Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 31

Yoswa na Agibeoni

Yoswa na Agibeoni

Mbili ya kuwonongedwa kwa Yeriko inamveka ku mitundu ina ya m’dziko la Kanani. Mafumu awo anagwilizana kuti akamenyane na Aisiraeli. Koma Agibeoni anapanga pulani. Atavala vovala vong’ambika-ng’ambika anapita kwa Yoswa. Iwo anati kwa iye: ‘Tacokela kudziko lakutali ngako. Tinamva za Yehova, na zonse zimene anakucitilani ku Iguputo na ku Mowabu. Lonjezani kuti simudzatipha, ndipo ife tidzakhala atumiki anu.’

Yoswa anawakhulupilila na kuwalonjeza kuti sadzawapha. Koma patapita masiku atatu, Yoswa anadziŵa zakuti iwo sanacokele kudziko lakutali. Anali kukhala m’dziko la Kanani mmenemo. Conco, Yoswa anafunsa Agibeoni kuti: ‘N’cifukwa ciani munatinamiza?’ Iwo anayankha kuti: ‘Cifukwa tinacita mantha! Tidziŵa kuti Yehova Mulungu wanu ndiye akukumenyelani nkhondo. Conde musatiphe.’ Yoswa anasunga lonjezo lake, cakuti sanawaphe.

Pasanapite nthawi, mafumu asanu acikanani, na magulu awo a asilikali, anagwilizana zokathila nkhondo Agibeoni. Yoswa atamva zimenezi, anatenga asilikali ake na kuyenda usiku wonse kuti akapulumutse Agibeoni. Nkhondo inayamba m’mawa mwake kuseni-seni. Akanani anayamba kubalalika, aliyense kuloŵela kwake. Koma kulikonse kumene anathaŵila, Yehova anali kuwagwetsela vimiyala va matalala. Kenako Yoswa anapempha Yehova kuti aimitse dzuŵa. N’cifukwa ciani Yoswa anapempha Yehova kuimitsa dzuŵa, zimene sizinacitikepo cikhalile? Cifukwa anali kukhulupilila Yehova. Ndipo dzuŵa silinaloŵedi tsiku lonselo, mpaka Aisiraeli anagonjetsa mafumu acikananiwo, na magulu awo a nkhondo.

“Tangotsimikizani kuti mukati ‘Inde’ akhaledi inde, ndipo mukati ‘Ayi’ akhaledi ayi, pakuti mawu owonjezela pamenepa acokela kwa woipayo.”—Mateyu 5:37