Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 51

Kamtsikana Kathandiza Mkulu wa Asilikali

Kamtsikana Kathandiza Mkulu wa Asilikali

Ku Siriya kunali kamtsikana kaciisiraeli kamene kanatengedwa kukakhala kutali na kwawo. Kanatengedwa na asilikali acisiriya kuti kaziseŵenzela mkazi wa mkulu wa asilikali, dzina lake Namani. Kamtsikanaka kanali kulambila Yehova, olo kuti onse kumeneko sanali kulambila Yehova.

Namani anali kudwala matenda oipa akhate, ndipo anali kumvela kuŵaŵa kwambili. Kamtsikanako kanafuna kwambili kum’thandiza. Conco kanauza mkazi wa Namani kuti: ‘Nidziŵa amene angaŵacilitse amuna anu. Ku Isiraeli kuli mneneli wa Yehova dzina lake Elisa. Angaŵacilitse amuna anu.’

Mkazi wa Namani anauza mwamuna wake zimene kamtsikanako kanamuuza. Namani anali wokonzeka kucita ciliconse kuti acile. Conco, anapita ku Isiraeli ku nyumba ya Elisa. Koma iye anaganiza kuti Elisa adzamulandila mwapadela monga munthu wolemekezeka. Koma m’malo mokamba naye mwacindunji, Elisa anangouza mtumiki wake kuti apite akaonane na Namani, na kumuuza kuti: ‘Pita ukasambe maulendo 7 mu Mtsinje wa Yorodano, ndipo udzacila.’

Koma Namani anakwiya kwambili. Anati: ‘Ni nali kuganiza kuti mneneliyo adzanicilitsa mwapadela, mwa kuitanila kwa Mulungu wake poniika manja. Koma akuniuza kuti nikasambe mu mtsinje wa kuno ku Isiraeli. Tili na mitsinje yabwino ku Siriya kuposa twanu. Bwanji osangoniuza kuti nikasambe mu mtsinje wakwathu?’ Namani anakwiya kwambili, cakuti anacoka pa nyumba ya Elisa.

Koma atumiki a Namani anam’thandiza kuti aganizepo bwino. Iwo anati: ‘Kodi simungacite ciliconse kuti mucile? Zimene mneneliyu wakuuzani kucita si zovuta. Bwanji osangocita zimene wakamba?’ Namani anamvela. Conco, anapita ku Mtsinje wa Yorodano na kumila m’madzi maulendo 7. Pamene anavuuka ka namba 7, anapolelatu! Namani anakondwela kwambili, cakuti anapitanso kwa Elisa kuti akawonge zikomo. Iye anati: ‘Lomba nadziŵa kuti Yehova ndiye Mulungu woona.’ Uganiza kuti kamtsikana kaciisiraeli kanamvela bwanji, pamene kanaona kuti Namani wabwelako atacila?

“M’kamwa mwa ana ndi mwa ana oyamwa mwaikamo mawu otamanda.”—Mateyu 21:16