Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 96

Yesu Asankha Saulo

Yesu Asankha Saulo

Saulo anali nzika ya dziko ya Roma, ndipo anabadwila ku Tariso. Anali Mfarisi wodziŵa Cilamulo ca Mose, koma anali kuzonda Akhristu. Anali kupita ku nyumba za Akhristu, kuwadonsela panja na kukawaponya mu jele. Tsiku lina anali kungotamba pamene Sitefano, wophunzila wa Yesu, anali kuphedwa na cigulu ca anthu mwa kum’ponya miyala.

Koma Saulo sanakhutile na kugwila Akhristu a ku Yerusalemu cabe. Conco anakapempha kwa mkulu wa ansembe kuti amutumize ku mzinda wa Damasiko. Colinga cake cinali kukagwila Akhristu a kumeneko. Koma pamene Saulo anayandikila mzindawo, mwadzidzidzi anangoona kuwala kocita kutowa m’maso, ndipo anagwa pansi. Pamenepo anamva mawu akuti: ‘Saulo, n’cifukwa ciani ukunizunza?’ Saulo anafunsa kuti: ‘Kodi ndimwe ndani?’ Mawuwo poyankha anati: ‘Ndine Yesu. Pita ku Damasiko, ndipo udzauzidwa zimene ufunika kucita.’ Pamenepo Saulo analeka kuona. Anacita kum’gwila dzanja kuti akaloŵe mu mzinda.

Ku Damasiko kunali Mkhristu wina wokhulupilika dzina lake Hananiya. M’masomphenya, Yesu anamuuza kuti: ‘Nyamuka, upite ku nyumba kwa Yudasi ku msewu wochedwa Msewu Wowongoka, ndipo ukafunse za munthu wa dzina lakuti Saulo.’ Hananiya anati: ‘Ambuye, mbili ya munthu uja niidziŵa bwino! Iye amaponya ophunzila anu m’ndende!’ Koma Yesu anati: ‘Upite kwa iye, pakuti nasankha Saulo kuti akalalikile uthenga wabwino kwa anthu a mitundu yambili.’

Hananiya atapita kwa Saulo anati kwa iye: ‘M’bale wanga Saulo, Yesu wanituma kwa iwe kuti nikutsegule maso.’ Pamenepo Saulo anayambanso kuona. Anaphunzitsidwa za Yesu, kenako anakhala wotsatila wake. Monga Mkhristu wobatizika tsopano, Saulo anayamba kulalikila m’masunagoge pamodzi na Akhristu anzake. Ganizila cabe mmene Ayuda anadabwila kuona Saulo akuphunzitsa anthu za Yesu. Amvekele: ‘Kodi munthu uyu si uja amene anali kugwila ophunzila a Yesu?’

Saulo analalikila mu Damasiko kwa zaka zitatu. Koma Ayuda anamuzonda kwambili, moti anakonza ciwembu cakuti amuphe. Koma abale anamva za ciwembu cawo, ndipo anathandiza Saulo kuthaŵa. Anamuika m’dengu na kumutulutsila pawindo pa mpanda wa mzinda.

Iye anapita ku Yerusalemu. Kumeneko, anayesa kugwilizana na gulu la abale. Koma abalewo anali kumuyopa. Ndiyeno wophunzila wina wokoma mtima Baranaba, anatenga Saulo n’kupita naye kwa atumwi, na kuŵatsimikizila kuti Saulo anatembunukadi. Kenako Saulo anayamba kulalikila uthenga wabwino mwakhama pamodzi na mpingo mu Yerusalemu. M’kupita kwa nthawi, anadziŵika monga Paulo.

“Khristu Yesu anabwela m’dziko kudzapulumutsa ocimwa.  . . Mwa ocimwa amenewa, ine ndiye wocimwa kwambili.”—1 Timoteyo 1:15