Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 64

Danieli Aponyedwa m’Dzenje la Mikango

Danieli Aponyedwa m’Dzenje la Mikango

Mfumu ina ya Babulo inali Dariyo amene anali Mmedi. Dariyo anaona kuti Danieli anali munthu wofunika kwambili. Anam’sankha kukhala woyang’anila amuna olemekezeka a mu mzindawo. Koma amuna amenewo anam’citila nsanje Danieli, ndipo anafuna kumupha. Iwo anali kudziŵa kuti Danieli anali kupemphela kwa Yehova katatu tsiku lililonse. Conco iwo anauza Dariyo kuti: ‘Mbuyathu mfumu, khazikitsani lamulo lakuti aliyense azipemphela kwa imwe cabe. Ndipo aliyense amene sadzamvela lamulo limenelo, akaponyedwe m’dzenje la mikango.’ Nkhaniyo anakondwela nayo Dariyo, cakuti anasaina lamulo limenelo.

Danieli atamva za lamulo latsopano limenelo, anapita ku nyumba kwake. Anagwada pansi pa windo yotsegula, na kuyamba kupemphela kwa Yehova. Amuna ansanje aja analowa m’nyumba mwake, ndipo anapeza kuti akupemphela. Iwo anathamanga kukauza Dariyo kuti: ‘Danieli samvela lamulo lanu. Akupemphelabe kwa Mulungu wake katatu pa tsiku.’ Dariyo anali kum’konda kwambili Danieli, ndipo sanafune kuti aphedwe. Tsiku lonse anavutika maganizo kuyesa-yesa kuti apeze njila yopulumutsila Danieli. Koma ngakhale kwa mfumu zinali zosatheka kucinja lamulo imene anasainila kale. Conco, anakakamizika kulamula anthu ake kuti akaponye Danieli m’dzenje la mikango.

Usiku umenewo, tulo sanatuone Dariyo, cifukwa codela nkhawa Danieli. Kutaca m’maŵa, iye anathamangila ku dzenje kuja, na kufuulila Danieli kuti: ‘Kodi Mulungu wako wakupulumutsa?’

Danieli anayankha kuti: ‘Mngelo wa Yehova watseka pakamwa pa mikango. Siinanilume ngakhale pang’ono.’ Dariyo anakondwela ngako! Analamula kuti Danieli atulutsidwe m’dzenjemo. Mikangoyo siinam’khudze ngakhale pang’ono. Ndiyeno mfumu inalamula kuti: ‘Aponyeni m’dzenjemo aja amene ananeneza Danieli.’ Pamene anawaponyamo, mikango inawakhadzula-khadzula n’kuwadyelatu.

Ndiyeno Dariyo anapeleka lamulo ili kwa anthu ake: ‘Aliyense aziyopa Mulungu wa Danieli. Anapulumutsa Danieli ku mikango.’

Kodi umapemphela kwa Yehova tsiku lililonse monga Danieli?

“Yehova amadziŵa kupulumutsa anthu odzipeleka kwa iye akakhala pa mayeselo.” —2 Petulo 2:9