Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MUTU 8

Yehova Amafuna Anthu Ake Kukhala Oyela

Yehova Amafuna Anthu Ake Kukhala Oyela

“Kwa munthu wokhalabe woyela, mudzadzisonyeza kuti ndinu woyela.”—SALIMO 18:26.

1-3. (a) N’cifukwa ciani mayi amaonetsetsa kuti mwana wake akuoneka bwino? (b) Nanga Yehova amafunilanji anthu ake kukhala oyela?

YELEKEZANI mayi wacikondi amene akonzekeletsa kamwana kake kamnyamata kupita ku sukulu. Amaonetsetsa kuti mwanayo wasamba, ndipo zovala zake n’zoyela komanso zochisa bwino. Izi zimam’pangitsa kuoneka bwino, ndipo ena amaona kuti makolo ake amam’samalila bwino.

2 N’cimodzi-modzi Atate wathu Yehova. Amafuna kuti tizikhala oyela, opanda codetsa ciliconse. (Salimo 18:26) Iye amadziŵa kuti ukhondo uli na ubwino kwa ife. Ndipo tikakhala aukhondo timalemekeza Mulungu.—Ezekieli 36:22; ŵelengani 1 Petulo 2:12.

3 Kodi kukhala oyela kumatanthauza ciani? Ndipo n’cifukwa ciani kukhala woyela kuli na mapindu? Pamene tikambilana mafunso amenewa, aliyense angaone zimene ayenela kusintha mu umoyo wake.

N’CIFUKWA CIANI TIYENELA KUKHALA OYELA?

4, 5. (a) N’cifukwa ciani timafuna kukhala oyela? (b) Kodi cilengedwe cimationetsa bwanji kuti Yehova amafuna ciyelo?

4 Yehova ni citsanzo cabwino kwambili pa nkhani ya kukhala oyela. (Levitiko 11:44, 45) Conco, cifukwa cacikulu cofunila kukhala oyela n’cakuti tifuna ‘kutsanzila Mulungu,’ kapena kuti kutengela citsanzo cake.—Aefeso 5:1.

5 Cilengedwe ca Yehova cimationetsa mmene amaonela nkhani ya ciyelo. Iye anakonza zungulile-zungulile wacilengedwe kuti dziko lapansi likhale malo oyela okhalapo anthu. Mwacitsanzo, mvula ikagwa ndiyeno dzuŵa n’kutuluka, madzi amakamuka n’kukwela kumwamba monga nkhungu na kukapanga mitambo. Kenako imasungunuka n’kugwanso monga mvula. (Yeremiya 10:12) Komanso, Yehova m’nthaka anaikamo tudoyo tung’ono-tung’ono kwambili tumene sitingatuone na maso athu. Tumakwanitsa kusintha zinthu zapoizoni kukhala zinthu zabwino zothandiza. Ndipo ngakhale asayansi amatuseŵenzetsa kukonza zacilengedwe zimene zinawonongeka.—Aroma 1:20.

6, 7. Kodi Cilamulo ca Mose cinaonetsa bwanji kuti olambila Yehova afunika kukhala oyela?

6 Kufunika kwa ciyelo kumaonekelanso m’Cilamulo cimene Yehova anapatsa Aisiraeli kupitila mwa Mose. Mwacitsanzo, pokalambila Yehova, anthu anafunika kukhala oyela pathupi. Pa Tsiku Lophimba Macimo, mkulu wa ansembe anafunikila kusamba kaŵili m’thupi. (Levitiko 16:4, 23, 24) Ngakhalenso ansembe ena, kuti apeleke nsembe, anafunikila kusamba m’manja na kumapazi. (Ekisodo 30:17-21; 2 Mbiri 4:6) Ndipo nthawi zina, cilango cake wina akaphwanya malamulo a ciyelo, anali kuphedwa.—Levitiko 15:31; Numeri 19:17-20.

7 Nanga bwanji masiku ano? Tingaphunzile zambili m’Cilamulo pa za miyezo ya Yehova. (Malaki 3:6) Cilamulo cinaonetselatu kuti olambila Yehova afunika kukhala anthu oyela. Miyezo ya Yehova siinasinthe. Ngakhale masiku ano, amafunabe kuti alambili ake akhale oyela.—Yakobo 1:27.

KODI KUKHALA OYELA KUMATANTHAUZA CIANI?

