Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 72

Pamene Yesu Anali Wacicepele

Pamene Yesu Anali Wacicepele

Yosefe na Mariya anali kukhala ku Nazareti pamodzi na Yesu, komanso ana ena aamuna ndi aakazi. Kuti asamalile banja lake, Yosefe anali kuseŵenza nchito yaukalipentala. Ndipo anali kuphunzitsa banja lake za Yehova na Cilamulo cake. Nthawi zonse, banja limeneli linali kupita ku sunagoge kukalambila. Komanso, caka ciliconse anali kupita ku Yerusalemu ku cikondwelelo ca Pasika.

Pamene Yesu anafika zaka 12, monga mwa nthawi zonse banja lawo linapanga ulendo wautali wopita ku Yerusalemu. Atafika, mu mzinda munali anthu ambili obwela ku cikondwelelo ca Pasika. Pambuyo pa cikondwelelo, Yosefe na Mariya anauyamba ulendo wobwelela kwawo. Iwo anaganiza kuti Yesu ali pakati pawo. Koma pamene anam’funa-funa sanam’peze.

Iwo anabwelela ku Yerusalemu, ndipo anasakila mwana wawo kwa masiku atatu. Potsilizila pake anapita ku kacisi. Anam’peza kumeneko. Anali pakati pa aphunzitsi, akuwamvetsela mwachelu na kuŵafunsa mafunso anzelu. Aphunzitsiwo anacita cidwi kwambili na Yesu cakuti nawonso anayamba kum’funsa mafunso. Ndipo anadabwa na mayankho ake. Anaona kuti Yesu anali kucidziŵa bwino Cilamulo ca Yehova.

Yosefe na Mariya anada nkhawa kwambili. Ndiyeno Mariya anati: ‘Iwe mwana iwe, tinali kukufuna-funa! Unali kuti?’ Yesu anayankha kuti: ‘Kodi simudziŵa kuti nifunika kupezeka m’nyumba ya Atate wanga?’

Kenako Yesu anapita na makolo ake ku Nazareti. Yosefe anaphunzitsa Yesu nchito yaukalipentala. Kodi uganiza kuti Yesu anali munthu wotani pamene anali wacicepele? Pamene Yesu anali kukula, nzelu zake zinali kuwonjezeleka, ndipo anali kukondewa kwambili na Mulungu komanso anthu.

“Ndimakondwela ndi kucita cifunilo canu, inu Mulungu wanga, ndipo cilamulo canu cili mumtima mwanga.”—Salimo 40:8