Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 100

Paulo na Timoteyo

Paulo na Timoteyo

Timoteyo anali m’bale wacicepele mu mpingo wa ku Lusitara. Atate ake anali Mgiriki ndipo amayi ake anali Myuda. Amayi ake a Yunike, na ambuye ake a Loisi, anam’phunzitsa za Yehova kuyambila ali wamng’ono.

Pamene Paulo anacezela mpingo wa ku Lusitara pa ulendo wake waciŵili, anaona kuti Timoteyo anali kukonda kwambili abale, ndipo anali kuwathandiza. Paulo anapempha Timoteyo kuti ayende naye pa ulendo umenewo. M’kupita kwa nthawi, Paulo anaphunzitsa Timoteyo kukhala mlaliki komanso mphunzitsi wabwino wa uthenga wabwino.

Mzimu woyela unatsogolela Paulo na Timoteyo kulikonse kumene anali kuyenda. Tsiku lina usiku, Paulo anaona masomphenya. M’masomphenyawo, munthu wina anauza Paulo kupita ku Makedoniya kuti akaŵathandize. Conco Paulo, Timoteyo, Sila, komanso Luka, anapita kukalalikila na kukhazikitsa mipingo.

Mu mzinda wa Tesalonika ku Makedoniya, amuna ndi akazi ambili anakhala Akhristu. Koma Ayuda ena anali kucitila nsanje Paulo na anzakewo. Iwo anatuntha cigulu ca anthu kuti aukile abalewo, ndipo anawagwila na kuŵapeleka kwa olamulila a mzinda. Anthuwo anali kufuula kuti: ‘Anthu awa ni adani a boma la Roma!’ Moyo wa Paulo na Timoteyo unali pa ciwopsezo. Cakuti anacita kuthaŵila ku Bereya usiku.

Anthu a ku Bereya anali ofunitsitsa kumvela uthenga wabwino. Ndipo Agiriki komanso Ayuda a kumeneko anakhala okhulupilila. Koma pamene Ayuda ena anabwela kucokela ku Tesalonika, iwo anayambitsa zaciwawa. Izi zinapangitsa Paulo kuthaŵila ku Atene. Paulo na Sila anakhalabe ku Bereya kuti alimbikitse abale. M’kupita kwa masiku, Paulo anatumizanso Timoteyo ku Tesalonika kuti akathandize abale kupilila cizunzo kumeneko. Pambuyo pake, Paulo anatumiza Timoteyo kuti akacezele mipingo ina yambili na kuilimbikitsa.

Paulo anauza Timoteyo kuti: ‘Amene afuna kutumikila Yehova adzazunzidwa.’ Timoteyo anazunzidwa na kuponyedwa m’ndende cifukwa ca cikhulupililo cake. Anauona kukhala mwayi wake woonetsa kuti ni wokhulupilika kwa Yehova.

Paulo anauza Afilipi kuti: ‘Natumiza Timoteyo kwa inu. Adzakuphunzitsani tanthauzo la kuyenda m’coonadi. Ndiponso adzakuphunzitsani zimene muyenela kucita polalikila.’ Paulo anali kum’dalila Timoteyo. Kwa zaka zambili, iwo anali kuseŵenzela pamodzi monga mabwenzi komanso atumiki a Mulungu.

“Ndilibe wina wamtima ngati iye, amene angasamaledi za inu moona mtima. Pakuti ena onse akungofuna za iwo eni, osati za Khristu Yesu.”—Afilipi 2:20, 21