Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 17

Mose Anasankha Kulambila Yehova

Mose Anasankha Kulambila Yehova

Ku Iguputo, banja la Yakobo linadziŵika na dzina lakuti Aisiraeli. Pambuyo pakuti Yakobo na Yosefe amwalila, Farao watsopano anayamba kulamulila. Iye anawopa kuti Aisiraeli adzaculuka na kukhala amphamvu kuposa Aiguputo. Conco, Farao ameneyu anapanga Aisiraeli kukhala akapolo awo. Anawakakamiza kuumba nchelwa na kuwagwilitsa nchito yakalavula gaga m’minda yawo. Koma pamene anali kuwakhaulitsa nazo nchito, m’pamenenso Aisiraeli anali kuculukila-culukila. Lomba Farao pothedwa nzelu, analamula kuti mwana wamwamuna aliyense waciisiraeli aziphedwa akabadwa. Aisiraeli atamve zimenezi, anacita mantha kwambili!

Mzimayi wina waciisiraeli, dzina lake Yokebedi, anabala mwana wamwamuna wokongola kwambili. Kuti amuteteza, anamuika mu basiketi n’kukam’bisa m’mabango, kapena kuti m’matete, ku Mtsinje wa Nailo. Mlongo wake wa mwanayo, dzina lake Miriamu, anakhala pafupi kuti azimuyang’anila.

Mwana wamkazi wa Farao anabwela kudzasamba ku mtsinje, ndipo anaona basiketi imeneyo. Ataitsegula, anapezamo kamwana kakulila. Anakamvelela cifundo. Miriamu anafunsa kuti: ‘Kodi nikakupezeleni mzimayi amene angakuleleleni mwanayu?’ Mwana wa Farao atavomeleza, Miriamu anapita kukatenga mayi wake wa mwanayo, Yokebedi. Pamenepo mwana wa Farao anamuuza kuti: ‘Tenga mwanayu ukanilelele, n’dzayamba kukulipila.’

Mwanayo atakulako, Yokebedi anam’peleka kwa mwana wa Farao. Ndipo iye anam’patsa dzina lakuti Mose. Anamulela monga mwana wake-wake. Mose anakula monga mwana wa Mfumu, ndipo anali kupeza zonse zimene anali kufuna. Koma Mose sanaiŵale Yehova. Anali kudziŵa kuti kweni-kweni iye anali Mwiisiraeli, osati Mwiiguputo. Conco anasankha kutumikila Yehova.

Pa msinkhu wa zaka 40, Mose anafuna kuthandiza anthu a mtundu wake. Pamene anaona Mwiiguputo akumenya kapolo waciisiraeli, Mose anam’menya mwamphamvu na kumupha. Atacita izi, Mose anafocela thupi la mwiguputoyo mu mcenga. Pamene Farao anadziŵa, anafuna kumupha Mose. Koma Mose anathaŵila ku dziko la Midiyani. Ndipo Yehova anam’samala kumeneko.

“Mwa cikhulupililo, Mose . . . anakana kuchedwa mwana wa mwana wamkazi wa Farao, ndipo anasankha kuzunzidwa pamodzi ndi anthu a Mulungu.”—Aheberi 11:24,, 25