Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 101

Paulo Atumizidwa ku Roma

Paulo Atumizidwa ku Roma

Ulendo wa Paulo wacitatu wokalalikila unathela ku Yerusalemu. Kumeneko anam’manga na kum’ponya m’ndende. M’masomphenya usiku, Yesu anauza Paulo kuti: ‘Udzapita ku Roma kuti ukalalikile kumeneko.’ Paulo anatengedwa kucoka ku Yerusalemu kupita ku Kaisareya, kumene anakhala m’ndende zaka ziŵili. Poweluzidwa mlandu pamaso pa Bwanamkubwa Festo, Paulo anati: ‘Nipempha kuti nikaweluzidwe na Kaisara ku Roma.’ Festo anati: “Popeza kuti wapempha kukaonekela kwa Kaisara, udzapitadi kwa Kaisara.” Basi anam’tenga na kum’kwezeka m’boti yoyenda ku Roma. Abale aŵili, Luka na Aristako, anapita naye.

Ali pa nyanja, panauka cimphepo camphamvu, ndipo cinawomba kwa masiku ambili. Onse m’botimo anaganiza kuti basi akufa. Koma Paulo anawauza kuti: ‘Amuna inu, mngelo waniuza m’maloto kuti: ‘Usayope Paulo. Udzafika ku Roma, ndipo onse amene uli nawo m’boti adzafika.’ Limbani mtima! Sitidzafa iyai.’

Cimphepo cija cinawomba kwa masiku 14. Kenako mtunda unaonekela. Cinali cisumbu ca Melita. Akuyandikila kumtunda, botiyo inagunda pansi na kupasuka-pasuka. Koma anthu onse 276 amene anali m’botiyo anafika kum’tunda bwino-bwino. Ena ananyaya, ena anagwila zidutswa za boti na kuyandama mpaka kumtunda. Anthu a ku Melita anaŵasamalila bwino, na kuwayatsila moto kuti awothe.

Patapita miyezi itatu, asilikali anakwezeka Paulo boti ina kupita naye ku Roma. Atafika ku Roma, abale anabwela kudzamuona. Paulo ataona abalewo, anayamikila Yehova ndipo analimba mtima. Ngakhale kuti Paulo anali mkaidi, analoledwa kukakhala m’nyumba ya lendi na msilikali wom’londa. Anakhala kumeneko kwa zaka ziŵili. Anthu anali kubwela kudzamuona, ndipo iye anali kuwalalikila za Ufumu wa Mulungu na kuwaphunzitsa za Yesu. Analembanso makalata opita ku mipingo ya ku Asia Minor, komanso ku Yudeya.

“Tikusonyeza mwa njila ina iliyonse kuti ndife atumiki a Mulungu. Tikucita zimenezi mwa kupilila zambili, kudutsa m’masautso, kukhala osowa, kukumana ndi zovuta.”—2 Akorinto 6:4