Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 9

Kuseŵenzetsa Bwino Zitsanzo Zooneka

Kuseŵenzetsa Bwino Zitsanzo Zooneka

Genesis 15:5

ZOFUNIKILA: Kuti mumveketse bwino mfundo zofunika mungaseŵenzetse zitsanzo za zinthu zooneka.

MOCITILA:

  • Sankhani zinthu zooneka zothandizila kuphunzitsa. Mungaseŵenzetse mapikica, zithunzi, mapu, chati ya nthawi, na zinthu zina zooneka, kotelo kuti mumveketse mfundo zofunika, osati tumfundo tung’ono-tung’ono. Onetsetsani kuti omvela anu asakumbukile citsanzo cooneka cokhaco, koma maka-maka phunzilo lake.

  • Tsimikizani kuti omvela anu akutha kuciona bwino citsanzo coonekaco.