Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 74

Pamene Yesu Anakhala Mesiya

Pamene Yesu Anakhala Mesiya

Yohane anali kulalikila kuti: ‘Wina wamkulu kuposa ine akubwela.’ Pamene Yesu anali na zaka pafupi-fupi 30, ananyamuka kucoka ku Galileya kupita ku Mtsinje wa Yorodano. Kumeneko anapeza Yohane akubatiza anthu. Nayenso Yesu anapempha Yohane kuti am’batize. Koma Yohane anakana. Anati: ‘Ine siniyenela kubatiza imwe. Imwe muyenela kubatiza ine.’ Yesu anauza Yohane kuti: ‘Yehova afuna kuti iwe unibatize.’ Conco onse aŵili analoŵa pa Mtsinje wa Yorodano, ndipo Yohane anamiza Yesu thupi lonse m’madzi.

Yesu atavuuka m’madzi, anapemphela. Pamenepo kumwamba kunatseguka, ndipo mzimu wa Mulungu wooneka monga nkhunda unatsikila pa iye. Ndiyeno panamveka mawu a Yehova kucokela kumwamba akuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwela naye.”

Pamene mzimu wa Yehova unabwela pa Yesu, m’pamene iye anakhala Khristu kapena kuti Mesiya. Tsopano anafunikila kuyamba nchito imene Yehova anamutumizila pa dziko lapansi.

Atangobatizika, Yesu anapita ku cipululu, ndipo anakhalako masiku 40. Atabwelako, anapita kwa Yohane. Yohane ataona Yesu akubwela ca apo, anati: ‘Uyu ndiye Mwanawankhosa wa Mulungu amene adzacotsa ucimo wa dziko.’ Mwa kukamba izi, Yohane anathandiza anthu kudziŵa kuti Yesu ndiye Mesiya. Kodi udziŵa zinam’citikila Yesu ku cipululu? Tidzaona.

“Panamveka mawu ocokela kumwamba akuti: ‘Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa, ndimakondwela nawe.’”—Maliko 1:11