Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mawu Oyamba a Cigawo 2

Mawu Oyamba a Cigawo 2

N’cifukwa ciani Yehova anabweletsa cigumula cimene cinawononga anthu m’nthawi yakale? Kuciyambi kwa mbili ya anthu, Satana anapandukila Yehova. Anthu ena monga Adamu, Hava, na mwana wawo Kaini, anasankha kukhala ku mbali yoipa ya Satana. Koma anthu ena ocepa, monga Abele na Nowa, anasankha kukhala ku mbali yabwino ya Yehova. Anthu ambili anakhala oipa kwambili, cakuti Yehova anaŵawononga onse. Cigawo cino, cidzatithandiza kudziŵa kuti Yehova amaona mbali imene tasankha. Ndipo sadzalola anthu oipa kugonjetsa anthu abwino.

M'CIGAWO CINO

PHUNZILO 3

Adamu na Hava Sanamvele Mulungu

N’ciani cinali capadela ndi mtengo umodzi wa m’munda wa Edeni? N’cifukwa ciani Hava anadya cipatso ca mu mtengowo?

PHUNZILO 4

Kukwiya Mpaka Kupha Munthu

Mulungu analandila nsembe ya Abele osati ya Kaini. Kaini atadziŵa, akwiya kwambili na kucita cinthu coipa maningi.

PHUNZILO 5

Cingalawa ca Nowa

Angelo oipa atakwatila akazi pa dziko, anakhala na viŵana vimphona vankhanza ngako. Ciwawa cinali paliponse. Koma Nowa sanali ngati anthu amenewo—iye anali kukonda Mulungu na kumumvela.

PHUNZILO 6

Anthu 8 Anapulumuka na Kulowa m’Dziko Latsopano

Cimvula cinagwa kwa masiku 40 usana na usiku. Nowa na banja lake anakhala m’cingalawa kuposa caka cimodzi. Potsilizila, anatuluka m’cingalawa.