwino kumatipatsa cimwemwe
Yehova anapatsa Yesu nchito yolengeza uthenga wabwino. Kodi Yesu anaiona motani nchito imeneyo? Ŵelengani Yohane 4:34, na kukambilana mafunso aya:
-
Kudya cakudya cabwino kumatipatsa thanzi, ndipo timakhala na moyo wosangalala. N’cifukwa ciyani Yesu anayelekezela kucita cifunilo ca Mulungu—cophatikizapo kuuzako ena uthenga wabwino—na kudya cakudya?
-
Kodi muganiza mudzapeza mapindu otani mukamauzako ena uthenga wabwino?
Maganizo othandiza
-
Pa msonkhano wa mkati mwa mlungu, muziona njila zimene mungatengeleko zoyambitsila makambilano.
-
Ganizilani zolembetsa mu sukulu ya msonkhano wa mkati mwa mlungu. Nkhani za m’sukulu zingakuthandizeni kukhala wokonzeka kuuzako ena zimene mukuphunzila.
-
Seŵenzetsani mbali za m’buku lino zakuti “Anthu Ena Amakamba Kuti” kapena “Munthu Wina Angafunse Kuti,” pofuna kuyesela mmene mungayankhile mafunso amene anthu amakonda kufunsa, kapena mawu ofala oyesa kukanila ulaliki.
MUNTHU WINA ANGAFUNSE KUTI: “Umoyo uyenda bwanji?”
-
Mungaseŵenzetse bwanji mpata umenewo kumuuzako zimene munaphunzila pa phunzilo lanu la Baibo?
CIDULE CAKE
Kuuzako ena uthenga wabwino kumabweletsa cimwemwe, ndipo mudzadabwa kuona kuti kucita zimenezi n’kosavuta.
Mafunso Obweleza
-
N’cifukwa ciyani timauzako ena uthenga wabwino?
-
Nanga mungacite bwanji zimenezi mwaulemu?
-
Kodi mungathetse bwanji mantha amene mungakhale nawo mukaganizila zolalikila?
FUFUZANI
Ganizilani njila zinayi zosavuta zimene mungauzileko wina uthenga wabwino pomugaŵila kakhadi koloŵela pa webusaiti yathu.
Maulaliki a Citsanzo Ogaŵila Khadi Yongenela pa Webusaiti Yathu (1:43)
Dziŵani makhalidwe anayi amene angakuthandizeni kuuzako ena uthenga wabwino.
“Kodi Ndimwe Wokonzeka Kukhala Msodzi wa Anthu?” (Nsanja ya Mlonda, September 2020)
Onani citsanzo ca m’Baibo cimene cingakuthandizeni kukhala wolimba mtima polengeza uthenga wabwino, olo mukhale wacicepele.
Dziŵani mmene mungauzileko abululu ŵanu uthenga wa m’Baibo amene sanaphunzilepo za Yehova.
“Kodi Tingathandize Bwanji Acibale Omwe Si Mboni?” (Nsanja ya Mlonda, March 15, 2014)