Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 60

Ufumu Umene Udzalamulila Kwamuyaya

Ufumu Umene Udzalamulila Kwamuyaya

Tsiku lina usiku, Mfumu Nebukadinezara inalota maloto odabwitsa. Malotowo anam’detsa nkhawa kwambili cakuti anasoŵa tulo. Iye anaitanitsa amatsenga ake na kuwauza kuti: ‘Nimasulileni zimene nalota.’ Amatsengawo anati: ‘Mfumu yathu, tiuzeni zimene mwalota.’ Koma Nebukadinezara anaŵauza kuti: ‘Iyai! Imwe muniuze zimene nalota, mukakangiwa nikuphani.’ Koma iwo anakambanso kuti: ‘Koma tiuzeni zimene mwalota, ndipo tidzakumasulilani.’ Mfumuyo inati: ‘Nonsenu mufuna kuniputsitsa. Nati niuzeni zimene nalota!’ Tsopano anauza mfumuyo kuti: ‘Palibe munthu angakwanitse kucita zimenezo. Zimene mufuna n’zosatheka.’

Nebukadinezara anakalipa kwambili, cakuti analamula kuti onse amatsenga na amuna anzelu aphedwe. Izi zinali kuphatikizapo Danieli, Sadirake, Mesake na Abedinego. Koma Danieli anapempha mfumu kuti iyembekezeko pang’ono. Pamenepo iye na anzake anapemphela kwa Yehova kuti aŵathandize. Kodi Yehova anacita ciani?

M’masomphenya, Yehova anaonetsa Danieli zimene mfumu Nebukadinezara analota, na kumuuza tanthauzo lake. Tsiku lotsatila, Danieli anapita kwa mtumiki wa mfumu na kumuuza kuti: ‘Musaphe aliyense wa amuna anzelu. Ine nikhoza kumasulila maloto a mfumu.’ Mtumikiyo anapeleka Danieli kwa Nebukadinezara. Ndipo Danieli anauza mfumu kuti: ‘Mulungu wakuululilani zakutsogolo. Zimene munalota ni izi: Munaona cifano cacikulu ca mutu wagolide, cifuŵa na manja asiliva, mimba na nchafu zamkuwa, miyendo yacitsulo, ndipo mapazi ake osakaniza citsulo na dongo kapena kuti dothi. Kenako, mwala unasemedwa m’phili ndipo unabwela n’kumenya kumapazi kwa cifano cija. Cifanoco cinapwanyika n’kupeleka kukhala fumbi lokha-lokha. Kenako fumbilo linauluzika na mphepo. Mwalawo unakula n’kukhala phili lalikulu, cakuti linadzaza dziko lonse lapansi.’

Ndiyeno Danieli anati: ‘Tanthauzo la maloto anu ni ili: Mutu wagolide uimila ufumu wanu. Cifuŵa ca siliva ni ufumu umene udzabwela pambuyo panu. Ndiyeno padzabwela wina woimilidwa na mkuwa, ndipo udzalamulila pa dziko lonse. Koma ufumu umene udzakonkhapo udzakhala wolimba monga citsulo kapena kuti nsimbi. Ufumu wothela udzakhala wogaŵikana, mbali zina zolimba monga citsulo, mbali zina zosalimba monga dongo. Mwala umene unakhala phili, ni Ufumu wa Mulungu. Ufumuwo udzaphwanya maufumu onsewa ndipo udzakhalapo kwamuyaya.’

Pamenepo Mfumu Nebukadinezara inagwada pamaso pa Danieli na kuŵelama mpaka nkhope yake pansi. Ndiyeno inati: ‘Mulungu wako wakuululila maloto amenewa. Palibe Mulungu wina wolingana naye.’ M’malo mwa kumupha Danieli, Nebukadinezara anamuika kukhala woyang’anila amuna onse anzelu, na kumusankha kukhala wolamulila cigawo ca Babulo. Kodi waona mmene Yehova anayankhila pemphelo la Danieli?

“Anawasonkhanitsa pamodzi, kumalo amene m’Ciheberi amachedwa Haramagedo.”—Chivumbulutso 16:16