8. Kodi tifunika kukhala oyela m’mbali ziti?

8 Kwa Yehova, kukhala oyela sikulekezela pa kuyeletsa matupi athu, zovala, na pakhomo cabe iyai. Kumakhudza umoyo wathu wonse. Kumaphatikizaponso kulambila kwathu, makhalidwe, na malingalilo athu. Inde, kuti tikhale oyela kwa Yehova, tiyenela kukhala oyela m’mbali zonse za umoyo wathu.

9, 10. Kodi kukhala oyela pa kulambila kwathu kutanthauza ciani?

9 Kulambila koyela. Sitifunika kukhala na mbali iliyonse m’kulambila konama. Pamene Aisiraeli anali andende ku Babulo, anali kukhala pakati pa anthu acipembedzo cacikunja ca makhalidwe oipa. Yesaya anakambilatu kuti Aisiraeli adzabwelela kwawo ku Isiraeli kukakhazikitsanso kulambila koyela. Ndipo Yehova anawauza kuti: “Tulukani mmenemo! Musakhudze cinthu ciliconse codetsedwa. Cokani pakati pake! Khalani oyela.” Sanafunikile kusakaniza kulambila kwawo Mulungu na ziphunzitso, makhalidwe, kapena miyambo ya cipembedzo conama ca ku Babulo.—Yesaya 52:11.

10 Ngakhale masiku ano, Akhristu oona amapewa zipembedzo zonama. (Ŵelengani 1 Akorinto 10:21.) Kuzungulila dziko lonse, miyambo yambili, zikhalidwe, na zikhulupililo, zimazikidwa pa ziphunzitso zonama. Mwacitsanzo, anthu ambili amakhulupilila kuti munthu akafa, mzimu umacoka m’thupi mwake kukakhala kwina. Ndipo pamakhala zocitika zambili zokhudzana na cikhulupililo cimeneci. (Mlaliki 9:5, 6, 10) Akhristu ayenela kupewa miyambo imeneyo. N’zoona kuti acibanja angatikakamize kuti ticiteko miyambo ina. Koma pofuna kukhalabe oyela kwa Yehova, sitigonja ku mayeselo amenewo.—Machitidwe 5:29.

11. Kodi kukhala oyela m’makhalidwe kumatanthauzanji?

11 Makhalidwe oyela. Kuti tikhale oyela kwa Yehova, tiyenela kupewa zaciwelewele za mtundu uliwonse. (Ŵelengani Aefeso 5:5.) M’Baibo, Yehova amatiuza kuti “thaŵani dama.” Amakamba mosapita m’mbali, kuti anthu ocita zaciwele-wele osalapa, “sadzaloŵa mu ufumu wa Mulungu.”—1 Akorinto 6:9, 10, 18; onani Mfundo ya Kumapeto 22.

12, 13. N’cifukwa ciani tiyenela kukhala oyela m’maganizo?

12 Maganizo oyela. Maganizo ndiwo amatitsogolela kucita zinthu. (Mateyu 5:28; 15:18, 19) Maganizo oyela amatithandiza kucita zinthu zoyela. N’zoona kuti ndise opanda ungwilo, ndipo nthawi zina maganizo oipa amatibwelela. Koma akabwela, tifunika kuwacotsa nthawi imeneyo. Tikaleka kuwacotsa, m’kupita kwa nthawi tidzapeza kuti mtima wathu si woyela. Tingayambe kufuna kucita zinthu zimene timakonda kukambapo. Koma kuti tipewe zimenezi, tifunikila kumadyetsa maganizo athu malingalilo abwino. (Ŵelengani Afilipi 4:8.) Conco, tifunika kupewa zinthu monga zosangalatsa zolaula, kapena zaciwawa. Tiyenela kusankha mosamala zimene tiŵelenga, kutamba, kapena kulankhula.—Salimo 19:8, 9.

13 Kuti tikhalebe m’cikondi ca Mulungu, tifunika kukhala oyela m’kalambilidwe kathu, makhalidwe, na m’maganizo. Koma Yehova amafunanso kuti tikhale oyela kuthupi.

KODI TINGAKHALE BWANJI OYELA KUTHUPI?

