Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 39

Mfumu Yoyamba ya Aisiraeli

Mfumu Yoyamba ya Aisiraeli

Yehova anapatsa Aisiraeli oweluza kuti aziŵatsogolela, koma iwo anafuna mfumu. Anauza Samueli kuti: ‘Mitundu yonse yotizungulila ili na mafumu. Na ise tifuna mfumu.’ Samueli anaona kuti kucita zimenezo kunali kulakwa, conco anapemphela kwa Yehova za nkhani imeneyi. Koma Yehova anamuuza kuti: ‘Sikuti anthu aŵa akana iwe, akana ine. Uŵauze kuti niwapatsa mfumu, koma adziŵe kuti mfumuyo idzafuna zambili kwa iwo.’ Koma anthuwo anaumililabe, amvekele: ‘Zilibe kanthu izo. Ise tifuna mfumu cabe!’

Ndiyeno Yehova anauza Samueli kuti Sauli ndiye adzakhala mfumu yoyamba. Pamene Sauli anapita kwa Samueli ku Rama, Samueli anamudzoza kukhala mfumu pomuthila mafuta pa mutu.

Pambuyo pake, Samueli anaitana Aisiraeli onse kuti aŵaonetse mfumu yawo. Koma Sauli sanapezeke. Udziŵa kumene anali? Anabisala pa vikatundu. Atamupeza anamubweletsa na kumuimika pakati pa anthu. Sauli anali wamtali kuposa onse, komanso wokongola kwambili. Ndiyeno Samueli anati: ‘Uyu ni amene Yehova wasankha kukhala mfumu yanu.’ Anthu anafuula kuti: ‘Moyo wautali kwa mfumu!’

Poyamba, Mfumu Sauli anali kumvela kwa Samueli na Yehova. Koma m’kupita kwa nthawi anasintha. Mwacitsanzo, mfumu siinali kufunika kupeleka nsembe. Pa nthawi ina, Samueli anauza Sauli kuti amuyembekezele, koma Samueli anacedwako. Conco, Sauli anapeleka nsembe iye mwini. Kodi Samueli anacita bwanji? Anamuuza kuti: ‘Sunafunikile kucimwila Yehova.’ Kodi Sauli anaphunzilapo kanthu pa colakwa cake?

Pa nthawi ina, Sauli atapita kukamenyana nkhondo ndi Aamaleki, Samueli anauza Sauli kuti asakasiyepo aliyense wamoyo. Koma Sauli sanaphe Mfumu Agagi. Yehova anauza Samueli kuti: ‘Sauli wanisiya ndipo waleka kunimvela.’ Samueli anamvela cisoni kwambili, ndipo anauza Sauli kuti: ‘Cifukwa cakuti sunamvelele Yehova, iye adzasankha mfumu ina.’ Samueli potembenuka kuti apite, Sauli anagwila covala ca Samueli, ndipo cinang’ambika. Pamenepo Samueli anauza Sauli kuti: ‘Yehova wang’amba ufumu kuucotsa kwa iwe.’ Yehova anafuna kupeleka ufumuwo kwa munthu amene angakonde Mulungu na kumvela malamulo ake.

“Kumvela kuposa nsembe.”—1 Samueli 15:22