Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 29

Yehova Asankha Yoswa

Yehova Asankha Yoswa

Mose anatsogolela Aisiraeli kwa zaka zambili. Koma apa lomba, anali pafupi kumwalila. Conco Yehova anamuuza kuti: ‘Sindiwe udzaloŵetsa Aisiraeli m’Dziko Lolonjezedwa. Koma nidzakuonetsa dzikolo.’ Ndiyeno Mose anapempha Yehova kuti asankhe munthu wina kuti atsogolele anthu ake. Yehova anamuyankha kuti: ‘Pita kwa Yoswa, ndipo ukamuuze kuti ndam’sankha kukhala mtsogoleli.’

MMose anauza Aisiraeli kuti iye adzamwalila posacedwa, na kuti Yehova wasankha Yoswa kuti awatsogolele ku Dziko Lolonjezedwa. Ndiyeno Mose anauza Yoswa kuti: ‘Usacite mantha. Yehova adzakuthandiza.’ Pasanapite nthawi yaitali, Mose anakwela pamwamba m’Phili la Nebo, ndipo Yehova anamuonetsa dziko limene analonjeza Abulahamu, Isaki, na Yakobo. Kenako Mose anamwalila, ali na zaka 120.

Ndiyeno Yehova anauza Yoswa kuti: ‘Woloka Mtsinje wa Yorodano, uloŵe m’dziko la Kanani. N’dzakuthandiza monga mmene n’nathandizila Mose. Ndipo uonetsetse kuti ukuŵelenga Cilamulo canga tsiku lililonse. Usacite mantha, limba mtima. Pita ukacite zimene ndakuuza.’

Yoswa anatuma azondi aŵili ku mzinda wa Yeriko. M’nkhani yokonkhapo, tidzaphunzila zimene zinacitika mu mzinda umenewu. Atabwelako azondiwo, anati inali nthawi yabwino yokaloŵa m’dziko la Kanani cifukwa anthu anali na mantha. M’maŵa mwake, Yoswa anauza Aisiraeli kuti apasule msasa. Ndiyeno, anauza ansembe onyamula likasa la cipangano kukhala patsogolo pokawoloka Mtsinje wa Yorodano. Mtsinjewo unali wosefukila. Koma pamene ansembe anaponda m’madzi, mtsinjewo unaleka kuyenda, ndipo madzi anapita. Ansembe anapita kukaima pakati pa mtsinje, ndipo mtundu wonse wa Isiraeli unawolokela ku tsidya linalo. Uganiza bwanji, kodi cozizwitsa ici sicinawakumbutse zimene Yehova anacita pa Nyanja Yofiila?

Lomba, pambuyo pa zaka zambili, Aisiraeli analoŵa m’Dziko Lolonjezedwa. Anayamba kumanga manyumba na mizinda. Anayamba kulima mphesa, zipatso, na mbewu zina. Linalidi dziko loyenda mkaka na uci.

“Yehova azidzakutsogolelani nthawi zonse ndipo adzakukhutilitsani ngakhale m’dziko louma.”—Yesaya 58:11