Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 5

Kuŵelenga Bwino

Kuŵelenga Bwino

1 Timoteyo 4:13

ZOFUNIKILA: Ŵelengani mokweza mawu, komanso ndendende mmene awalembela.

MOCITILA:

  • Konzekelani bwino. Dziŵani cifukwa cimene analembela nkhaniyo. Yesezani kuŵelenga magulu a mawu, osati liwu limodzi-limodzi. Samalani kuti musaikilepo mawu, kulumphila, kapena kuchula mawu ena ofananako. Samalani zizindikilo zonse za m’kalembedwe.

  • Chulani liwu lililonse moyenelela. Ngati simudziŵa mochulila bwino liwu, iyang’aneni mu dikishonale, kapena imvetseleni pa lekoding’i ya cofalitsa, kapena funsilani kwa munthu amene amaŵelenga bwino.

  • Muzikamba momveka bwino. Muzichula mawu mowamveketsa bwino, mutaŵelamutsa mutu wanu na kutsegula bwino pakamwa panu. Yesetsani kumawachula bwino-bwino mawu.