14. N’cifukwa ciani tiyenela kukhala oyela kuthupi?

14 Ngati matupi athu na malo athu akhala oyela, timapindula ife eni, komanso anthu okhala nafe pafupi. Timamvela bwino, ndipo anthu ena amakonda kukhala nafe. Koma pali cifukwa coposa cimeneci. Tikakhala oyela timalemekeza Yehova. Mwacitsanzo: Ngati muona mwana amene nthawi zonse amaoneka wadothi, mungaganize bwanji za makolo ake? Kuti samusamalila, si conco kodi? N’cimodzi-modzi na ife. Ngati sitizisamala kuti tizioneka bwino, anthu angamuganizile molakwika Yehova. Paulo anati: “Sitikucita ciliconse cokhumudwitsa, kuti utumiki wathu usapezedwe cifukwa. Koma tikusonyeza mwa njila ina iliyonse kuti ndife atumiki a Mulungu.”—2 Akorinto 6:3, 4.

Pokhala anthu a Yehova, tifunika kukhala oyela, kuphatikizapo malo athu

15, 16. Kodi tifunika kucita ciani kuti tizikhala oyela?

15 Thupi lathu na vovala vathu. Tifunika kukhala aukhondo nthawi zonse. Mwacitsanzo, tifunika kusamba m’thupi tsiku lililonse, ngati n’kotheka. Tifunika kusamba m’manja na sopo, maka-maka pofuna kuphika kapena kudya. Maka-makanso tikacoka ku toileti, kapena tikagwila cinthu cadothi. Kusamba m’manja kumaoneka monga si nkhani yaikulu, koma kumaletsa tudoyo twa matenda kufalikila. Conco kumapulumutsa miyoyo. Ngati tilibe toileti, tifunika kupezabe njila yotetezeka yotaila zonyansazo. Aisiraeli analibe matoileti. Conco, anali kufocela pansi zonyansa, kutali na manyumba a anthu, komanso kutali na madzi.—Deuteronomo 23:12, 13.

16 Zovala zathu, sikuti zicite kukhala zokongola, zodula, kapena za mu fashoni ya letesti, iyai. Cacikulu zizikhala zoyela, zowasha bwino. (Ŵelengani 1 Timoteyo 2:9, 10.) Tifuna kuti maonekedwe athu azilemekeza Yehova nthawi zonse.—Tito 2:10.

17. N’cifukwa ciani nyumba zathu na malo ozungulila afunika kukhala aukhondo?

17 Nyumba yathu na malo ozungulila. Zilibe kanthu kuti tikhala kuti, nyumba zathu zifunika kuoneka zaukhondo. Tifunika kuonetsetsanso kuti motoka yathu, honda, njinga, kapena coyendela ciliconse n’cosamalika bwino, maka-maka popita ku misonkhano na mu ulaliki. Ndipo m’pakedi, cifukwa tikakhala mu ulaliki, timauza anthu za umoyo wa m’dziko loyela la paradaiso. (Luka 23:43; Chivumbulutso 11:18) Maonekedwe a nyumba yathu na malo ozungulila angaonetse kuti tikukonzekela moyo wa m’dziko loyela latsopano.

18. N’cifukwa ciani timafuna malo athu olambilila kukhala oyela?

18 Malo athu olambilila. Timaonetsa kuti ukhondo ni wofunika kwa ife ngati malo athu olambilila amakhala aukhondo, kaya ni pa Nyumba ya Ufumu kapena malo ocitilako misonkhano ikulu-ikulu. Anthu akabwela pa Nyumba ya Ufumu koyamba, kambili amaona ukhondo umene umakhalapo. Izi zimalemekeza Yehova. Monga ziwalo za mpingo, timakhala na mwayi woyeletsa Nyumba yathu ya Ufumu na kukonza zowonongeka.—2 Mbiri 34:10.

KULEKA MACITIDWE ODETSA MUNTHU

19. Kodi tifunika kupewa ciani?

19 Olo kuti Baibo siicita kuchula mcitidwe uliwonse umene tiyenela kupewa, imapeleka mfundo zoonetsa kuti Yehova amadana nawo macitidwe amenewo. Iye safuna kuti tizikoka fodya, kumwa moŵa mwaucidakwa, kapena kumwa amkola bongo. Ngati tili mabwenzi a Mulungu, tiyenela kupewa macitidwe amenewa. Cifukwa ciani? Cifukwa timalemekeza moyo kwambili. Macitidwe amenewa amafupikitsa moyo, kuwononga thanzi, komanso kuvulaza anthu ena. Pofuna kukhala na thanzi labwino, anthu ambili amayesetsa kuti aleke macitidwe amenewa. Koma ife pokhala mabwenzi a Yehova, tili na cifukwa coposa pamenepo—timakonda Mulungu. Mzimayi wina wacicepeleko anati: “Yehova ananithandiza kuyeletsa moyo wanga, na kuleka kumwa zoledzeletsa. . . . Panekha, zinali zosatheka kusintha moyo wanga.” Tsopano, tiyeni tikambilane mfundo za m’Baibo zisanu zimene zingathandize wina kuleka macitidwe odetsa amenewa.

