Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 12

Mzimu Waubwenzi na Cifundo

Mzimu Waubwenzi na Cifundo

1 Atesalonika 2:7, 8

ZOFUNIKILA: Lankhulani na mzimu woyenelela, ndipo onetsani kuti mumawaganizila omvela anu.

MOCITILA:

  • Ganizilani za omvela anu. Konzekeletsani mtima wanu poganizila mavuto amene omvela anu angamakumane nawo. Yesani kuganizila za mmene amamvelela.

  • Sankhani mawu mosamala. Yesetsani kutsitsimula omvela anu, kuwatonthoza, na kuwalimbikitsa. Pewani mawu amene angawakhumudwitse. Komanso pewani kukamba mawu onyoza omvela anu amene si Mboni, kapena kusuliza zikhulupililo zawo, zimene eni ake amazilemekeza.

  • Aikileni mtima omvela anu. Pokamba na mawu acifundo komanso magesca oyenelela, onetsani omvela anu kuti mumasamaladi za iwo. Samalaninso na nkhope yanu, muzimwetulila kaŵili-kaŵili.