Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mawu Oyamba a Cigawo 10

Mawu Oyamba a Cigawo 10

Yehova ni Mfumu ya cilengedwe conse. Iye nthawi zonse wakhala akulamulila, ndipo adzalamulilabe kwamuyaya. Mwacitsanzo, anapulumutsa Yeremiya m’citsime cozama. Anapulumutsa Sadirake, Mesake na Abedinego m’ng’anjo ya moto, komanso Danieli m’dzenje la mikango. Yehova anateteza Esitere kuti apulumutse anthu onse a mtundu wake. Iye sadzalola kuti zoipa zipitilize kwamuyaya. Maulosi okhudza fano lalikulu komanso mtengo waukulu, amatitsimikizila kuti Ufumu wa Yehova posacedwa udzacotsapo zoipa zonse na kuyamba kulamulila pa dziko lapansi.

M'CIGAWO CINO

PHUNZILO 57

Yehova Atumiza Yeremiya Kuti Akalalikile

Zimene mneneli wacicepele uyu anakamba, zinawakwiitsa kwambili akulu-akulu a Yuda.

PHUNZILO 58

Yerusalemu Awonongedwa

Ayuda apitiliza kulambila milungu yabodza, ndiyeno Yehova awasiya.

PHUNZILO 59

Anyamata Anayi Amene Anamvela Yehova

Anyamata aciyuda sanaleke kukhulupilila Yehova, ngakhale ali ku nyumba kwa mfumu nebukadinezara ku Babulo.

PHUNZILO 60

Ufumu Umene Udzalamulila Kwamuyaya

Danieli amasulila tanthauzo la maloto odabwitsa a Nebukadinezara.

PHUNZILO 61

Anakana Kugwadila Fano

Sadirake, Mesake, na Abedinego akana kulambila fano lagolide la mfumu ya Babulo.

PHUNZIIO 62

Ufumu Umene Uli Monga Mtengo Waukulu

Maloto a Nebukadinezara alosela za tsogolo la iye mwini.

PHUNZILO 63

Dzanja Lilemba pa Cipupa

Kodi mawu osadziŵika anaonekela pa nthawi iti? Nanga atanthauza ciani?

PHUNZILO 64

Danieli Aponyedwa m’Dzenje la Mikango

Pemphelani kwa Yehova tsiku lililonse, monga mmene Danieli anali kucitila!

PHUNZILO 65

Mfumukazi Esitere Apulumutsa Anthu a Mtundu Wake

Ngakhale kuti anali ku dziko la eni, zinthu zinasintha kucoka pa mwana wamasiye n’kukhala mfumukazi.

PHUNZILO 66

Ezara Aphunzitsa Cilamulo ca Mulungu

Aisiraeli atamvetsela kwa Ezara, iwo anapanga lonjezo lapadela kwa Mulungu.

PHUNZILO 67

Mpanda wa Yerusalemu Umangidwanso

Nehemiya anadziŵa kuti adani ake afuna kuukila. Koma n’cifukwa ciani sanacite mantha?