Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 15

Kukamba Motsimikiza

Kukamba Motsimikiza

1 Atesalonika 1:5

ZOFUNIKILA: Onetsani kuti mumakhulupilila kuti zimene mukamba n’zoona komanso n’zofunika ngako.

MOCITILA:

  • Muzikonzekela mokwanila. Iŵelengeni nkhaniyo mpaka mutamvetsetsa mfundo zazikulu, komanso mmene Malemba amatsimikizila kuti n’za zoona. Yesani kufotokoza mfundo zanu mwa mawu ocepa komanso osavuta kumva. Unikani bwino mmene mfundozo zingawapindulitsile omvela anu. Pemphelelani mzimu woyela.

  • Seŵenzetsani mawu okhutilitsa omvela. M’malo mokamba mawu ndendende mmene anawalembela m’cofalitsa, akambeni m’mawu anu-anu. Lankhulani m’njila yoonetsa kuti mudziŵa zimene mukamba.

  • Kambani mocokela pansi pa mtima. Kambani na mawu omveka bwino. Komanso muziwayang’ana omvela anu.