Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mawu Oyamba a Cigawo 11

Mawu Oyamba a Cigawo 11

Cigawo cino cifotokoza nkhani za m’Malemba Acigiriki Acikhristu. Yesu anabadwila m’banja yosaukila, imene inali kukhala m’tauni yaing’ono. Anali kuthandiza atate ake pa nchito yawo ya ukalipentala. Yesu ndiye anali kudzapulumutsa mtundu wa anthu. Yehova anam’sankha kukhala Mfumu ya Ufumu wakumwamba. Ngati ndimwe kholo, thandizani mwana wanu kumvetsa kuti Yehova anasankha mosamala banja limene Yesu adzabadwilamo, komanso kumene adzakulila. Fotokozani mmene Yehova anatetezela Yesu kuti asaphedwe na Herode, komanso kuti palibe cingalepheletse colinga ca Yehova. Kambilanani za mmene Yehova anapatsila Yohane nchito yokonzela njila Yesu. Unikani mmene Yesu anaonetsela kuti kuyambila ali mwana, anali kukonda nzelu zocokela kwa Yehova.

M'CIGAWO CINO

PHUNZILO 68

Elizabeti Akhala na Mwana

N’cifukwa ciani mwamuna wa Elizabeti anauzidwa kuti adzaleka kukamba mpaka mwana akabadwe?

PHUNZILO 69

Gabirieli Aonekela kwa Mariya

Amuuza uthenga umene udzasintha moyo wake wonse

PHUNZILO 70

Angelo Analengeza za Kubadwa kwa Yesu

Abusa amene anamvela cilengezo ca kubadwa kwa Yesu anacitapo kanthu mwamsanga.

PHUNZILO 71

Yehova Anam’teteza Yesu

Mfumu yoipa inafuna kupha Yesu.

PHUNZILO 72

Pamene Yesu Anali Wacicepele

Kodi n’ciani cinadabwitsa aphunzitsi pakacisi ponena za Yesu?

PHUNZILO 73

Yohane Anakonza Njila

Pamene Yohane wakula akhala mneneli. Iye aphunzitsa anthu kuti Mesiya adzabwela. Kodi anthu aulandila bwanji uthenga wake?