20, 21. Ni macitidwe ati amene Yehova amafuna kuti tiwasiye?

20 “Popeza talonjezedwa zinthu zimenezi, tiyeni tidziyeletse ndipo ticotse cinthu ciliconse coipitsa thupi kapena mzimu, kwinaku tikukwanilitsa kukhala oyela poopa Mulungu.” (2 Akorinto 7:1) Yehova amafuna kuti timasuke ku macitidwe amene angawononge maganizo olo thupi lathu.

21 Cifukwa camphamvu cotipangitsa kuti “tidziyeletse ndipo ticotse cinthu ciliconse coipitsa thupi,” cili pa 2 Akorinto 6:17, 18. Pamenepo Yehova akutiuza kuti: “Musakhudze cinthu codetsedwa.” Kenako akulonjeza kuti: “Ndidzakhala atate wanu, ndipo inu mudzakhala ana anga aamuna ndi aakazi.” Inde, ngati timapewa ciliconse cimene cingatidetse kwa Yehova, iye adzatikonda monga mmene tate amakondela ana ake.

22-25. Ni mfundo za m’Malemba ziti zingatithandize kupewa macitidwe oipa?

22 “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.” (Mateyu 22:37) Iyi ndiye lamulo yaikulu kuposa onse. (Mateyu 22:38) Yehova amafuna tizim’konda na mtima wathu wonse. Kodi zimenezi zingatheke bwanji ngati timacita zinthu zimene zingafupikitse moyo wathu, kapena kuwononga ubongo wathu? M’malo mwake, timacita zonse zotheka kuti tilemekeze moyo umene iye anatipatsa.

23 “[Yehova] amene amapatsa anthu onse moyo, mpweya, ndi zinthu zonse.” (Machitidwe 17:24, 25) Kodi mnzanu akakupatsani mphatso yapadela, mungaitaye kapena kuiwononga? Moyo nawonso ni mphatso yodabwitsa yocokela kwa Yehova. Ndipo timaiyamikila kwambili. Conco, timafuna kuseŵenzetsa moyo wathu kulemekeza Mulungu.—Salimo 36:9.

24 “Uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha.” (Mateyu 22:39) Macitidwe oipa savulaza ife cabe. Amavulazanso amene ali nafe pafupi, anthu amene timawakonda kwambili. Mwacitsanzo, munthu wokhala m’nyumba imodzi na munthu wokoka fodya, angadwale matenda oopsa, cabe cifukwa copumako utsi wa fodya. Koma tikaleka macitidwe ngati amenewa, timaonetsa kuti timakonda anthu amene tikhala nawo.—1 Yohane 4:20, 21.

25 “Pitiliza kuwakumbutsa kuti azigonjela ndi kumvela maboma ndiponso olamulila.” (Tito 3:1) M’maiko ambili, ni mlandu kumwa kapena kukoka amkola bongo, ngakhale kupezeka nawo cabe. Popeza Yehova amatilamula kuti tizilemekeza maboma, tiyenela kumvela malamulo amenewo.—Aroma 13:1.

Tikakhala oyela ndi aukhondo, timalemekeza Yehova

26. (a) Kodi cofunikila n’ciani kuti kulambila kwathu kukhale kolandilika kwa Yehova? (b) N’cifukwa ciani kukhala oyela kwa Mulungu ndiwo umoyo wabwino koposa?

26 Ngati tifuna kukhala bwenzi la Yehova, tiyenela kusintha zinthu zina mu umoyo wathu. Ndipo tifunika kuyambapo pali pano. N’zoona kuti zingakhale zovuta kusintha cinthu cimene unazoloŵela, koma tingakwanitse! Ndipo Yehova akulonjeza kutithandiza. Akutiuza kuti: “Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendeleni bwino, amene ndimakucititsani kuti muyende m’njila imene muyenela kuyendamo.” (Yesaya 48:17) Ngati tiyesetsa kukhala oyela, tidziŵe kuti timalemekeza Mulungu.