PHUNZILO 34
Kodi Tingaonetse Bwanji Kuti Yehova Timamukonda?
Kucokela pamene munayamba kuphunzila Baibo, kodi muona kuti cikondi canu pa Yehova cikukula? Kodi mungakonde kupitiliza kulimbitsa ubwenzi wanu na iye? Ngati n’telo, kumbukilani kuti pamene Yehova akuona cikondi canu cikukula pa iye, adzakukondani kwambili na kukusamalilani. Koma mungaonetse bwanji kuti mumamukonda?
1. Kodi timamuonetsa bwanji Yehova kuti timamukonda?
Timaonetsa cikondi cathu kwa Yehova mwa kumumvela. (Ŵelengani 1 Yohane 5:3.) Iye sakakamiza munthu aliyense kumumvela. Amafuna munthu aliyense asankhe yekha kumumvela kapena kusamumvela. N’cifukwa ciyani amatelo? Cifukwa Yehova amafuna kuti tizimumvela “mocokela pansi pa mtima.” (Aroma 6:17) Kunena kwina, iye safuna kuti muzimumvela mokakamizika ayi, koma cifukwa cakuti mumamukonda. Zigawo 3 na 4 za buku lino, zidzakuthandizani mmene mungaonetsele cikondi canu kwa Yehova, pocita zimene zimamukondweletsa na kupewa zomukhumudwitsa.
2. N’cifukwa ciyani nthawi zina kungakhale kovuta kuonetsa cikondi cathu pa Yehova?
“Masoka a munthu wolungama ndi oculuka.” (Salimo 34:19) Tonsefe timalimbana na kupanda ungwilo kwathu. Timakhalanso na mavuto azacuma, kucitilidwa zosalungama, na mavuto ena ambili. Cifukwa ca zimenezi, kungakhale kovuta kucita zimene Yehova amafuna kwa ife. Koma kucita zimene Yehova amaletsa, ndiko kumakhala kosavuta. Mukakhulupilika kucita zimene Yehova amakuuzani, mumaonetsa kuti mumam’konda kuposa cinthu cina ciliconse. Umenewo ndiwo umboni wakuti ndinu wokhulupilikadi kwa iye. Mukatelo, iyenso adzakhalanso wokhulupilika kwa inu, ndipo sadzakusiyani konse.—Ŵelengani Salimo 4:3.
KUMBANI MOZAMILAPO
Onani cifukwa cake kukhala kwanu womvela ni nkhani yaikulu kwa Yehova. Ndipo dziŵani cimene cingakuthandizeni kukhalabe wokhulupilika kwa iye.
3. Nkhani imene inunso imakukhudzani
Buku la Yobu m’Baibo, lionetsa kuti Satana sananeneze Yobu yekha, ananenezanso anthu onse ofuna kutumikila Yehova. Ŵelengani Yobu 1:1, 6–2:10, na kukambilana mafunso aya:
-
Kodi Satana anakamba kuti Yobu amamvela Yehova cifukwa ciyani?—Onani Yobu 1:9-11.
-
Ndipo Satana anati ciyani ponena za anthu onse, kuphatikizapo inuyo?—Onani Yobu 2:4.
Ŵelengani Yobu 27:5b, na kukambilana funso ili:
-
Kodi Yobu anaonetsa bwanji kuti anali kukondadi Yehova?
4. Kondweletsani mtima wa Yehova
Ŵelengani Miyambo 27:11, na kukambilana mafunso aya:
-
Kodi Yehova amamva bwanji mukamacita zinthu mwanzelu komanso kumumvela? Ndipo cifukwa ciyani?
5. Mungathe kukhala wokhulupilika kwa Yehova
Cifukwa Yehova timamukonda, timauzako ena za iye. Ngakhale zinthu zikhale zovuta, cikhulupililo cathu cimatilimbikitsa kuuzabe ena za iye. Tambani VIDIYO, kenako kambilanani mafunso otsatila.
-
Kodi nthawi zina zimakuvutani kuuzako ena za Yehova?
-
Mu vidiyo imene mwaona, kodi n’ciyani cinathandiza Grayson kuthetsa mantha ake?
Kukhala okhulupilika kwa Yehova n’kosavuta ngati tikonda zimene iyenso amakondwela nazo, na kuzonda zimene iye amadana nazo. Ŵelengani Salimo 97:10, na kukambilana mafunso aya:
-
Malinga na zimene mwaphunzila, kodi ni zinthu ziti zimene Yehova amakondwela nazo? Nanga ni zinthu ziti zimene amadana nazo?
-
Kodi cingakuthandizeni n’ciyani kuti muzikonda zabwino komanso kudana na zoipa?
6. Tikamvela Yehova timapindula
Kumvela Yehova ni kwanzelu nthawi zonse. Ŵelengani Yesaya 48:17, 18, na kukambilana mafunso aya:
-
Kodi muganiza n’zoona kuti Yehova amatifunila zabwino nthawi zonse? Mwayankha conco cifukwa ciyani?
-
Pofika pano, kodi kuphunzila kwanu Baibo komanso za Mulungu woona Yehova, kwakupindulilani motani?
ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Zocita zanga sizimukhudza kwenikweni Mulungu.”
-
Kodi mungamuŵelengele lemba liti pomuonetsa kuti zocita zathu zimamukhudza Yehova?
CIDULE CAKE
Ngakhale mukumane na mavuto otani, mungaonetse kuti Yehova mumamukonda pomumvela na kukhalabe wokhulupilika kwa iye.
Mafunso Obweleza
-
Kodi mwaphunzilapo ciyani pa citsanzo ca Yobu?
-
Kodi muyenela kucita ciyani poonetsa kuti Yehova mumamukonda?
-
Kodi n’ciyani cidzakuthandizani kukhalabe wokhulupilika kwa Yehova?
FUFUZANI
Pezani mmene mungakhalile wokhulupilika kwa Yehova komanso ku mpingo.
Onaninso zina zimene Satana amakamba zoneneza anthu.
Onani mmene ana aang’ono nawonso angaonetsele cikondi cawo pa Yehova.
Kodi wacicepele amene akuvutitsidwa na anzake, angacite ciyani kuti akhalebe wokhulupilika kwa Mulungu?