Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 36

Lonjezo la Yefita

Lonjezo la Yefita

Aisiraeli anamusiyanso Yehova na kuyamba kulambila milungu yonama. Pamene Aamoni anali kumenyana na Aisiraeli, milungu imeneyo siinaŵathandize. Aisiraeli anavutitsidwa kwa zaka zambili. Potsilizila pake anauza Yehova kuti: ‘Takucimwilani. Conde tipulumutseni kwa adani athu.’ Ndiyeno anawononga mafano awo na kuyambanso kulambila Yehova. Yehova sanafune kuti Aisiraeli apitilize kuvutika.

Msilikali wina dzina lake Yefita, anasankhidwa kuti atsogolele anthu pa nkhondo yomenyana ndi Aamoni. Yefita anauza Yehova kuti: ‘Mukatithandiza kupambana nkhondoyi, nilonjeza kuti nidzapeleka kwa inu munthu woyamba kutuluka m’nyumba yanga, kudzanilandila nikadzabwelako ku nkhondo.’ Yehova anamvela pemphelo ya Yefita, ndipo anamuthandiza kupambana nkhondoyo.

Pamene Yefita anabwelako ku nkhondo, mwana wake wamkazi ndiye anali woyamba kutuluka kukam’landila. Anali na mwana mmodzi yekhayo. Mwanayo anali kuvina na kuliza masece. Kodi Yefita anacita ciani? Anakumbukila lonjezo lake, amvekele: ‘Kalanga ine mwana wanga! Wacititsa mtima wanga kukhala wacisoni. N’napanga lonjeza kwa Yehova. Kuti nikwanilitse lonjezo limeneli, niyenela kukupeleka ku Silo kuti uzikatumikila pa cihema’. Koma mtsikanayo anati: ‘Atate ngati munapanga lonjezo kwa Yehova, muyenela kulikwanilitsa. Cimene nipempha cabe n’cakuti, munilole nikakhale ku mapili kwa miyezi iŵili na atsikana anzanga. Kenako nidzapita.’ Mwana wa Yefita anatumikila mokhulupilika pa cihema kwa moyo wake wonse. Caka ciliconse, anzake anali kupita ku Silo kukamuona.

“Amene amakonda kwambili mwana wake wamwamuna kapena wamkazi kuposa ine sali woyenela ine.”—Mateyu 10:37