Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 16

Khalani Wolimbikitsa Komanso Wotsitsimula

Khalani Wolimbikitsa Komanso Wotsitsimula

Yobu 16:5

ZOFUNIKILA: Muzikamba zinthu zothandiza komanso zolimbikitsa.

MOCITILA:

  • Khalani na cidalilo mwa omvela anu. Dalilani kuti iwo ali na mtima wofuna kukondweletsa Yehova. Ngakhale pofuna kupeleka uphungu, coyamba pezani cowayamikila moona mtima.

  • Cepetsani kukamba pa zinthu zoipa. Chulani zoipa m’nkhani yanu mongofuna kumveketsa mfundo inayake. Koma mzimu wonse wa nkhani yanu uzikhala pa zinthu zabwino.

  • Seŵenzetsani kwambili Mawu a Mulungu. Unikani zimene Yehova anacita, zimene akucita, na zimene adzacitila anthu. Apatseni ciyembekezo omvela anu na kuwalimbikitsa.